New Testament in a Year
Fanizo la Nkhosa Yotayika
15 Tsopano amisonkho ndi “ochimwa” ankasonkhana kudzamvera mawu ake. 2 Koma Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo amangʼungʼudza nati, “Munthu uyu amalandira ochimwa ndi kudya nawo.”
3 Ndipo Yesu anawawuza fanizo ili: 4 “Tiyerekeze kuti mmodzi mwa inu ali ndi nkhosa 100 ndipo imodzi yatayika, kodi iye sangasiye 99 zija kutchire ndi kupita kukafuna yotayikayo mpaka atayipeza? 5 Ndipo iye akayipeza, amayinyamula pa phewa lake mwachimwemwe 6 ndi kupita kwawo. Kenaka amayitana anzake ndi anansi pamodzi, ndi kuti, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza nkhosa yanga yotayika ija.’ 7 Ine ndikukuwuzani kuti momwemonso kudzakhala chikondwerero chachikulu kumwamba chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima kusiyana ndi anthu olungama 99 amene ali otembenuka mtima kale.”
Fanizo la Ndalama Yotayika
8 “Kapena tiyeni tifanizire mayi amene anali ndi ndalama zasiliva khumi ndipo imodzi nʼkutayika, kodi sayatsa nyale ndi kusesa mʼnyumba ndi kufuna mosamalitsa mpaka atayipeza? 9 Ndipo pamene wayipeza, amayitana anzake, ndi anansi pamodzi nati, ‘Kondwerani nane; ine ndayipeza ndalama yanga yotayika ija.’ 10 Momwemonso, Ine ndikukuwuzani kuti angelo a Mulungu amakondwera kwambiri chifukwa cha wochimwa mmodzi amene watembenuka mtima.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.