New Testament in a Year
Yesu Aphunzitsa za ku Pemphera
11 Tsiku lina Yesu amapemphera pamalo ena. Atamaliza, mmodzi wa ophunzira ake anati kwa Iye, “Ambuye tiphunzitseni kupemphera, monga momwe Yohane anaphunzitsira ophunzira ake.”
2 Yesu anawawuza kuti, “Pamene mukupemphera muzinena kuti:
“ ‘Atate,
dzina lanu lilemekezedwe,
ufumu wanu ubwere.
3 Mutipatse chakudya chathu chalero,
4 mutikhululukire machimo athu,
monga ifenso timakhululukira aliyense amene watilakwira.
Ndipo musalole kuti tigwe mʼmayesero.’ ”
5 Kenaka anawawuza kuti, “Tiyerekeze: Mmodzi mwa inu atakhala ndi bwenzi lake, ndipo iye nʼkupita ku nyumba yake pakati pa usiku, nakanena kuti, ‘Mnzanga, bwereke malofu atatu abuledi, 6 chifukwa ndalandira bwenzi langa amene ali pa ulendo ndipo ine ndilibe choti ndimupatse.’
7 “Ndipo yerekezani kuti amene ali mʼnyumbamo ndi kuyankha kuti, ‘Usandivutitse ine, ndatseka kale chitseko, ndipo ine ndi ana anga tagona. Ine sindingadzukenso kuti ndidzakupatse.’ 8 Ine ndikukuwuzani kuti adzadzuka ndi kumupatsa bulediyo, osati chifukwa ndi bwenzi lake, koma chifukwa cha liwuma la munthu wopemphayo, ndipo kudzamupatsa zonse zimene akuzifuna.
9 “Choncho Ine ndikunena kwa inu kuti: Pemphani ndipo adzakupatsani. Funafunani ndipo mudzapeza. Gogodani ndipo adzakutsekulirani. 10 Pakuti aliyense amene amapempha amalandira. Munthu amene amafunafuna amapeza. Iye amene amagogoda amamutsekulira.
11 “Ndani mwa inu abambo, kodi mwana wanu atapempha nsomba, mʼmalo mwake mungamupatse njoka? 12 Kapena atapempha dzira, kodi mungamupatse chinkhanira? 13 Tsono ngati inu, anthu oyipa, mumadziwa kupereka mphatso zabwino kwa ana anu, koposa kotani Atate anu akumwamba, angalephere bwanji kupereka Mzimu Woyera kwa amene awapempha!”
Yesu ndi Belezebabu
14 Yesu amatulutsa chiwanda chimene chinali chosayankhula. Chiwandacho chitatuluka, munthu wosayankhulayo anayankhula, ndipo gulu la anthu linadabwa. 15 Koma ena mwa iwo anati, “Iye akutulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu mfumu ya ziwanda.” 16 Ena anamuyesa pomufunsa chizindikiro chochokera kumwamba.
17 Yesu anadziwa maganizo awo ndipo anawawuza kuti, “Ufumu uliwonse wogawikana udzawonongeka, ndipo nyumba yogawikana idzapasuka. 18 Ngati Satana adziwukira yekha, ufumu wake ungalimbe bwanji? Ine ndikunena izi chifukwa inu mukuti Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu. 19 Tsopano ngati Ine ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Belezebabu, nanga ophunzira anu amazitulutsa ndi mphamvu ya ndani? Choncho, iwowo ndiye adzakhala oweruza anu. 20 Koma ngati ndimatulutsa ziwanda ndi mphamvu ya Mulungu, ndiye kuti ufumu wa Mulungu wafika pakati panu.
21 “Munthu wamphamvu, amene ali ndi zida, akamalondera nyumba yake, katundu wake amatetezedwa. 22 Koma pakabwera wina wamphamvu zoposa namugonjetsa, amalanda zida zimene munthuyo amazidalirazo ndi kugawa katundu wake.
23 “Munthu amene sali mbali yanga ndi wotsutsana nane. Ndipo wosandithandiza kusonkhanitsa, ameneyo ndi womwaza.
Za Mzimu Woyipa
24 “Mzimu woyipa ukatuluka mwa munthu, umakayendayenda ku malo owuma, kufunafuna malo opumulirako ndipo suwapeza. Kenaka umati, ‘Ndibwerera ku nyumba kwanga kumene ndachokera.’ 25 Ukafika umapeza mʼnyumba mosesedwa bwino ndi mokonza. 26 Pamenepo umakatenga mizimu ina isanu ndi iwiri yoyipa kwambiri kuposa iwowo ndipo imakalowa ndi kukhala mʼmenemo. Ndipo makhalidwe otsiriza a munthuyo amakhala oyipa kuposa oyamba aja.”
Munthu Wodala
27 Pamene Yesu ankanena zonsezi, mayi wina mʼgulu la anthuwo anafuwula nati, “Ndi wodala amayi amene anakubalani ndi kukulerani!”
28 Koma Yesu anayankha kuti, “Odala ndi amene amamva mawu a Mulungu ndi kuwasunga.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.