New Testament in a Year
Timoteyo Atsagana ndi Paulo ndi Sila
16 Paulo anafika ku Derbe ndi Lusitra, kumene kumakhala ophunzira wina dzina lake Timoteyo. Amayi ake anali Myuda wokhulupirira, koma abambo ake anali Mgriki. 2 Abale a ku Lusitra ndi Ikoniya anamuchitira iye umboni wabwino. 3 Paulo anafuna kumutenga pa ulendo, kotero anachita mdulidwe chifukwa cha Ayuda amene amakhala mʼderalo pakuti onse amadziwa kuti abambo ake anali Mgriki. 4 Pamene amayenda mzinda ndi mzinda, amafotokoza zimene atumwi ndi akulu ampingo ku Yerusalemu anagwirizana kuti anthu azitsatire. 5 Kotero mipingo inalimbikitsidwa mʼchikhulupiriro ndipo anthu amachulukirachulukirabe tsiku ndi tsiku.
Paulo Awona Masomphenya
6 Paulo ndi anzake anadutsa mayiko a Frugiya ndi Galatiya, Mzimu Woyera atawaletsa kulalikira Mawu a Mulungu ku Asiya. 7 Atafika ku malire a Musiya, anayesa kulowa ku Bituniya, koma Mzimu wa Yesu sunawalole kutero. 8 Ndipo iwo anadutsa Musiya ndipo anapita ku Trowa. 9 Nthawi ya usiku Paulo anaona masomphenya, munthu wa ku Makedoniya atayimirira ndi kumupempha kuti, “Bwerani ku Makedoniya, mudzatithandize.” 10 Paulo ataona masomphenyawa, tinakonzeka kupita ku Makedoniya, kutsimikiza kuti Mulungu anatiyitana kuti tikalalikire Uthenga Wabwino.
Lidia Atembenuka Mtima ku Filipi
11 Kuchokera ku Trowa tinakwera sitima ya pamadzi kupita ku Samotrake ndipo mmawa mwake tinapitirira mpaka ku Neapoli. 12 Kuchokera kumeneko tinapita ku Filipi, boma la Aroma ndiponso mzinda waukulu wa dera la Makedoniya. Tinakhala kumeneko masiku owerengeka.
13 Pa tsiku la Sabata tinatuluka mu mzindawo kupita ku mtsinje kumene timayembekezera kukapeza malo opempherera. Tinakhala pansi ndipo tinayamba kuyankhula ndi amayi amene anasonkhana pamenepo. 14 Mmodzi wa amayi amene amamvetserawo ndi Lidiya amene amagulitsa nsalu zofiira, wochokera ku mzinda wa Tiyatira, ndipo amapembedza Mulungu. Ambuye anatsekula mtima wake kuti amve mawu a Paulo. 15 Iye ndi a mʼbanja lake atabatizidwa, anatiyitana kuti tipite ku nyumba yake. Iye anati, “Ngati mwanditenga ine kukhala wokhulupirira mwa Ambuye, bwerani mudzakhale mʼnyumba mwanga.” Ndipo anatiwumiriza ife kwambiri.
Paulo ndi Sila Mʼndende
16 Tsiku lina pamene timapita kumalo wopempherera, tinakumana ndi mtsikana wina amene anali ndi mzimu woyipa umene umanena zamʼtsogolo. Iye amapezera ndalama zambiri ambuye ake pa ulosi wake. 17 Mtsikanayu anatsatira Paulo ndi ife, akufuwula kuti, “Anthu awa ndi atumiki a Mulungu Wammwambamwamba, amene akukuwuzani inu njira yachipulumutso.” 18 Iye anachita izi masiku ambiri. Kenaka Paulo anavutika mu mtima, natembenuka ndipo anati kwa mzimuwo, “Ndikukulamula iwe mʼdzina la Yesu Khristu kuti utuluke mwa iye!” Nthawi yomweyo mzimuwo unatuluka.
19 Pamene ambuye a mtsikana uja anazindikira kuti chiyembekezo chawo chopezera ndalama chatha, anagwira Paulo ndi Sila nawakokera ku bwalo la akulu. 20 Anawabweretsa iwo kwa oweruza milandu ndipo anati, “Anthu awa ndi Ayuda, iwo akuvutitsa mu mzinda wathu. 21 Ndipo akuphunzitsa miyambo imene ife Aroma sitiloledwa kuyilandira kapena kuyichita.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.