M’Cheyne Bible Reading Plan
Alamulidwa Kukhala Womvera
4 Mverani inu Aisraeli, malangizo ndi malamulo amene ndikuphunzitseni. Muwatsatire kuti mukhale ndi moyo ndi kuti mulowe ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wa makolo anu akukupatsani. 2 Musawonjezere pa zimene ndikukulamulirani ndipo musachotserepo, koma muwasunge malamulo a Yehova Mulungu wanu amene ndikukupatsani.
3 Inu munaona ndi maso anu zimene Yehova anachita ku Baala-Peori. Yehova Mulungu wanu anawononga aliyense amene anatsata Baala wa ku Peori pakati panu. 4 Koma inu nonse amene munagwiritsitsa Yehova Mulungu wanu mukanali ndi moyo mpaka lero.
5 Taonani, ndakuphunzitsani malangizo ndi malamulo monga Yehova Mulungu wanga anandilamulira kuti inuyo muwatsatire mʼdziko limene mukulowa ndi kulitengali. 6 Muwasunge mosamalitsa pakuti zimenezi zidzaonetsa nzeru zanu ndi kuzindikira kwanu kwa anthu a mitundu ina, amene adzamva za malangizo onsewa nati, “Ndithudi, mtundu waukulu uwu ndi wa anthu anzeru ndi ozindikira.” 7 Mtundu wina wa anthu ndi uti umene uli waukulu chomwechi, woti ukhoza kukhala ndi milungu yawo pafupi monga mmene alili Yehova Mulungu wathu ndi ife nthawi zonse pamene tipemphera kwa Iye? 8 Ndipo ndi mtundu uti mwa mitundu ya anthu umene ndi waukulu chotere kuti nʼkukhala ndi malangizo ndi malamulo olungama ngati malamulo amene ndikuyika pamaso panu lero?
9 Inu mungosamala ndi kudziyangʼanira kwambiri nokha kuti musayiwale zimene maso anu aona. Musalole kuti zichoke mʼmitima mwanu pa moyo wanu wonse. Zimenezi muziphunzitse kwa ana anu ndi zidzukulu zanu ngakhale mʼtsogolo. 10 Kumbukirani tsiku limene munayimirira pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku Horebu, pamene anati kwa ine, “Sonkhanitsa anthu pamaso panga kuti amve mawu anga ndi kuti aphunzire kundilemekeza mʼmoyo wawo onse mʼdzikomo ndi kuti ana awo aziwaphunzitsa zimenezi.” 11 Munabwera pafupi ndi kuyima pa tsinde pa phiri pamene phirilo limayaka moto umene umafika mpaka kumwamba. Panalinso mtambo wakuda ndi mdima wambiri. 12 Kenaka Yehova anayankhula nanu kuchokera mʼmotowo. Inu munamva mawu ake okha koma simunamuone pakuti panali mawu chabe. 13 Iye anakuwuzani Malamulo Khumi omwe ndi pangano lake limene anakulamulirani kuti mutsatire. Ndipo anawalemba malamulowo pa mapale awiri a miyala. 14 Ndipo Yehova anandilamula nthawi imene ija kuti ndikuphunzitseni malangizo ndi malamulo amene muyenera kutsata mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani.
Mafano Aletsedwa
15 Tsiku limene Yehova anayankhula nanu ku Horebu mʼmoto uja, simunaone thupi lake. Choncho mudziyangʼanire nokha mosamalitsa, 16 kuti musasokonezeke ndi kudzipangira nokha fano kapena chifanizo cha mtundu uliwonse, kaya chokhala ngati mwamuna kapena ngati mkazi, 17 kaya chokhala ngati nyama iliyonse ya pa dziko lapansi kapena mbalame iliyonse yowuluka mlengalenga. 18 Kapena cholengedwa chilichonse choyenda pa nthaka kapena nsomba ya mʼmadzi akuya. 19 Ndipo pamene muyangʼana kumwamba muona dzuwa, mwezi ndi nyenyezi, zonse zakumwambazo musakopeke kuti muzigwadire ndi kumapembedza zinthu zimene Yehova wapereka kwa anthu a mitundu yonse pa dziko lapansi. 20 Koma inuyo, Yehova anakutengani ndi kukutulutsani mʼngʼanjo yosungunulira zitsulo, ku Igupto kuti mukhale anthu olandira chuma chake monga mmene mulili tsopano.
