Beginning
Hezekiya Mfumu ya Yuda
18 Mʼchaka chachitatu cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Hezekiya mwana wa Ahazi mfumu ya Yuda analowa ufumu. 2 Anakhala mfumu ali ndi zaka 25 ndipo analamulira mu Yerusalemu zaka 29. Amayi ake anali Abi, mwana wa Zekariya. 3 Iye anachita zolungama pamaso pa Yehova monga anachitira Davide kholo lake. 4 Anachotsa malo opembedzerako mafano, anaphwanya miyala yachipembedzo ndiponso anadula mafano a Asera. Iye anaphwanya njoka yamkuwa imene Mose anapanga, pakuti mpaka kufikira nthawi imeneyi Aisraeli amafukiza lubani kwa njoka imeneyi. (Imatchedwa Nehusitani).
5 Hezekiya anadalira Yehova Mulungu wa Israeli. Kotero panalibe wina wofanana naye pakati pa mafumu onse a Yuda, asanakhale mfumu kapena atakhala kale mfumu. 6 Iye anakangamira Yehova ndipo sanamusiye koma anasunga malamulo amene Yehova anapatsa Mose. 7 Ndipo Yehova anali naye ndipo kulikonse kumene anapita zinthu zinkamuyendera bwino. Iye anagalukira mfumu ya ku Asiriya ndipo sanayitumikirenso. 8 Iye anakantha Afilisti kuyambira ku nsanja ya alonda mpaka ku mzinda wotetezedwa. Anakafika mpaka ku Gaza ndi ku malire ake.
9 Mʼchaka chachinayi cha Mfumu Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chiwiri cha Hoseya mwana wa Ela mfumu ya Israeli, Salimenezeri, mfumu ya ku Asiriya anabwera kudzathira nkhondo mzinda wa Samariya ndi kuwuzinga 10 Asiriya analanda mzindawu patatha zaka zitatu. Choncho mzinda wa Samariya unalandidwa chaka chachisanu ndi chimodzi cha Hezekiya, chimene chinali chaka chachisanu ndi chinayi cha Hoseya mfumu ya Israeli. 11 Mfumu ya ku Asiriya inatenga Aisraeli kupita nawo ku ukapolo ku Asiriya ndipo anakawakhazika ku Hala, ku Habori pafupi ndi mtsinje wa Gozani ndi mʼmizinda ya Amedi. 12 Izi zinachitika chifukwa sanamvere zonena za Yehova Mulungu wawo, koma anaphwanya pangano lake ndi zonse zimene Mose mtumiki wa Yehova anawalamula. Iwo sanamvere malamulowo kapena kuwagwiritsa ntchito.
13 Mʼchaka chakhumi ndi chinayi cha ulamuliro wa Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anathira nkhondo mizinda yonse yotetezedwa ya Yuda, nayilanda. 14 Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya ku Asiriya ku Lakisi wonena kuti, “Ine ndalakwa. Chokani kuno ndipo ndidzakupatsani chilichonse chimene munene.” Mfumu ya ku Asiriya inalamula mfumu Hezekiya, mfumu ya Yuda, kuti azipereka makilogalamu a siliva okwana 3,000 ndi makilogalamu a golide 1,000. 15 Mfumu Hezekiya inapereka siliva yense amene anapezeka mʼNyumba ya Yehova ndi mʼnyumba zosungiramo chuma cha mfumu.
16 Nthawi imeneyi Hezekiya mfumu ya Yuda anakanganula golide amene anakuta zitseko ndi mphuthu za chipata cha Nyumba ya Yehova namupereka kwa mfumu ya ku Asiriya.
Senakeribu Aopseza Yerusalemu
17 Mfumu ya ku Asiriya inatuma Taritani, Rabusarisi ndi Rabusake pamodzi ndi gulu lalikulu la ankhondo, kwa Mfumu Hezekiya ku Yerusalemu kuchokera ku Lakisi. Iwo anafika ku Yerusalemu nakayima pafupi ndi ngalande ya madzi yochokera ku Dziwe Lakumtunda, pa msewu waukulu wopita ku malo a Munda wa Mmisiri Wochapa. 18 Iwo anayitana mfumu, ndipo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu mlembi wa zochitika anapita kwa anthuwo.
