Beginning
64 Inu Yehova, bwanji mukanangongʼamba mlengalenga ndi kutsika pansi,
kuti mapiri agwedezeke pamaso panu!
2 Monga momwe moto umatenthera tchire
ndiponso kuwiritsa madzi,
tsikani kuti adani anu adziwe dzina lanu,
ndiponso kuti mitundu ya anthu injenjemere pamaso panu.
3 Pakuti nthawi ina pamene munatsika munachita zinthu zoopsa zimene sitinaziyembekezere,
ndipo mapiri anagwedezeka pamaso panu.
4 Chikhalire palibe ndi mmodzi yemwe anamvapo
kapena kuona
Mulungu wina wonga Inu,
amene amachitira zinthu zotere amene amadikira pa Iye.
5 Inu mumabwera kudzathandiza onse amene amakondwera pochita zolungama,
amene amakumbukira njira zanu.
Koma Inu munakwiya,
ife tinapitiriza kuchimwa.
Kodi nanga tingapulumutsidwe bwanji?
6 Tonsefe takhala ngati anthu amene ndi odetsedwa,
ndipo ntchito zathu zili ngati sanza za msambo;
tonse tafota ngati tsamba,
ndipo machimo athu akutiwuluzira kutali ngati mphepo.
7 Palibe amene amapemphera kwa Inu
kutekeseka kuti apemphe chithandizo kwa Inu;
pakuti mwatifulatira
ndi kutisiya chifukwa cha machimo athu.
8 Komabe, Inu Yehova ndinu Atate athu.
Ife ndife chowumba, Inu ndinu wowumba;
ife tonse ndi ntchito ya manja anu.
9 Inu Yehova, musatikwiyire kopitirira muyeso
musakumbukire machimo athu mpaka muyaya.
Chonde, mutiganizire, ife tikupempha,
pakuti tonsefe ndi anthu anu.
10 Mizinda yanu yopatulika yasanduka chipululu;
ngakhaletu Ziyoni wasanduka chipululu, Yerusalemu ndi wamasiye.
11 Nyumba yanu yopatulika ndi yaulemu, kumene makolo athu ankakutamandani,
yatenthedwa ndi moto
ndipo malo onse amene tinkawakonda asanduka bwinja.
12 Inu Yehova, zonse zachitikazi, kodi mungokhala osatithandiza?
Kodi mudzapitirizabe kukhala chete ndi kutilangabe mopitirira muyeso?
Chiweruzo ndi Chipulumutso
65 “Ndinali wokonzeka kumva mapemphero a amene sankandipempha kanthu;
ndipo ndinalola kuti anthu amene ankandifunafuna kuti andipeze.
Kwa mtundu wa anthu umene sunkapempha chithandizo kwa Ine,
ndinati, ‘Ine ndili pano, Ine ndili pano.’
2 Tsiku lonse ndatambasulira manja anga
anthu owukira aja,
amene amachita zoyipa,
natsatira zokhumba zawo.
3 Ndatambasulira manja anga anthu aja amene nthawi zonse amandikwiyitsa
mopanda manyazi.
Iwo amapereka nsembe mʼminda
ndi kufukiza lubani pa maguwa ansembe a njerwa.
4 Amakatandala ku manda
ndipo amakachezera usiku wonse kumalo obisika.
Amadya nyama ya nkhumba,
ndipo mʼmiphika mwawo muli msunzi wa nyama yodetsedwa.
5 Amawuza ena kuti, ‘Khala patali usandiyandikire,
chifukwa ungatengere kupatulika kwanga!’
Ukali wanga pa anthu otere uli ngati utsi mphuno zanga,
ngati moto umene umayaka tsiku lonse.
6 “Taonani, ndatsimikiza kale mlandu ndi chilango chawo;
sindidzakhala chete koma ndidzawalanga kwathunthu
chifukwa cha machimo awo
7 ndi a makolo awo,”
akutero Yehova.
“Chifukwa anapereka nsembe zopsereza pa mapiri
ndi kundinyoza Ine pa zitunda zawo,
Ine ndidzawalanga kwathunthu potsata
zimene anachita kale.”
8 Yehova akuti,
“Pamene madzi akanapezeka mu phava la mphesa
ndipo anthu amati, ‘Musawononge phavalo,
popeza madzi ena abwino akanalimobe mʼphavalo,’
Inenso chifukwa cha mtumiki wanga;
sindidzawononga onse.
9 Ndidzatulutsa zidzukulu mʼbanja la Yakobo,
ndipo a banja la Yuda adzalandira mapiri anga ngati cholowa chawo.
Anthu anga osankhidwa adzalandira zimenezi,
ndipo atumiki anga adzakhala kumeneko.