21 Yehova anakwiya nane chifukwa cha inu, ndipo analumbira kwathunthu kuti sindidzawoloka Yorodani ndi kulowa mʼdziko labwinolo limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani inu ngati cholowa chanu. 22 Ine ndifera mʼdziko lino, sindiwoloka Yorodani. Koma inu mwatsala pangʼono kuwoloka ndi kukatenga dziko labwinolo. 23 Samalani, musayiwale pangano limene Yehova Mulungu wanu anapangana nanu ndipo musadzipangire nokha fano la chinthu chilichonse chimene Yehova Mulungu wanu waletsa. 24 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi moto wonyeketsa ndipo ndi Mulungu wansanje.
25 Mukadzakhala nthawi yayitali mʼdzikomo ndi kubereka ana ndi kukhala ndi zidzukulu ndipo mukadzasokonekera ndi kupanga fano la mtundu uliwonse, nʼkumachita zoyipa pamaso pa Yehova Mulungu wanu ndi kumukwiyitsa, 26 ine ndi kuti kumwamba ndi dziko lapansi zikhale mboni lero zokutsutsani kuti mudzawonongedwa msanga ndipo mudzachotsedwa mʼdziko limene mutenge mukawoloka Yorodani. Simudzakhalitsa kumeneko koma mudzawonongedwa ndithu. 27 Yehova adzakubalalitsani pakati pa anthu ena. Ochepa okha pakati panu ndi amene adzapulumuke pakati pa anthu a mitundu ina kumene Yehova adzakupirikitsireniko. 28 Kumeneko mudzapembedza milungu ya mitengo ndi miyala yopangidwa ndi anthu, imene singaone kapena kumva kapena kudya kapena kununkhiza. 29 Mukanali komweko, ngati mudzamufunafuna Yehova Mulungu wanu mudzamupeza koma ngati mutamufunafuna ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse. 30 Mukadzakhala pa chipsinjo ndipo zonsezi zikadzakuchitikirani, ndi pamene pambuyo pake mudzabwerera kwa Yehova Mulungu wanu ndi kumumvera Iye. 31 Pakuti Yehova Mulungu wanu ndi Mulungu wachifundo, Iye sadzakutayani kapena kukuwonongani kapena kuyiwala pangano lake ndi makolo anu, limene analitsimikiza mwa lumbiro.
Yehova Ndiye Mulungu
32 Tsopano tafunsani za masiku a mʼmbuyomu, zakale inu musanabadwe, kuyambira tsiku limene Mulungu analenga munthu pa dziko lapansi. Tafufuzani kuyambira kumapeto mpaka mapeto anzake a thambo. Kodi chinachitikako china chachikulu ngati ichi, kapena chinayamba chamvekako chokhala ngati ichi? 33 Kodi uliponso mtundu wina wa anthu umene unamva mawu a Mulungu akuyankhula kuchokera mʼmoto nʼkukhala ndi moyo monga mwachitira inumu? 34 Kodi alipo mulungu amene anayeserapo kudzitengera mtundu wa anthu kuwachotsa mu mtundu unzake mwa mayesero, zizindikiro zozizwitsa, nkhondo, komanso mwa mphamvu zake zopanda malire, kapena mwa zochita zazikulu ndi zochititsa mantha, monga zimene Yehova Mulungu wanu anakuchitirani ku Igupto inu mukupenya?