19 Ndipo Rabusake anawawuza kuti, “Kamuwuzeni Hezekiya kuti,
“ ‘Mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya ikunena kuti, ‘Kodi chikukulimbitsa mtima ndi chiyani?’ 20 Iwe ukuti uli ndi luso ndiponso mphamvu pa nkhondo, komatu ukuyankhula mawu opanda pake. Kodi tsono iwe ukudalira yani kuti undiwukire ine? 21 Taona tsono, iwe ukudalira Igupto, bango lothyokalo, limene limalasa mʼmanja mwa munthu ngati waliyesa ndodo yoyendera! Umo ndi mmene Farao mfumu ya ku Igupto imachitira aliyense amene akuyidalira.’ ” 22 Ndipo ngati ukunena kwa ine kuti, “Ife tikudalira Yehova Mulungu wathu.” Kodi si Mulungu yemweyo amene nyumba zake ndi maguwa ake Hezekiya anachotsa, nawuza anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu kuti, “Muzipembedza pa guwa lansembe ili mu Yerusalemu?”
23 “ ‘Ndipo tsopano bwera udzakambirane ndi mbuye wanga, mfumu ya ku Asiriya: ine ndidzakupatsa akavalo 2,000 ngati ungathe kupeza okwerapo! 24 Ungathe bwanji kugonjetsa ngakhale mmodzi mwa akazembe angʼonoangʼono a mbuye wanga, pamene ukudalira Igupto kuti akupatse magaleta ndi anthu okwera pa akavalo? 25 Kuwonjezera pamenepa, kodi ine ndabwera kudzathira nkhondo ndi kuwononga malo ano popanda chilolezo cha Yehova? Yehova mwini ndiye anandiwuza kuti ndidzathire nkhondo ndi kuwononga dziko lino.’ ”
26 Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya, Sebina ndi Yowa anawuza Rabusakeyo kuti, “Chonde yankhulani kwa atumiki anufe mʼChiaramu, popeza timachimva. Musayankhule nafe mu Chihebri kuopa kuti anthu onse amene ali pa khomapa angamve.”
27 Koma Rabusake anayankha kuti, “Kodi mbuye wanga wandituma kuti ndidzanene zinthu izi kwa mbuye wanu yekha ndi inu nokha basi? Ayi, komanso kwa anthu amene akhala pa khomawa. Iwowa adzadya chimbudzi chawo chomwe ndi kumwa mkodzo wawo womwe monga momwe mudzachitire inuyonso.”
28 Tsono Rabusake anayimirira nafuwula mu Chihebri kuti, “Imvani mawu a mfumu yayikulu, mfumu ya ku Asiriya! 29 Zimene mfumu ikunena ndi izi: ‘Musalole kuti Hezekiya akunamizeni. Iye sangakupulumutseni mʼdzanja langa. 30 Hezekiya asakukakamizeni kudalira Yehova ndi mawu akuti, ‘Ndithu, Yehova adzatipulumutsa; ndipo sadzapereka mzindawu mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya.’
31 “ ‘Musamumvere Hezekiya. Zimene mfumu ya ku Asiriya ikunena ndi izi: Pangani mtendere ndi ine ndipo mutuluke mu mzinda. Mukatero aliyense wa inu adzadya mphesa ndi nkhuyu za mʼmunda mwake ndiponso adzamwa madzi a mʼchitsime chake, 32 mpaka nditabwera kudzakutengani kupita ku dziko lofanana ndi lanuli, dziko la tirigu ndi vinyo watsopano, dziko la chakudya ndi minda ya mipesa, dziko la mitengo ya olivi ndi uchi. Sankhani moyo osati imfa!
“Musamvere zonena Hezekiya, pakuti iye akukusocheretsani ponena kuti, ‘Yehova adzatipulumutsa.’ 33 Kodi mulungu wa anthu a mtundu wina uliwonse wapulumutsapo dziko lake mʼdzanja la mfumu ya ku Asiriya? 34 Kodi ili kuti milungu ya Hamati ndi Aripadi? Ili kuti milungu ya Sefaravaimu, Hena ndi Ivani? Kodi inapulumutsa Samariya mʼdzanja langa? 35 Kodi ndi milungu iti mwa milungu yonse ya mayiko awa amene anapulumutsa dziko lake mʼdzanja langa? Nanga tsono Yehova adzapulumutsa Yerusalemu mʼdzanja langa motani?”
36 Koma anthu anakhala chete ndipo sanayankhepo kanthu, chifukwa mfumu inawalamula kuti, “Musayankhe.”
37 Pamenepo anthu atatu aja Eliyakimu, mwana wa Hilikiya amene ankayangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi Yowa mwana wa Asafu, mlembi wa zochitika anapita kwa Hezekiya atangʼamba zovala zawo ndipo anamuwuza Hezekiya zonse zimene anayankhula Rabusake uja.
