Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

M’Cheyne Bible Reading Plan

The classic M'Cheyne plan--read the Old Testament, New Testament, and Psalms or Gospels every day.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 38

Guwa Lansembe Yopsereza

38 Anapanga guwa lansembe zopsereza lamatabwa amtengo wa mkesha. Linali lofanana mbali zonse. Msinkhu wake masentimita 137, mulitali mwake masentimita 229, mulifupi masentimita 229. Anapanga nyanga imodziimodzi pa ngodya zake zinayizo, kotero kuti nyangazo ndi guwalo zinali chinthu chimodzi, ndipo anakuta guwalo ndi mkuwa. Anapanganso ziwiya zamkuwa izi zogwirira ntchito pa guwalo: miphika, mafosholo, mabeseni owazira magazi, ngowe zokowera nyama ndi zosonkhezera moto. Anapanga sefa yachitsulo chamkuwa ya guwa lansembelo kuti ikhale mmunsi mwa khoma la guwa lansembelo, kuchokera pansi mpaka pakati pa khoma la guwalo. Anapanga mphete zamkuwa zinayi ndipo anazilumikiza ku ngodya zinayi za sefa ija kuti zigwire nsichi zonyamulira. Anapanga nsichi zamtengo wa mkesha ndipo anazikuta ndi mkuwa. Iwo analowetsa nsichizo mʼmphetemo mbali zonse ziwiri za guwalo kuti azinyamulira. Guwalo linali lamatabwa ndi logoba mʼkati mwake.

Beseni Losambira

Anapanga beseni lamkuwa lokhala ndi miyendo yamkuwanso kuchokera ku magalasi oyangʼanira nkhope a amayi amene ankatumikira pa chipata cha tenti ya msonkhano.

Bwalo la Chihema

Kenaka anapanga bwalo la chihema. Mbali yakummwera inali yotalika mamita 46 ndipo kunali nsalu yotchinga yofewa yosalala yolukidwa bwino. 10 Anapanganso mizati makumi awiri, matsinde makumi awiri amkuwa ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. 11 Mbali yakumpoto inalinso yotalika mamita 46 ndipo inali ndi mizati makumi awiri, matsinde amkuwa makumi awiri, ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo.

12 Mbali yakumadzulo inali yotalika mamita 23 ndipo inali ndi nsalu yotchinga, mizati khumi ndi matsinde khumi. Inalinso ndi ngowe zasiliva ndi zingwe za mizatiyo. 13 Mbali yakummawa, kotulukira dzuwa, inalinso yotalika mamita 23. 14 Mbali imodzi yachipata kunali nsalu yotchinga yotalika mamita asanu ndi awiri, mizati itatu ndi matsinde atatu, 15 polowera mʼbwalo panali nsalu yotchinga ya mamita asanu ndi awiri pamodzi ndi mizati itatu ndi matsinde atatu. 16 Katani yonse yotchinga kuzungulira chihema inali yofewa, yosalala ndi yolukidwa bwino. 17 Matsinde amizati anali amkuwa. Ngowe ndi zingwe za mizati zinali zasiliva, ndipo pamwamba pa mizatiyo anakutapo siliva. Choncho mizati yonse ya bwalolo inalumikizidwa ndi zingwe zasiliva.

18 Nsalu yotchinga ya pa chipata inali yamtundu wa mtambo, yapepo ndi yofiira, yofewa yosalala ndi yopangidwa ndi anthu aluso. Nsaluyo inali yotalika mamita asanu ndi anayi, molingana ndi nsalu zotchinga bwalo. Msinkhu wake unali masentimita 229, 19 pamodzi ndi mizati yake inayi ndi matsinde amkuwa anayi. Ngowe ndi zingwe zake zinali za siliva, ndipo pamwamba pake pa mzati anakutapo ndi siliva. 20 Zikhomo za chihema ndi zina zonse zozungulira chihemacho zinali zamkuwa.