35 Iye anakuonetsani zonsezi kuti inu muzindikire kuti Yehova ndiye Mulungu, palibenso wina wofanana naye. 36 Kuchokera kumwamba, Iye anafuna kuti inu mumve mawu ake ndi kuti mukhale osunga mwambo. Pa dziko lapansi anakuonetsani moto waukulu, ndipo inu munamva mawu ake kuchokera mʼmotomo. 37 Popeza anakonda makolo anu ndi kusankha adzukulu awo, a pambuyo pawo, anakutulutsani kuchoka ku Igupto ali pakati panu ndi mphamvu yake, 38 kuti akupirikitsireni mayiko akuluakulu ndi amphamvu kuposa inu, ndi kukubweretsani inu ku dziko lawo kuti likhale lanu, monga liliri lero.
39 Vomerezani lero ndipo dziwani mu mtima mwanu kuti Yehova ndiye Mulungu kumwamba ndi pa dziko lapansi. Palibenso wina. 40 Sungani malangizo ake ndi malamulo ake amene ndikukupatsani lero lino, kuti zikuyendereni bwino inu ndi ana anu kutsogoloko, ndi kuti mukhalitse mʼdziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani kwa nthawi zonse.
Mizinda Yothawirako
41 Kenaka Mose anapatula mizinda itatu cha kummawa kwa Yorodani, 42 kumene aliyense amene wapha munthu akhoza kuthawirako ngati wopha munthuyo sanaphe mnzakeyo mwadala ndi maganizo oyipa. Iye akhoza kuthawira ku umodzi mwa mizinda imeneyi napulumutsa moyo wake. 43 Mizindayo inali iyi: ku fuko la Rubeni, unali mzinda wa Bezeri ku mapiri a ku chipululu; ku fuko la Gadi, unali Ramoti ku Giliyadi; ndipo ku fuko la Manase, unali Golani ku Basani.
Kufotokozera za Malamulo
44 Awa ndi malamulo amene Mose anapereka kwa Aisraeli. 45 Izi ndi ndondomeko, malangizo ndi malamulo amene Mose anawapatsa iwo pamene anatuluka ku Igupto. 46 Anali ku chigwa cha kufupi ndi Beti-Peori mbali ya kummawa kwa Yorodani, mʼdziko la Sihoni mfumu ya Aamori amene ankalamulira ku Hesiboni ndipo anagonjetsedwa ndi Mose ndi Aisraeli pamene ankachokera ku Igupto. 47 Iye anamulanda dziko lake ndi dziko la Ogi mfumu ya ku Basani. Awa anali mafumu awiri Aamori a kummawa kwa Yorodani. 48 Dziko ili linayambira ku Aroeri cha kumphepete kwa khwawa la Arinoni ku phiri la Siyoni (limeneli ndi phiri la Herimoni), 49 ndi kuphatikizapo dziko lonse la Araba cha kummawa kwa Yorodani mpaka kukafika ku Nyanja ya Araba, kumunsi kwa Phiri la Pisiga.
Pemphero la Davide.
86 Ndimvereni Yehova ndipo mundiyankhe,
pakuti ndine wosauka ndi wosowa.
2 Yangʼanirani moyo wanga, pakuti ndine wodzipereka kwa Inu.
Inu ndinu Mulungu wanga;
pulumutsani mtumiki wanu amene amadalira Inu.
Inu ndinu Mulungu wanga.
3 Mundichitire chifundo, Inu Ambuye,
pakuti ndikuyitana Inu tsiku lonse.
4 Bweretsani chimwemwe kwa mtumiki wanu, Ambuye,
pakuti ndimadalira Inu.
5 Inu Ambuye, ndinu wokhululuka ndi wabwino,
wodzaza ndi chikondi kwa onse amene amayitana Inu.
6 Yehova imvani pemphero langa;
mvetserani kulira kwanga kofuna chifundo.
7 Pa tsiku la mavuto anga ndidzayitana Inu,
pakuti Inu mudzandiyankha.
8 Pakati pa milungu palibe wina wofanana nanu Ambuye;
palibe ntchito zolingana ndi ntchito zanu.