Kupulumutsidwa kwa Yerusalemu
19 Mfumu Hezekiya atamva zimenezi, anangʼamba zovala zake navala chiguduli ndipo analowa mʼNyumba ya Yehova. 2 Iye anatuma Eliyakimu, woyangʼanira nyumba ya mfumu, Sebina mlembi wa bwalo ndi ansembe akuluakulu, onse atavala ziguduli, kwa mneneri Yesaya mwana wa Amozi. 3 Iwo anamuwuza kuti, “Hezekiya akunena kuti, ‘Lero ndi tsiku lamavuto, lachilango ndi lamanyazi. Ife lero tili ngati mayi woyembekezera amene pofika nthawi yoti achire akupezeka kuti alibe mphamvu zoberekera. 4 Mwina Yehova Mulungu wanu adzamva mawu onse a Rabusake amene mbuye wake, mfumu ya ku Asiriya anamutuma kudzanyoza Mulungu wamoyo, ndipo Mulunguyo adzamulanga chifukwa cha mawu amene Yehova Mulungu wanu wamva. Choncho pemphererani anthu otsala amene akanali ndi moyo.’ ”
5 Akuluakulu a Mfumu Hezekiya atafika kwa Yesaya, 6 Yesaya anawawuza kuti, “Kawuzeni mbuye wanu kuti, ‘Yehova akunena kuti: Usachite mantha ndi zimene wamva, mawu amene nthumwi za mfumu ya ku Asiriya zandinyoza nawo Ine. 7 Tamverani! Ine ndidzayika mwa mfumuyo mzimu wina kotero kuti akadzamva mphekesera ya nkhondo, adzabwerera ku dziko lake ndipo Ine ndidzachititsa kuti aphedwe ndi lupanga kwawo komweko.’ ”
8 Rabusake atamva kuti mfumu ya ku Asiriya yachoka ku Lakisi, iye anabwerera mʼmbuyo ndipo anakapeza mfumu ikuchita nkhondo ndi mzinda wa Libina.
9 Nthawi imeneyi Senakeribu analandira uthenga wakuti Tirihaka, mfumu ya ku Kusi, akubwera kudzachita naye nkhondo. Choncho iye anatumanso amithenga kwa Hezekiya ndi mawu awa: 10 “Kawuzeni Hezekiya mfumu ya Yuda kuti: Usalole kuti Mulungu amene ukumudalira akupusitse ponena kuti, ‘Yerusalemu sadzaperekedwa mʼmanja mwa mfumu ya ku Asiriya.’ 11 Ndithu iwe unamva chimene mafumu a Asiriya anachita ku mayiko ena onse, kuti anawawononga kotheratu. Ndipo kodi iwe nʼkupulumuka? 12 Kodi milungu ya mitundu imene makolo anga anayigonjetsa, milungu ya anthu a ku Gozani, Harani, Rezefi ndi Aedeni amene anali ku Teli Asara, inawapulumutsa? 13 Kodi mafumu a Hamati, Aripadi ndi mafumu a mizinda ya Sefaravaimu, Hena ndi Iva, ali kuti?”
Pemphero la Hezekiya
14 Hezekiya analandira kalata kwa amithenga aja nayiwerenga. Pomwepo anapita ku Nyumba ya Yehova nayika kalatayo pamaso pa Yehova. 15 Ndipo Hezekiya anapemphera kwa Yehova nati, “Inu Yehova Mulungu wa Israeli, Inu amene mumakhala pa Akerubi, Inu nokha ndinu Mulungu wolamulira maufumu onse a dziko lapansi. Inu munalenga kumwamba ndi dziko lapansi. 16 Inu Yehova, tcherani khutu lanu ndipo mumve Yehova tsekulani maso anu ndipo muone, imvani mawu onse amene Senakeribu watumiza kunyoza Inu Mulungu wamoyo.
17 “Inu Yehova, nʼzoonadi kuti mafumu a Asiriya anawononga mitundu iyi ndi mayiko awo. 18 Iwo anaponya milungu yawo pa moto ndi kuyiwononga pakuti sinali milungu koma mitengo ndi miyala chabe, yopangidwa ndi anthu. 19 Ndipo tsopano Inu Yehova Mulungu wathu, tipulumutseni ndithu mʼdzanja lake, kuti maufumu onse a dziko lapansi adziwe kuti Inu nokha, Inu Yehova, ndinu Mulungu.”