Zipangizo Zachitsulo za ku Malo Opatulika

21 Chiwerengero cha zipangizo zimene anagwiritsa ntchito popanga chihema, chihema chaumboni, zimene Mose analamulira Alevi kuti alembe motsogozedwa ndi Itamara mwana wa Aaroni, wansembe, chinali ichi: 22 Bezaleli mwana wa Uri, mwana wa Huzi wa fuko la Yuda anapanga chilichonse Yehova analamulira Mose, 23 pamodzi ndi Oholiabu mwana wa Ahisamaki, wa fuko la Dani, wa luso la zopangapanga ndi kulemba mapulani, ndi wopanga nsalu zolukidwa bwino za mtundu wa mtambo, yapepo ndi zofiira, zofewa ndi zosalala. 24 Golide yense wochokera ku nsembe yoweyula amene anagwiritsa ntchito pa ntchito yonse yopanga malo wopatulika anali wolemera makilogalamu 1,000 potsata miyeso ya kumalo wopatulika.

25 Siliva wochokera ku gulu lonse la anthu anali wolemerera makilogalamu 3,430, potsata miyeso ya ku malo wopatulika. 26 Munthu aliyense amapereka beka imodzi, kufanana ngati makilogalamu 6, potsata muyeso wa ku malo wopatulika. Kuchokera kwa aliyense amene anawerengedwa kuyambira zaka 20 kapena kuposerapo, amuna onse analipo 603,550. 27 Anagwiritsa ntchito siliva wolemera makilogalamu 3,400 kupanga matsinde 100 a ku malo wopatulika ndi makatani, ndipo makilogalamu 34 kupanga tsinde limodzi. 28 Makilogalamu otsalawo anagwiritsa ntchito popanga ngowe zamzati kukutira pamwamba pa mizati ndiponso kupanga zingwe zake.

29 Mkuwa ochokera ku nsembe yoweyula unali makilogalamu 2,425. 30 Iwo anawugwiritsa ntchito popanga matsinde a pa chipata cha tenti ya msonkhano, guwa la mkuwa pamodzi ndi sefa yake ndiponso ziwiya zonse, 31 matsinde ozungulira bwalo ndiponso a pa chipata pake, ndi zikhomo zonse za tentiyo ndi matsinde a malo wozungulirapo.

Yohane 17

Yesu Adzipempherera Yekha

17 Yesu atatha kunena izi, anayangʼana kumwamba ndipo anapemphera:

“Atate, nthawi yafika. Lemekezani Mwana wanu, kuti Mwana wanuyo akulemekezeni Inu. Pakuti Inu munamupatsa Iye ulamuliro pa anthu onse kuti apereke moyo wosatha kwa onse amene mwamupatsa. Tsono moyo wosathawo ndi uwu: Iwo akudziweni Inu, Mulungu yekhayo woona, ndi Yesu Khristu, amene Inu mwamutuma. Ine ndabweretsa ulemerero wanu pa dziko pamene ndamaliza ntchito imene munandipatsa kuti ndi igwire. Ndipo tsopano, Atate, ndilemekezeni Ine pamaso panu ndi ulemerero uja umene ndinali nawo kwa Inu dziko lapansi lisanayambe.

Yesu Apempherera Ophunzira Ake

“Ine ndawadziwitsa za Inu anthu amene munandipatsa mʼdziko lapansi. Iwo anali anu. Inu munawapereka kwa Ine ndipo amvera mawu anu. Tsopano akudziwa kuti zonse zimene munandipatsa nʼzochokera kwa Inu. Pakuti Ine ndiwapatsa mawu amene Inu munandipatsa ndipo awalandira. Iwo akudziwa ndithu kuti Ine ndinachokera kwa Inu, ndipo akukhulupirira kuti Inu ndiye amene munandituma Ine. Ine ndikuwapempherera. Ine sindikupempherera dziko lapansi, koma anthu amene Inu mwandipatsa, pakuti ndi anu. 10 Zonse zimene Ine ndili nazo ndi zanu, ndipo zonse zimene Inu muli nazo ndi zanga. Choncho Ine ndalemekezedwa mwa iwowo. 11 Ine sindikukhalanso mʼdziko lapansi nthawi yayitali, koma iwo akanali mʼdziko lapansi. Ine ndikubwera kwa Inu. Atate Woyera, atetezeni ndi mphamvu za dzina lanu. Dzina limene munandipatsa Ine, kuti iwo akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 12 Pamene ndinali nawo, ndinawateteza ndi kuwasunga mosamala mʼdzina limene munandipatsa. Palibe ndi mmodzi yemwe amene anatayika kupatula yekhayo amene anayenera kuwonongeka kuti malemba akwaniritsidwe.