9 Mitundu yonse ya anthu imene munayipanga
idzabwera ndi kudzalambira pamaso panu Ambuye;
iwo adzabweretsa ulemerero pa dzina lanu.
10 Pakuti ndinu wamkulu ndipo mumachita zodabwitsa;
Inu nokha ndiye Mulungu.
11 Ndiphunzitseni njira yanu Yehova,
ndipo ndidzayenda mʼchoonadi chanu;
patseni mtima wosagawikana
kuti ndilemekeze dzina lanu.
12 Ndidzakutamandani Ambuye Mulungu wanga, ndi mtima wanga wonse;
ndidzalemekeza dzina lanu kwamuyaya.
13 Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu kwa ine;
mwandipulumutsa ku malo ozama a manda.
14 Inu Mulungu wanga, anthu odzikuza akundithira nkhondo;
anthu ankhanza akufuna kundipha,
amene salabadira za Inu.
15 Koma Ambuye ndinu Mulungu wachifundo ndi wokoma mtima,
wosakwiya msanga, wodzaza ndi chikondi ndi wokhulupirika.
16 Tembenukirani kwa ine ndipo ndichitireni chifundo;
perekani mphamvu zanu kwa mtumiki wanu
ndipo pulumutsani mwana wa mdzakazi wanu.
17 Mundionetse chizindikiro cha ubwino wanu
kuti adani achione ndi kuchititsidwa manyazi,
pakuti Yehova mwandithandiza ndi kunditonthoza.
Salimo la Ana a Kora.
87 Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;
2 Yehova amakonda zipata za Ziyoni
kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.
3 Za ulemerero wako zimakambidwa,
Iwe mzinda wa Mulungu:
Sela
4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni
pakati pa iwo amene amandidziwa.
Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,
ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”
5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,
“Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,
ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”
6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:
“Uyu anabadwira mʼZiyoni.”
Sela
7 Oyimba ndi ovina omwe adzati,
“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”
Ufumu Wachilungamo
32 Taonani, kudzakhala mfumu ina imene idzalamulira mwachilungamo,
ndipo akalonga ake adzaweruza molungama.
2 Munthu aliyense adzakhala ngati pothawirapo mphepo
ndi malo obisalirapo namondwe,
adzakhala ngati mitsinje ya mʼchipululu,
ngati mthunzi wa thanthwe lalikulu la mʼdziko lowuma.
3 Ndipo maso a anthu openya sadzakhalanso otseka,
ndipo makutu a anthu akumva adzamvetsetsa.
4 Anthu a mtima wopupuluma adzadziwa ndi kuchita zinthu mofatsa,
ndipo anthu ovutika kuyankhula adzayankhula mosadodoma ndi momveka.
5 Chitsiru sichidzatchedwanso munthu waulemu wake
ndipo munthu woyipa sadzalemekezedwa.
6 Pakuti munthu opusa amayankhula zauchitsiru,
amaganiza kuchita zoyipa:
Iye amachita zoyipira Mulungu,
ndipo amafalitsa zolakwika zokhudza Yehova;
anjala sawapatsa chakudya
ndipo aludzu sawapatsa madzi.
7 Munthu woyipa njira zake ndi zoyipanso,
iye kwake nʼkulingalira zinthu zoyipa.
Amalingalira zakuti awononge anthu aumphawi ndi mabodza ake
ngakhale kuti waumphawiyo akuyankhula zoona.
8 Koma munthu wolemekezeka amalingaliranso kuchita zinthu zabwino,
Iye amakhazikika pa zinthu zabwinozo.
Akazi a ku Yerusalemu
9 Khalani maso, inu akazi
amene mukungokhala wopanda kulingalira kuti kunja kulinji
ndipo imvani mawu anga.
Inu akazi odzitama, imvani zimene ndikunena!
10 Pakapita chaka ndi masiku pangʼono
inu akazi amatama mudzanjenjemera;
chifukwa mitengo ya mphesa idzakanika
ndipo zipatso sizidzaoneka.
