Read the New Testament in 24 Weeks
Babuloni Wagwa, Haleluya!
19 Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti,
“Haleluya!
Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,
2 pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo.
Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja
amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake.
Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”
3 Ndipo anafuwulanso kuti,
“Haleluya!
Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”
4 Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti,
“Ameni, Haleluya!”
5 Kenaka mawu anachoka ku mpando waufumu kuti,
“Lemekezani Mulungu wathu
inu nonse atumiki ake,
inu amene mumamuopa,
nonse angʼono ndi akulu!”
6 Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati,
“Haleluya!
Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira.
7 Tiyeni tisangalale ndi kukondwera
ndi kumutamanda!
Pakuti nthawi ya ukwati wa Mwana Wankhosa yafika,
ndipo Mkwatibwi wakonzekeratu.
8 Wapatsidwa nsalu yoyera kwambiri, yowala ndi yosada
kuti avale.”
(Nsalu yoyera kwambiri ikuyimira ntchito zolungama za oyera mtima).
9 Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”
10 Pamenepo ndinadzigwetsa pa mapazi ake kumupembedza. Koma anandiwuza kuti, “Usatero ayi, ine ndine mtumiki mnzako ngati iwe yemwe, ndiponso ngati abale ako amene asunga umboni wa Yesu. Pembedza Mulungu. Pakuti umboni wa Yesu ndiye mzimu wa uneneri.”
Wokwera pa Kavalo Woyera
11 Ndinaona kumwamba kutatsekuka ndipo patsogolo panga panali kavalo woyera, amene anakwerapo dzina lake linali Wokhulupirika ndiponso Woona. Poweruza ndi kuchita nkhondo, amachita molungama. 12 Maso ake anali ngati malawi amoto, ndipo pamutu pake panali zipewa zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lodziwika ndi Iye yekha, osati wina aliyense. 13 Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu. 14 Magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera pa akavalo oyera, ndipo iwowo atavala nsalu zoyera kwambiri ndi zosada. 15 Mʼkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa limene anati akaphe nalo mitundu ya anthu. Iye adzalamulira ndi ndodo yachitsulo. Iye anaponda choponderamo mphesa cha ukali wa Mulungu Wamphamvuzonse. 16 Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili:
MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE.
17 Ndipo ndinaona mngelo atayimirira pa dzuwa amene anafuwula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zowuluka mlengalenga kuti, “Bwerani, sonkhanani pamodzi ku phwando lalikulu la Mulungu. 18 Kuti mudye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, ndi wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi okwerapo awo, ndi wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, angʼono ndi aakulu.”
19 Kenaka ndinaona chirombo chija ndi mafumu a dziko lapansi ndi magulu ankhondo atasonkhana pamodzi kuti achite nkhondo ndi wokwera pa kavalo ndi ankhondo ake. 20 Koma chirombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonyenga uja amene anachita zizindikiro zodabwitsa pamaso pake. Ndi zizindikirozi anasocheretsa amene analembedwa chizindikiro cha chirombocho napembedza fano lake. Onse awiri anaponyedwa amoyo mʼnyanja yamoto yasulufule wotentha. 21 Ena onse anaphedwa ndi lupanga lija linatuluka mʼkamwa mwa wokwera pa kavalo uja, ndipo mbalame zonse zinadya mokwanira mnofu wa anthu akufawo.
Zaka 1,000
20 Ndipo ndinaona mngelo akutsika kuchokera kumwamba ali ndi kiyi ya ku chidzenje chakuya chija atanyamula mʼdzanja lake unyolo waukulu. 2 Iye anachigwira chinjokacho, chinjoka chakalekale chija, amene ndi Mdierekezi kapena kuti Satana, ndipo anamumanga zaka 1,000. 3 Anamuponya ku chidzenje chakuya chija namutsekera ndi kiyi ndi kumatirira pa khomopo kuti asatulukenso kukanyenga mitundu ya anthu mpaka patapita zaka 1,000. Zikadzatha zakazo, adzamumasula kwa kanthawi pangʼono chabe.
4 Ndinaona mipando yaufumu pamene anakhalapo anthu amene anapatsidwa mphamvu zoweruza. Ndipo ndinaona mizimu ya amene anadulidwa makosi chifukwa cha umboni wa Yesu ndi chifukwa cha Mawu a Mulungu. Iwo sanapembedze nawo chirombo kapena fano lake ndipo sanalembedwe chizindikiro chake pa mphumi zawo kapena pa manja awo. Iwo anakhalanso ndi moyo nalamulira pamodzi ndi Khristu zaka 1,000. 5 (Akufa ena onse sanaukenso mpaka zitatha zaka 1,000). Uku ndiko kuuka kwa akufa koyamba. 6 Odala ndi oyera mtima amene adzaukitsidwa nawo pa kuukitsidwa koyamba. Imfa yachiwiri ilibe mphamvu pa iwo koma adzakhala ansembe a Mulungu ndi a Khristu ndipo adzalamulira naye pamodzi zaka 1,000.
Kugonjetsedwa kwa Satana
7 Zaka 1,000 zikadzatha, Satana adzamasulidwa ku ndende yake 8 ndipo adzapita kukanyenga mitundu ya anthu kumbali zonse zinayi za dziko lapansi, Gogi ndi Magogi, kuwasonkhanitsa kuti akachite nkhondo. Kuchuluka kwawo kudzakhala ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja. 9 Iwo anayenda ponseponse pa dziko lapansi nazinga msasa wa anthu a Mulungu, mzinda umene Iye amawukonda. Koma moto unatsika kuchokera kumwamba ndi kuwanyeketsa. 10 Ndipo Mdierekezi amene anawanyenga, anaponyedwa mʼnyanja ya sulufule wotentha, kumene kunaponyedwa chirombo chija ndi mneneri wonama uja. Iwo adzazunzika usiku ndi usana kwamuyaya.
Chiweruzo Chotsiriza
11 Kenaka ndinaona Mpando Waufumu waukulu woyera ndi Iye amene anakhalapo. Dziko lapansi ndi kumwamba zinathawa pamaso pake ndipo panalibenso malo awo. 12 Ndipo ndinaona akufa, aakulu ndi aangʼono omwe atayimirira patsogolo pa Mpando Waufumu ndipo mabuku anatsekulidwa. Buku lina linatsekulidwa limene linali Buku Lamoyo. Akufa anaweruzidwa monga mwa zimene anachita monga mmene zinalembedwera mʼmabuku. 13 Nyanja inapereka amene anaferamo ndipo imfa ndi Hade zinapereka akufa ake ndipo munthu aliyense anaweruzidwa monga mwa ntchito zake. 14 Kenaka imfa ndi Hade zinaponyedwa mʼnyanja ya moto. Nyanja yamoto ndiyo imfa yachiwiri. 15 Ngati dzina la wina aliyense silinapezeke mʼBuku Lamoyo, anaponyedwa mʼnyanja yamoto.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.