13 “Tsopano ndikubwera kwa Inu. Ndikunena izi ndikanali mʼdziko lapansi, kuti iwo akhale ndi muyeso wodzaza wachimwemwe changa mʼkati mwawo. 14 Ine ndawapatsa mawu anu ndipo dziko lapansi likudana nawo, pakuti sali a dziko lapansi monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 15 Sindikupempha kuti muwachotse mʼdziko lapansi koma kuti muwateteze kwa woyipayo. 16 Iwo si a dziko lapansi, monga Ine sindilinso wa dziko lapansi. 17 Ayeretseni ndi choonadi chanu. Mawu anu ndiye choonadi. 18 Monga Inu munandituma Ine mʼdziko lapansi, Inenso ndikuwatuma mʼdziko lapansi. 19 Chifukwa cha iwowa Ine ndikudziyeretsa, kuti iwo ayeretsedwenso kwenikweni.

Yesu Apempherera Okhulupirira Onse

20 “Ine sindikupempherera iwo okhawa, komanso amene adzandikhulupirira chifukwa cha uthenga wawo. 21 Ndikuwapempherera kuti onsewa akhale amodzi. Monga Inu Atate muli mwa Ine ndi Ine mwa Inu, iwonso akhale mwa Ife kuti dziko lapansi likhulupirire kuti Inu munandituma Ine. 22 Ine ndawapatsa ulemerero umene munandipatsa Ine, kuti akhale amodzi monga Ife tili amodzi. 23 Ine ndikhale mwa iwo ndipo Inu mwa Ine kuti umodzi wawo ukhale wangwiro. Choncho dziko lapansi lidzadziwa kuti Inu munandituma Ine ndipo Inu mwawakonda iwowa monga momwe Inu munandikondera Ine.

24 “Atate, Ine ndikufuna kuti anthu amene mwandipatsa Ine adzakhale ndi Ine kumene kuli Ine, ndi kuona ulemerero wanga, ulemerero umene munandipatsa chifukwa Inu munandikonda dziko lapansi lisanalengedwe.

25 “Atate wolungama, ngakhale kuti dziko lapansi silikudziwani Inu, Ine ndimakudziwani, ndipo iwo amadziwa kuti Inu munandituma Ine. 26 Ine ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiriza kuwadziwitsa dzina lanulo, kuti chikondi chomwe munandikonda nacho chikhale mwa iwo, ndipo Ine mwa iwo.”

Miyambo 14

14 Mkazi wanzeru amamanga banja lake,
    koma mkazi wopusa amalimasula ndi manja ake omwe.

Amene amayenda molungama amaopa Yehova,
    koma amene njira zake ndi zoyipa amanyoza Yehova.

Kuyankhula kwa chitsiru kumamuyitanira ndodo pa msana,
    koma milomo ya munthu wanzeru imamuteteza.

Pakasowa ngʼombe zolima gome limakhala lopanda chakudya,
    koma pakakhala ngʼombe zamphamvu zakudya zimachulukanso.

Mboni yokhulupirika sinama,
    koma mboni yonyenga imayankhula zabodza.

Wonyoza anzake amafunafuna nzeru koma osayipeza,
    koma munthu womvetsa bwino amadziwa zinthu msanga.

Khala kutali ndi munthu wopusa
    chifukwa sudzapeza mawu a nzeru.

Nzeru za munthu wochenjera zagona pakuzindikira njira zake.
    Koma uchitsiru wa zitsiru umapusitsidwa ndi chinyengo chawo chomwe.

Zitsiru zimanyoza za kulapa machimo, awo,
    koma kufuna kwabwino kumapezeka mwa anthu olungama.

10 Mtima uliwonse umadziwa wokha zowawa zake,
    ndipo palibe wina aliyense angadziwe kukondwa kwake.

11 Nyumba ya munthu woyipa idzapasuka,
    koma tenti ya munthu wowongoka mtima idzakhazikika.

12 Pali njira ina yooneka ngati yabwino kwa munthu,
    koma kumatsiriziro kwake ndi ku imfa.

13 Ngakhale poseka mtima utha kumva kuwawa,
    ndipo mathero achimwemwe akhoza kukhala chisoni.

14 Munthu wosakhulupirika adzalandira zogwirizana ndi ntchito yake,
    koma munthu wabwino adzalandira mphotho ya ntchito yake.