11 Nthunthumirani inu okhala mosatekesekanu;
ndipo njenjemerani, inu akazi omadzikhulupirira nokhanu.
Vulani zovala zanu,
ndipo valani ziguduli mʼchiwuno mwanu.
12 Dzigugudeni pachifuwa mwachisoni chifukwa minda yachonde,
ndi mphesa yawonongeka.
13 Mʼdziko la anthu anga
mwamera minga ndi mkandankhuku.
Zoona, mulilire nyumba zonse zachikondwerero
ndi mzinda uno umene unali wachisangalalo.
14 Nyumba yaufumu idzasiyidwa,
mzinda waphokoso udzakhala wopanda anthu;
malinga ndi nsanja zidzasanduka chipululu mpaka muyaya.
Abulu adzasangalalamo ndipo ziweto zidzapezamo msipu.
15 Yehova adzatipatsa mzimu wake,
ndipo dziko lachipululu lidzasanduka munda wachonde,
ndipo munda wachonde udzakhala ngati nkhalango.
16 Tsono mʼchipululu mudzakhala chiweruzo cholungama
ndipo mʼminda yachonde mudzakhala chilungamo.
17 Mtendere udzakhala chipatso chachilungamo;
zotsatira za chilungamo zidzakhala bata ndi kudzidalira mpaka muyaya.
18 Anthu anga adzakhala mʼmidzi yamtendere,
mʼnyumba zodalirika,
ndi malo osatekeseka a mpumulo.
19 Ngakhale nkhalango idzawonongedwa ndi matalala
ndipo mzinda udzagwetsedwa mpaka pansi,
20 inutu mudzakhala odalitsika ndithu.
Mudzadzala mbewu zanu mʼmbali mwa mtsinje uliwonse,
ndipo ngʼombe zanu ndi abulu anu zidzadya paliponse.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Efeso
2 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Efeso kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi nyenyezi zisanu ndi ziwiri zija mʼdzanja lake lamanja amene akuyenda pakati pa zoyikapo nyale zisanu ndi ziwiri zagolide. 2 Ine ndimadziwa zochita zako, ntchito yako yowawa ndi kupirira kwako. Ine ndimadziwa kuti sungalekerere anthu oyipa amene amadzitcha atumwi pamene sichoncho, unawayesa, ndipo unawapeza kuti ndi abodza. 3 Iwe wapirira ndipo wakumana ndi zovuta chifukwa cha dzina langa, ndipo sunatope.
4 Komabe ndili ndi chotsutsana nawe: Wataya chikondi chako chapoyamba. 5 Kumbukirani kuti munagwa kuchokera patali. Lapa ndikuchita zinthu zimene unkachita poyamba. Ngati sulapa ndidzabwera ndikukuchotsera choyikapo nyale chako pamalo pake. 6 Komabe chokomera chako ndi chakuti umadana ndi zochita za Anikolai, zimene Inenso ndimadana nazo.
7 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana, ndidzamupatsa ufulu wakudya zipatso za mtengo wopatsa moyo umene uli ku paradizo wa Mulungu.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Simurna
8 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Simurna kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ndi Woyamba ndi Wotsiriza, amene anafa nʼkukhalanso ndi moyo. 9 Ine ndimadziwa masautso ako ndi umphawi wako, chonsecho ndiwe wolemera! Ndikudziwa zimene amakusinjirira anthu amene amati ndi Ayuda pamene sizili choncho, koma ndi a mpingo wa Satana. 10 Musachite mantha ndi zimene muti musauke nazo posachedwapa. Ndithu, Satana adzayika ena a inu mʼndende pofuna kukuyesani, ndipo mudzazunzika kwa masiku khumi. Khalani okhulupirika ngakhale zitafika pa imfa, ndipo Ine ndidzakupatsani chipewa cha ulemerero wamoyo.
11 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Amene adzapambana sadzapwetekedwa ndi pangʼono pomwe ndi imfa yachiwiri.
