Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Machitidwe a Atumwi 19:1-20

Paulo ku Efeso

19 Apolo ali ku Korinto, Paulo anadutsa mʼmayiko a ku mtunda ndipo anafika ku Efeso. Kumeneko anapeza ophunzira ena. Iye anawafunsa kuti, “Kodi munalandira Mzimu Woyera pamene munakhulupirira?”

Iwo anayankha kuti, “Ayi, ife sitinamvepo kuti kuli Mzimu Woyera.”

Tsono Paulo anawafunsa kuti, “Nanga munabatizidwa ndi ubatizo wotani?”

Iwo anati, “Ubatizo wa Yohane.”

Paulo anati, “Ubatizo wa Yohane unali wa kutembenuka mtima. Iye anawuza anthu kuti akhulupirire amene amabwera, ameneyo ndiye Yesu.” Atamva zimenezi, anabatizidwa mʼdzina la Ambuye Yesu. Pamene Paulo anawasanjika manja, Mzimu Woyera anadza pa iwo ndipo anayankhula mʼmalilime ndipo ananenera. Anthu onsewo analipo khumi ndi awiri.

Paulo analowa mʼsunagoge ndipo anayankhula molimba mtima kwa miyezi itatu, kuwatsutsa mowakopa za ufumu wa Mulungu. Koma ena anawumitsa mitima; anakana kukhulupirira ndipo ananyoza Njirayo pa gulu la anthu. Kotero Paulo anawasiya. Iye anatenga ophunzirawo ndipo amakambirana tsiku ndi tsiku mʼsukulu ya Turano. 10 Izi zinachitika kwa zaka ziwiri, kotero kuti Ayuda onse ndi Agriki amene amakhala ku Asiya anamva Mawu a Ambuye.

11 Mulungu anachita zodabwitsa zapadera kudzera mwa Paulo. 12 Kotero kuti mipango yopukutira thukuta ndi yovala pogwira ntchito, zomwe zinakhudza thupi la Paulo amapita nazo kwa odwala ndipo amachiritsidwa ndiponso mizimu yoyipa mwa iwo imatuluka.

Za Ana a Skeva

13 Ayuda ena amene ankayendayenda kutulutsa mizimu yoyipa anayesa kugwiritsa ntchito dzina la Ambuye Yesu pa amene anali ndi ziwanda. Iwo popemphera amati, “Ine ndikulamulira utuluke, mʼdzina la Yesu amene Paulo amamulalikira.” 14 Amene ankachita zimenezi anali ana asanu ndi awiri a Skeva, mkulu wa ansembe wa Chiyuda. 15 Tsiku lina mzimu woyipa unawayankha kuti, “Yesu ndimamudziwa ndiponso Paulo ndimamudziwa, nanga inu ndinu ndani?” 16 Pamenepo munthu amene anali ndi mzimu woyipa anawalumphira nawagwira onse. Iye anawamenya kwambiri, kotero kuti anathawa mʼnyumbamo ali maliseche, akutuluka magazi.

17 Ayuda ndi Agriki okhala ku Efeso atamva zimenezi, anachita mantha, ndipo anthu anachitira ulemu dzina la Ambuye Yesu koposa. 18 Ambiri a iwo amene tsopano anakhulupirira anafika ndi kuvomereza poyera ntchito zawo zoyipa. 19 Ambiri amene amachita za matsenga anasonkhanitsa mabuku awo pamodzi nawatentha pamaso pa anthu onse. Atawonkhetsa mtengo wa mabukuwo, unakwanira ndalama zasiliva 50,000. 20 Kotero Mawu a Ambuye anapitirira kufalikira ndipo anagwira ntchito mwamphamvu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.