15 Munthu wopusa amakhulupirira chilichonse,
    koma munthu wochenjera amaganizira bwino mayendedwe ake.

16 Munthu wanzeru amaopa Mulungu ndipo amapewa zoyipa,
    koma munthu wopusa ndi wokula mtima amakhala wosasamala.

17 Munthu wopsa mtima msanga amachita zinthu za uchitsiru,
    ndipo anthu amadana ndi munthu wachinyengo.

18 Anthu opusa amalandira uchitsiru,
    koma anthu ochenjera amavekedwa chipewa cha ulemerero wa kudziwa zinthu.

19 Anthu oyipa adzagwada pamaso pa anthu abwino,
    ndipo anthu oyipa adzapempha thandizo kwa anthu olungama.

20 Munthu wosauka ngakhale anansi ake omwe amamuda,
    koma munthu wolemera ali ndi abwenzi ambiri.

21 Wonyoza mnansi wake ndi wochimwa
    koma ndi wodala amene amachitira chifundo anthu osowa.

22 Kodi amene amakonzekera zoyipa sasochera?
    Koma amene amakonzekera zabwino anthu amawaonetsa chikondi ndi kukhulupirika.

23 Ntchito iliyonse imakhala ndi phindu,
    koma kuyankhulayankhula kumabweretsa umphawi.

24 Chipewa chaulemu cha anthu a nzeru ndi chuma chawo chomwe,
    koma malipiro a zitsiru ndi uchitsiru.

25 Mboni yokhulupirika imapulumutsa miyoyo,
    koma mboni yabodza imaphetsa.

26 Amene amaopa Yehova ali ndi chitetezo chokwanira
    ndipo iye adzakhala pothawira pa ana ake.

27 Kuopa Yehova ndiye kasupe wamoyo,
    kumathandiza munthu kuti apewe msampha wa imfa.

28 Gulu lalikulu la anthu ndiye ulemerero wa mfumu,
    koma popanda anthu kalonga amawonongeka.

29 Munthu wosapsa mtima msanga amamvetsa zinthu kwambiri,
    koma munthu wopsa mtima msanga amaonetsa uchitsiru wake.

30 Mtima wodekha umapatsa thupi moyo,
    koma nsanje imawoletsa mafupa.

31 Amene amapondereza mʼmphawi amanyoza mlengi wake,
    koma wochitira chifundo munthu wosowa amalemekeza Mulungu.

32 Anthu oyipa adzakanthidwa chifukwa cha ntchito zawo zomwe,
    koma olungama adzatetezedwa mwa imfa yawo.

33 Nzeru zimakhala mu mtima mwa anthu omvetsa zinthu,
    koma nzeru sipezeka mu mtima mwa zitsiru.

34 Chilungamo chimakweza mtundu wa anthu,
    koma uchimo umachititsa manyazi mtundu uliwonse.

35 Mfumu imasangalatsidwa ndi wantchito wanzeru,
    koma imachitira ukali wantchito wochititsa manyazi.

Afilipi 1

Paulo ndi Timoteyo, atumiki a Khristu Yesu.

Kulembera anthu onse oyera mtima a ku Filipi amene ali mwa Khristu Yesu, pamodzi ndi oyangʼanira ndi atumiki awo.

Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale kwa inu.

Kuyamika ndi Pemphero

Ndimayamika Mulungu wanga nthawi zonse ndikakumbukira inu. Mʼmapemphero anga onse opempherera inu, nthawi zonse ndimapemphera ndi chimwemwe chifukwa mwakhala mukundithandiza polalikira Uthenga Wabwino kuyambira tsiku loyamba mpaka tsopano. Sindikukayika konse kuti Iye amene anayamba ntchito yabwino mwa inu adzayipitiriza ndi kuyimaliza mpaka pa tsiku la kubweranso kwa Khristu Yesu.

Kwa ine ndi bwino kuti ndiziganiza zotere za nonsenu, popeza ndimakukondani, ngakhale ndikhale mʼndende, kapena pamene ndikuteteza ndi kukhazikitsa Uthenga Wabwino, inu nonse mumagawana nane chisomo cha Mulungu. Mulungu angandichitire umboni kuti ndimakulakalakani ndi chikondi cha Khristu Yesu.

