Read the New Testament in 24 Weeks
1 Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu mwachifuniro cha Mulungu, ndi Timoteyo mʼbale wathu.
2 Kulembera abale oyera mtima ndi okhulupirira a ku Kolose mwa Khristu.
Chisomo ndi mtendere kwa inu zochokera kwa Mulungu Atate athu.
Kuyamika ndi Pemphero
3 Timayamika Mulungu Atate wa Ambuye athu Yesu Khristu, nthawi zonse pamene tikukupemphererani. 4 Timayamika chifukwa tinamva za chikhulupiriro chanu mwa Khristu Yesu ndi za chikondi chanu pa oyera mtima onse. 5 Chikhulupiriro ndi chikondi, gwero lake ndi chiyembekezo chomwe muli nacho chodzalandira zimene anakusungirani kumwamba. Munamva kale za zimenezi kudzera mʼmawu a choonadi, Uthenga Wabwino 6 umene unafika kwa inu. Pa dziko lonse lapansi Uthenga Wabwino ukubereka chipatso ndi kukula monga momwe zakhala zikuchitikira pakati panu kuyambira tsiku limene munawumva ndi kuzindikira chisomo cha Mulungu mu choonadi chonse. 7 Inu munaphunzira zimenezi kuchokera kwa Epafra, mtumiki mnzathu wokondedwa, amene ndi mtumiki wokhulupirika wa Khristu mʼmalo mwathu. 8 Iye anatiwuza za chikondi chanu chimene Mzimu anakupatsani.
9 Chifukwa cha ichi, kuyambira tsiku limene tinamva za inu, sitinasiye kukupemphererani ndi kumupempha Mulungu kuti akudzazeni ndi chidziwitso cha chifuniro chake kudzera mu nzeru yonse yauzimu ndi kumvetsetsa. 10 Ndipo tikupempherera zimenezi ndi cholinga chakuti inu mukhale moyo oyenera Ambuye ndi kumukondweretsa mʼnjira zonse. Kubereka chipatso pa ntchito iliyonse yabwino, ndi kukula mʼchidziwitso cha Mulungu. 11 Timapempheranso kuti Mulungu akulimbikitseni ndi mphamvu yake yonse ya ulemerero wake, kuti muzipirira zonse ndi mitima yofatsa ndi ya chimwemwe 12 ndi kuyamika Atate nthawi zonse, amene wakuyenerezani kuti mulandire nawo chuma cha oyera mtima mu ufumu wa kuwunika. 13 Pakuti Iye anatipulumutsa ku ulamuliro wa mdima ndi kutibweretsa mu ufumu wa Mwana wake wokondedwa. 14 Mwa Iyeyu ife tinawomboledwa ndi kukhululukidwa machimo.
Kupambana Koposa kwa Khristu
15 Mwanayu ndiye chithunzi cha Mulungu wosaonekayo. Iye ndiye Mwana wake woyamba kubadwa ndi wolamulira zolengedwa zonse. 16 Pakuti zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye. Zinthu zakumwamba ndi za pa dziko lapansi, zooneka ndi zosaoneka, maufumu, akuluakulu, aulamuliro ndi amphamvu. Zinthu zonse zinalengedwa kudzera mwa Iye ndipo anazilengera Iyeyo. 17 Iyeyo analipo zinthu zonse zisanalengedwe ndipo zinthu zonse zimamangika pamodzi mwa Iye. 18 Iye ndiyenso mutu wa thupi, limene ndi mpingo. Iye ndiye chiyambi chake, woyamba kuuka kwa akufa, kuti Iyeyo akhale wopambana zonse. 19 Pakuti kunamukomera Mulungu kuti umulungu wake wonse ukhalemo mwa Khristu. 20 Ndipo kudzera mwa Iye Mulungu ayanjanitsenso zinthu zonse ndi Iye mwini, zinthu za pa dziko lapansi, kapena zinthu za kumwamba. Iye anachita mtendere kudzera mʼmagazi ake, wokhetsedwa pa mtanda.
21 Kale inu munali kutali ndi Mulungu ndipo munali adani a Mulungu mʼmaganizo mwanu chifukwa cha khalidwe lanu loyipa. 22 Koma tsopano Iye anakuyanjanitsani mʼthupi la Khristu kudzera mu imfa kuti akuperekeni pamaso pake oyera, opanda banga ndi opanda chotsutsidwa nacho 23 ngati mupitirirabe kukhala mʼchikhulupiriro chanu, okhazikika ndi olimba, osasunthidwa kuchoka pa chiyembekezo chimene munachigwira mu Uthenga Wabwino. Uwu ndi Uthenga Wabwino umene munawumva, umene wakhala ukulalikidwa kwa olengedwa onse a pansi pa thambo, ndi umenenso, ine Paulo ndinakhala mtumiki wake.
Utumiki wa Paulo ku Mpingo
24 Tsopano ine ndikukondwa kuti ndinavutika chifukwa cha inu, ndipo ndikukwaniritsa mʼthupi langa zimene zikuperewera pa masautso a Khristu, chifukwa cha thupi lake, limene ndi Mpingo. 25 Ine ndakhala mtumiki wake mwa lamulo limene Mulungu anandipatsa kuti ndipereke Mawu a Mulungu athunthu, 26 chinsinsi chimene chakhala chikubisika kwa nthawi ndi mibado, koma tsopano chawululidwa kwa oyera mtima. 27 Kwa iwo amene Mulungu anawasankha kuti awadziwitse pakati pa a mitundu ina, ulemerero wa chuma cha chinsinsi ichi, amene ndi Khristu mwa inu, chiyembekezo cha ulemerero.
