Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 66:1-12

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo.

66 Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!
    Imbani ulemerero wa dzina lake;
    kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.
Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!
    Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri
    kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.
Dziko lonse lapansi limaweramira inu;
    limayimba matamando kwa Inu;
    limayimba matamando pa dzina lanu.”
            Sela.

Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,
    ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.
Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma,
    iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi.
    Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.
Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya,
    maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina.
    Anthu owukira asadzitukumule.

Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,
    mulole kuti mawu a matamando ake amveke;
Iye watchinjiriza miyoyo yathu
    ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.
10 Pakuti Inu Mulungu munatiyesa;
    munatiyenga ngati siliva.
11 Inu mwatilowetsa mʼndende
    ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.
12 Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu;
    ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi,
    koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.

Yeremiya 27

Yuda Adzatumikira Nebukadinezara

27 Zedekiya mwana wa Yosiya, mfumu ya ku Yuda, atangoyamba kulamulira, Yehova anawuza Yeremiya kuti, “Tenga zingwe zomangira ndi mitengo ya goli ndipo uzimangirire mʼkhosi mwako. Tsono utumize uthenga kwa mafumu a Edomu, Mowabu, Amoni, Turo ndi Sidoni kudzera mwa amithenga amene abwera ku Yerusalemu kwa Zedekiya, mfumu ya Yuda. Uwapatse uthenga wokapereka kwa ambuye awo ndipo uwawuze kuti: Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, ‘Mukawuze ambuye anu kuti: Ndi mphamvu zanga ndi dzanja langa lamphamvu ndinalenga dziko lapansi ndi anthu ake onse pamodzi ndi nyama zili mʼmenemo, ndipo ndimalipereka kwa aliyense amene ndikufuna. Tsopano ndidzapereka mayiko anu onse kwa mtumiki wanga Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni. Ndamupatsanso nyama zakuthengo zonse kuti zimutumikire. Anthu a mitundu yonse adzamutumikira iyeyo, mwana wake ndi chidzukulu chake mpaka nthawi itakwana yoti dziko lake liwonongedwe. Pamenepo mitundu yambiri ndi mafumu amphamvu adzamugonjetsa.

“ ‘Koma ngati anthu a mtundu wina uliwonse kapena ufumu wina uliwonse adzakana kutumikira Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni kapena kusenza goli lake, Ine ndidzalanga mtundu umenewo ndi lupanga, ndi njala ndi mliri, akutero Yehova, mpaka nditawapereka mʼmanja mwake kotheratu. Choncho musamvere aneneri anu, owombeza anu, otanthauza maloto anu, amawula anu kapena amatsenga anu akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni.’ 10 Iwo akukuloserani zabodza kotero kuti adani adzakuchotsani mʼdziko lanu nʼkupita nanu ku dziko lakutali. Ndidzakupirikitsani ndi kukuwonongani kotheratu. 11 Koma ngati mtundu wina uliwonse udzagonjera mfumu ya ku Babuloni ndi kuyitumukira, ndidzawusiya kuti ukhale mʼdziko lake kuti uzilima ndi kukhalamo, akutero Yehova.’ ”

12 Uthenga womwewu ndinawuzanso Hezekiya mfumu ya Yuda. Ndinati, “Gonjerani mfumu ya ku Babuloni. Itumikireni iyoyo pamodzi ndi anthu ake ndipo mudzakhala ndi moyo. 13 Nanga inu ndi anthu anu, muferenji ndi lupanga, ndi njala, ndi mliri, zimene Yehova waopsezera mtundu wina uliwonse umene sudzatumikira mfumu ya ku Babuloni? 14 Musamvere mawu a aneneri akamakuwuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya ku Babuloni,’ chifukwa zimene akukuloseranizo nʼzabodza. 15 Sindinawatume ngakhale iwo akulosera mʼdzina langa. Nʼchifukwa chake, ndidzakupirikitsani ndipo mudzawonongeka kotheratu, inu pamodzi ndi aneneri amene akunenera zabodza kwa inu.”

16 Kenaka ndinawuza ansembe pamodzi ndi anthu ena onse kuti, “Yehova akuti: Musamvere aneneri amene akumanena kuti, ‘Posachedwapa ziwiya za mʼNyumba ya Yehova zibwera kuchokera ku Babuloni.’ Iwowo akunenera zabodza kwa inu. 17 Musawamvere. Tumikirani mfumu ya ku Babuloni, ndipo mudzakhala ndi moyo. Mzindawu usandukirenji bwinja? 18 Ngati iwo ndi aneneri ndipo ali ndi mawu a Yehova, apempheretu kwa Yehova Wamphamvuzonse kuti ziwiya zimene zatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndiponso mu Yerusalemu zisatengedwe kupita ku Babuloni. 19 Pakuti Yehova akunena za zipilala, za mbiya ya madzi, maphaka ndi ziwiya zina zimene zatsala mu Yerusalemu. 20 Izi ndi zimene Nebukadinezara mfumu ya ku Babuloni sanatenge pamene anatenga ukapolo Yekoniya mwana wa Yehoyakimu mfumu ya Yuda kupita ku Babuloni kuchokera ku Yerusalemu, pamodzi ndi anthu olemekezeka a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. 21 Inde, Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, akunena za zinthu zimene zinatsala mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba ya mfumu ya Yuda ndi mu Yerusalemu kuti, 22 ‘Zidzatengedwa kupita ku Babuloni ndipo zidzakhala kumeneko mpaka tsiku limene ndidzawakumbukirenso,’ akutero Yehova. ‘Pamenepo ndidzazitenganso ndi kuzibwezanso ku malo ano.’ ”

2 Timoteyo 2:1-7

Tsono iwe, mwana wanga, limbika mʼchisomo chimene chili mwa Khristu Yesu. Ndipo zinthu zimene unamva ine ndikuziyankhula pamaso pa mboni zambiri, uziphunzitse kwa anthu odalirika amene akaphunzitsenso ena. Umve nane zowawa, monga msilikali wa Khristu Yesu. Palibe msilikali amene ali pa ntchito amagwiranso ntchito za anthu wamba, iye amafuna kukondweretsa bwana wolamulira. Chimodzimodzinso, munthu amene ali pa mpikisano waliwiro, salandira mphotho ya wopambana pokhapokha atatsiriza monga mwa malamulo a mpikisanowo. Mlimi wolimbika ndi amene amayembekezereka kukhala woyambirira kulandira gawo la zokolola. Lingalira zimene ndikunenazi, pakuti Ambuye adzakuzindikiritsa zonsezi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.