Ndipo pemphero langa ndi lakuti chikondi chanu chipitirire kukulirakulira pa chidziwitso ndi kuzama mʼmaganizo, 10 kuti mukhoza kuzindikira chabwino koposa zonse ndi chiti kuti muthe kukhala wopanda chodetsa ndi wopanda chilema kufikira tsiku la Khristu. 11 Ndipo moyo wanu udzakhala odzazidwa ndi chipatso cha chilungamo chimene chimachokera mwa Yesu Khristu. Pakuti zimenezi zidzapereka ulemerero ndi matamando kwa Mulungu.

Maunyolo a Paulo Apititsa Mʼtsogolo Uthenga Wabwino

12 Tsopano abale, ndikufuna mudziwe kuti chimene chandichitikira ine chathandiza kwambiri kupititsa patsogolo Uthenga Wabwino. 13 Chotsatira chake nʼchakuti zadziwika bwino lomwe kwa onse amene ali ku nyumba yaufumu kuti ine ndili mʼmaunyolo chifukwa cha Khristu. 14 Moti chifukwa cha maunyolo angawa, abale ambiri alimbikitsidwa kuyankhula Mawu a Mulungu molimbika ndi mopanda mantha.

15 Nʼzoonadi kuti ena amalalikira Khristu chifukwa cha kaduka ndi mikangano, koma ena chifukwa cha zolinga zabwino. 16 Olalikira ndi zolinga zabwinowa amachita izi mwachikondi, podziwa kuti ine ndili muno chifukwa cha kuteteza Uthenga Wabwino. 17 Ena aja amalalikira Khristu modzikonda osati moona mtima namaganiza kuti kutero kubweretsa mavuto pamene ndili mʼmaunyolo. 18 Nanga kodi zimenezo zili ndi ntchito? Chofunika ndi chakuti Khristu alalikidwe, kaya ndi mwachinyengo kapena moona. Ndipo ndikukondwera chifukwa cha chimenechi.

Ndithu, ndidzapitirira kukondwera, 19 pakuti ndikudziwa kuti chifukwa cha mapemphero anu ndi thandizo lochokera kwa Mzimu wa Yesu Khristu, zimene zandionekera zidzathandiza kuti ndimasulidwe. 20 Ndili ndi chiyembekezo chonse kuti sindidzachita manyazi ndi pangʼono pomwe, koma ndidzakhala ndi chilimbikitso chokwanira kuti monga mwa nthawi zonse, tsopano Khristu adzakwezedwa mʼthupi langa kaya ndi mʼmoyo kapena mu imfa. 21 Pakuti kwa ine kukhala moyo ndi Khristu ndipo kufa ndi phindu. 22 Ngati nditi ndipitirire kukhala ndi moyo mʼthupi ndiye kuti kwa ine ndi kugwira ntchito yopindulitsa. Kodi ndisankhe chiyani? Sindikudziwa. 23 Ndathinidwa ndi zinthu ziwirizi: Ndikulakalaka kunyamuka kuti ndikakhale ndi Khristu, chimene ndi chinthu chabwino kwambiri. 24 Komanso nʼkofunika kwambiri kuti ndikhalebe mʼthupi chifukwa cha inu. 25 Ndili ndi chitsimikizo, ndikudziwa kuti ndidzakhala ndi moyo ndipo ndidzapitirira nanu kuti nonse mupite mʼtsogolo ndi kukhala ndi chimwemwe mu chikhulupiriro 26 kuti pokhala nanunso, kudzitamandira kwanu mwa Khristu Yesu kudzasefukire chifukwa cha ine.

Moyo Woyenerana ndi Uthenga Wabwino

27 Chilichonse chimene chingachitike, chachikulu nʼchakuti mukhale moyo ofanana ndi Uthenga Wabwino wa Khristu. Tsono ngati ndingabwere kudzakuonani kapena kumangomva za inu ndili kutali, ndidzadziwa kuti mwayima mwamphamvu mwa Mzimu mmodzi, kulimbika pamodzi ngati munthu mmodzi chifukwa cha chikhulupiriro cha Uthenga Wabwino 28 osachita mantha ndi pangʼono pomwe ndi amene akutsutsana nanu. Ichi ndi chizindikiro kwa iwo kuti adzawonongedwa, koma inu mudzapulumutsidwa ndi Mulungu. 29 Pakuti inu mwapatsidwa mwayi osati ongokhulupirira Khristu kokha, koma wakumva zowawa mʼmalo mwa Khristu. 30 Inunso mukudutsa mʼzowawa zomwe zija munaona ndikudutsamo inenso ndipo pano mukumva kuti ndikukumana nazobe.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.