28 Ife tikulalikira Khristu, kulangiza ndi kuphunzitsa aliyense mwa nzeru zonse kuti timupereke aliyense wangwiro mwa Khristu. 29 Ndi cholinga chimenechi, ine ndikugwira ntchito molimbika ndi mwamphamvu zonse zimene Iye anachita mwa ine.
2 Ndikufuna mudziwe kuti ndikukuvutikirani kwambiri, inuyo pamodzi ndi anzanu a ku Laodikaya, ndi ena onse amene sitinaonane maso ndi maso. 2 Cholinga changa nʼchakuti alimbikitsidwe ndi kuyanjana pamodzi mʼchikondi, akhale odzaza ndi nzeru zomvetsa zinthu, ndi kuti azindikire chinsinsi cha Mulungu, chimene ndi Khristu. 3 Mwa Iyeyu muli chuma chonse chobisidwa cha nzeru ndi chidziwitso. 4 Ndikukuwuzani zimenezi kuti wina aliyense asakunamizeni ndi kukukopani ndi mawu ake. 5 Pakuti ngakhale sindili pakati panu mʼthupi, ndili nanu pamodzi mu mzimu, ndipo ndikukondwa kuona kuti mukulongosola bwino zonse ndiponso kuti chikhulupiriro chanu mwa Khristu ndi chokhazikika ndithu.
Za Moyo Weniweni mwa Khristu
6 Tsono popeza munavomereza Khristu Yesu kukhala Ambuye anu, mupitirire kukhala mwa Iyeyo. 7 Mukhale ozikika mizu mwa Iye, ndipo moyo wanu umangike pa Iye. Mulimbike mʼchikhulupiriro monga momwe munaphunzirira, ndipo kuyamika kwanu kusefukire.
8 Musalole kuti wina aliyense akutengeni ukapolo ndi mʼnzeru zachinyengo zolongosola zinthu zozama, zomwe zimachokera ku miyambo ya anthu ndi ku maganizo awo okhudza za dziko lapansi osati kwa Khristu.
9 Pakuti mʼthupi la Khristu mumakhala umulungu wonse wathunthu. 10 Ndipo inunso ndinu athunthu mwa Khristu. Iye ndiye mtsogoleri wa pamwamba pa maufumu onse ndi maulamuliro wonse. 11 Mwa Iye inunso munachita mdulidwe mʼthupi lanu, osati mdulidwe ochitidwa ndi manja a anthu ayi, koma ochitidwa ndi Khristu pamene anavula khalidwe lanu lauchimo lija. 12 Mu ubatizo, munayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Khristu ndi kuukitsidwa naye pamodzi, pokhulupirira mphamvu za Mulungu amene anamuukitsa kwa akufa.
13 Pamene munali akufa chifukwa cha machimo anu ndi osachita mdulidwe mʼmitima mwanu, Mulungu anakupatsani moyo mwa Khristu. Iye anatikhululukira machimo athu onse. 14 Anafafaniza kalata ya ngongole yathu, pomwe panali milandu yotitsutsa ife. Iye anayichotsa, nayikhomera pa mtanda. 15 Ndipo atalanda zida maufumu ndi maulamuliro, Iye anawachititsa manyazi powayendetsa pamaso pa anthu onse atawagonjetsa ndi mtanda.
Ufulu Wathu
16 Nʼchifukwa chake musalole wina aliyense kukuzengani mlandu chifukwa cha zimene mumadya kapena kumwa, kapena za masiku achikondwerero cha chipembedzo, za chikondwerero cha mwezi watsopano, kapena za tsiku la Sabata. 17 Zimenezi ndi chithunzithunzi chabe cha zinthu zimene zikubwera, koma choonadi chenicheni chikupezeka mwa Khristu. 18 Musalole kuti wina aliyense amene amakonda kudzichepetsa mwachiphamaso ndi kumapembedza angelo akulepheretseni kukalandira mphotho. Munthu woteroyu amayankhulanso mwatsatanetsatane zinthu zimene akuti anaziona mʼmasomphenya. Anthuwa ndi odzitukumula ndi fundo zopanda pake zochokera mʼmaganizo mwawo amene si auzimu. 19 Iwo sakulumikizananso ndi mutu, kumene kumachokera thupi lonse, logwirizidwa ndi kumangiriridwa pamodzi ndi mʼmitsempha yake ndi mnofu, limene limakula monga mmene Mulungu afunira kuti likulire.
20 Popeza munafa pamodzi ndi Khristu kusiyana nayo miyambo ya dziko lapansi lino, nʼchifukwa chiyani mukukhalanso ngati a dziko lapansi lino? Bwanji mukumvera malamulo monga awa: 21 “Usagwire chakuti,” “Usalawe chakuti,” “Usakhudze chakuti?” 22 Malamulo amenewa amakhudza zinthu zimene zimatha zikamagwiritsidwa ntchito, ndipo malamulo ndi zophunzitsa za anthu chabe. 23 Ndithu malamulo oterewa amaoneka ngati anzeru, pakuti amalamulira anthu ambiri pa zachipembedzo ndi pa zakudzichepetsa kwa chiphamaso, ndi pa zakuzunza thupi lawo, koma alibe mphamvu zoletsa kuchita zofuna za thupilo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.