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Pergamo
12 “Lembera mngelo wa mpingo wa ku Pergamo kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa amene ali ndi lupanga lakuthwa konsekonse. 13 Iye akuti, ‘Ine ndimadziwa kumene mumakhala, kumene kuli mpando waufumu wa Satana. Komabe inu ndinu okhulupirika kwa Ine. Simunataye chikhulupiriro chanu pa Ine, ngakhale mʼmasiku a Antipa, mboni yanga yokhulupirika, amene anaphedwa mu mzinda wanu, kumene amakhala Satana.
14 Komabe, ndili ndi zinthu zingapo zotsutsana nanu. Kumeneko muli ndi anthu ena amene amatsata ziphunzitso za Balaamu, uja amene anaphunzitsa Baraki kukopa Aisraeli kuti azidya nsembe zoperekedwa ku mafano ndi kumachita chigololo. 15 Chimodzimodzinso inuyo muli ndi ena amene amatsatira ziphunzitso za Anikolai. 16 Tsono tembenukani mtima. Mukapanda kutero, ndidzabwera kwanuko posachedwa ndipo ndidzachita nanu nkhondo ndi lupanga lotuluka mʼkamwa mwanga lija.
17 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo. Kwa amene adzapambane ndidzamupatsa chakudya chobisika cha mana. Ndidzamupatsanso mwala woyera wolembedwapo dzina latsopano, lodziwa iye yekha amene walandirayo.’ ”
Kalata Yolembera Mpingo wa ku Tiyatira
18 “Lembera mngelo wampingo wa ku Tiyatira kuti:
Awa ndi mawu ochokera kwa Mwana wa Mulungu, amene maso ake ali ngati moto woyaka ndi mapazi ake ngati chitsulo chonyezimira. 19 Iye akuti: Ndimadziwa ntchito zanu, chikondi chanu ndi chikhulupiriro chanu, kutumikira kwanu ndi kupirira kwanu. Ndikudziwa tsopano kuti ntchito zanu ndi zabwino kuposa zoyamba zija.
20 Komabe ndili ndi chinthu chokudzudzula nacho. Umamulekerera mkazi uja Yezebeli amene amadzitcha yekha kuti ndi mneneri. Iye amaphunzitsa atumiki anga kuti azichita zadama ndi kumadya zansembe zoperekedwa ku mafano. 21 Ndamupatsa nthawi kuti aleke zachigololo zake koma sakufuna. 22 Tsono ndidzamugwetsa mʼmasautso ndipo amene amachita naye zadama zakezo ndidzawasautsa kwambiri akapanda kulapa ndi kuleka njira za mkaziyo. 23 Ana ake ndidzawakantha ndi kuwapheratu. Kotero mipingo yonse idzadziwa kuti Ine ndine uja amene ndimafufuza mʼmitima mwa anthu ndi mʼmaganizo mwawo. Aliyense wa inu ndidzachita naye monga mwa ntchito zake.
24 Tsopano ndikunena kwa enanu a ku Tiyatira, kwa inu amene simunatsate chiphunzitso cha mkaziyo ndipo simunaphunzire zimene iwo amati ndi ‘zinsinsi zonama’ za Satana. Kwa inu mawu anga ndi akuti sindikuwunjikirani malamulo ena. 25 Inu mungogwiritsa zimene munaphunzira basi, mpaka Ine ndidzabwere.
26 Amene adzapambana ndi kuchita chifuniro changa mpaka kumapeto, ndidzamupatsa ulamuliro pa mitundu yonse ya anthu. 27 Adzayilamulira ndi ndodo yachitsulo ndipo nadzayiphwanyaphwanya ngati mbiya. Ulamuliro umenewu ndi omwe ndinalandira kwa Atate anga. 28 Ine ndidzamupatsanso nthanda, nyenyezi yowala mʼmamawa ija. 29 Amene ali ndi makutu, amve zimene Mzimu akuwuza mipingo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.