Yankho la Mulungu Kudzera mwa Yesaya
20 Ndipo Yesaya mwana wa Amozi anatumiza uthenga kwa Hezekiya wakuti, “Yehova Mulungu wa Israeli akuti, ‘Ndamva pemphero lako lonena za Senakeribu mfumu ya ku Asiriya.’ ” 21 Mawu amene Yehova wayankhula wotsutsana naye ndi awa:
“Namwali wa Ziyoni
akukunyoza ndi kukuseka iwe.
Mwana wamkazi wa Yerusalemu
akupukusa mutu wake kumbuyo kwako.
22 Kodi iweyo wanyoza ndi kuchitira chipongwe yani?
Kodi ndani amene wamufuwulira mawu ako
ndi kumuyangʼana monyada?
Wachitiratu izi Woyera wa Israeli!
23 Kudzera mwa amithenga ako
wonyoza Ambuye.
Ndipo wanena kuti,
‘Ndi magaleta ochuluka
ndinakwera mapiri ataliatali,
pa msonga za mapiri a Lebanoni.
Ndigwetsa mitengo yake ya mkungudza yayitali kwambiri,
mitengo yake ya payini yabwino kwambiri.
Ndalowanso mʼkati mwake mwenimweni,
mwa nkhalango yake yowirira kwambiri.
24 Ndakumba zitsime ku mayiko achilendo
ndipo ndinamwa madzi a kumeneko.
Ndi mapazi anga
ndawumitsa mitsinje yonse ya ku Igupto.’ ”
25 “ ‘Kodi sunamvepo?
Zimenezi ndinazikhazikitsa kalekale.
Ndinazikonzeratu masiku amakedzana;
tsopano ndachita kuti zichitikedi,
iwe kwako kunali kungosandutsa mizinda yotetezedwa
kukhala milu ya miyala.
26 Anthu a kumeneko ndi opanda mphamvu,
athedwa nzeru ndipo ali ndi manyazi.
Ali ngati mbewu za mʼmunda,
ngati udzu wanthete,
ali ngati udzu womera pa denga,
umene umawuma usanakule nʼkomwe.’ ”
27 “ ‘Koma Ine ndimadziwa kukhala kwako,
kutuluka kwako ndi kulowa kwako,
ndi mkwiyo wako pa Ine.
28 Chifukwa chakuti wandikwiyira
ndipo ndamva za mwano wako,
ndidzakola mphuno yako ndi mbedza
ndi kuyika chitsulo changa mʼkamwa mwako,
ndipo ndidzakubweza pokudzeretsa
njira yomwe unadzera pobwera.’
29 “Koma iwe Hezekiya, chizindikiro chako chidzakhala ichi:
“Chaka chino mudzadya tirigu wamphulumukwa,
ndipo chaka chamawa mudzadya tirigu wongodzimerera.
Koma chaka chachitatu mudzadzala ndi kukolola,
mudzawoka mphesa ndipo mudzadya zipatso zake.
30 Anthu a nyumba ya Yuda amene adzatsale
adzazika mizu ndi kubereka zipatso.
31 Pakuti ku Yerusalemu kudzachokera anthu otsala,
ndi ku phiri la Ziyoni kudzachokera gulu la anthu opulumuka.”
“Changu cha Yehova Wamphamvuzonse chidzachita zimenezi.
32 “Choncho chimene Yehova akunena za mfumu ya ku Asiriya ndi ichi:
“ ‘Iye sadzalowa mu mzinda umenewu
kapena kuponyamo muvi.
Sadzayandikira mzindawu ndi zishango zake
kapena kumanga nthumbira ya nkhondo.
33 Adzabwerera potsata njira imene anadzera pobwera;
sadzalowa mu mzinda umenewu,
akutero Yehova.
34 Ndidzateteza mzinda umenewu kuwupulumutsa,
chifukwa cha Ine mwini ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”
35 Usiku umenewo mngelo wa Yehova anapita ku misasa ya ku Asiriya ndi kupha ankhondo 185,000. Ndipo pamene anthu anadzuka mmawa, taonani, mitembo inali ngundangunda! 36 Choncho Senakeribu mfumu ya ku Asiriya anapasula misasa ndi kuchoka. Anabwerera ku Ninive nakakhala kumeneko.
37 Tsiku lina, pamene Senakeribu ankapembedza mʼnyumba ya Nisiroki mulungu wake, ana ake Adirameleki ndi Sarezeri anamupha ndi lupanga ndipo anathawira ku dziko la Ararati. Tsono Esrahadoni, mwana wake, analowa ufumu mʼmalo mwake.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.