10 Chigwa cha Saroni chidzakhala kodyetserako nkhosa,
ndipo chigwa cha Akori chidzakhala malo opumirako ngʼombe
kwa anthu anga ondifunafuna Ine.
11 “Koma inu amene mumasiya Yehova
ndi kuyiwala phiri langa lopatulika,
amene munamukonzera Gadi chakudya
ndi kuthirira Meni chakumwa,
12 ndidzakuperekani ku lupanga ngati nsembe,
ndipo nonse mudzaphedwa;
chifukwa simunayankhe pamene ndinakuyitanani,
ndinayankhula koma simunamvere.
Munachita zoyipa pamaso panga
ndipo munasankha kuchita zoyipa zomwe sindikondwera nazo.”
13 Nʼchifukwa chake Ambuye Yehova akuti,
“Atumiki anga adzadya,
koma inu mudzakhala ndi njala;
atumiki anga adzamwa,
koma inu mudzakhala ndi ludzu;
atumiki anga adzakondwa,
koma inu mudzakhala ndi manyazi.
14 Atumiki anga adzayimba
mosangalala,
koma inu mudzalira kwambiri
chifukwa chovutika mu mtima
ndipo mudzalira mofuwula chifukwa mudzamva kuwawa mu mtima.
15 Anthu anga osankhidwa
adzatchula dzina lanu potemberera.
Ambuye Yehova adzakuphani,
koma atumiki ake adzawapatsa dzina lina.
16 Aliyense wopempha dalitso mʼdzikomo
adzachita zimenezo kwa Mulungu woona;
ndipo aliyense wochita malumbiro mʼdzikomo
adzalumbira mwa Mulungu woona.
Pakuti mavuto akale adzayiwalika
ndipo adzachotsedwa pamaso panga.
Chilengedwe Chatsopano
17 “Taonani, ndikulenga
mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.
Zinthu zakale sizidzakumbukika,
zidzayiwalika kotheratu.
18 Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya
chifukwa cha zimene ndikulenga,
pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa
ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
19 Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu
ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.
Kumeneko sikudzamvekanso kulira
ndi mfuwu wodandaula.
20 “Ana sadzafa ali akhanda
ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.
Wamngʼono mwa iwo
adzafa ali ndi zaka 100.
Amene adzalephere kufika zaka 100
adzatengedwa kukhala
wotembereredwa.
21 Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,
adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
22 Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,
kapena kudzala ndi ena nʼkudya.
Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo
wautali ngati mitengo.
Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito
ya manja awo nthawi yayitali.
23 Sadzagwira ntchito pachabe
kapena kubereka ana kuti aone tsoka;
chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,
iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.
24 Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe.
Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.
25 Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi.
Mkango udzadya udzu monga ngʼombe,
koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka.
Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala
chinthu chopweteka kapena chowononga,”
akutero Yehova.
Chiweruzo ndi Chiyembekezo
66 Yehova akuti,
“Kumwamba ndi mpando wanga waufumu
ndipo dziko lapansi ndilo chopondapo mapazi anga.
Tsono nyumba ili kuti yomwe mundimangire,
ndipo malo ali kuti amene inu mungandikonzere kuti ndizipumuliramo?
2 Kodi si manja anga amene anapanga zinthu zonsezi,
motero zonsezi ndi zanga?”
Akutero Yehova.
“Koma munthu amene ndimakondwera naye ndi uyu:
amene ali wodzichepetsa ndi wosweka mtima,
ndipo amamvera mawu anga.
3 Koma aliyense amene amapereka nsembe ngʼombe yayimuna
amaphanso munthu,
ndipo aliyense amene amapereka mwana wankhosa,
amaphanso galu.
Aliyense amene amapereka nsembe chopereka cha chakudya
amaperekanso magazi a nkhumba.
Ndipo amene amafukiza lubani pa guwa lansembe la chikumbutso
amapembedzanso fano.
Popeza iwo asankha njira zawozawo,
ndiponso kusangalatsidwa ndi zonyansa zawo.
4 Inenso ndawasankhira chilango chowawa
ndipo ndidzabweretsa pa iwo zimene amaziopa zija.
Pakuti pamene ndinawayitana palibe amene anayankha,
pamene ndinayankhula palibe amene anatchera khutu.
Anachita zoyipa pamaso panga
ndi kusankha kuchita zimene zimandinyansa zija.”
5 Imvani mawu a Yehova,
inu amene mumanjenjemera ndi mawu ake:
“Abale anu amene amakudani,
ndi kukuchotsani pakati pawo chifukwa cha dzina langa, amanena kuti,
‘Yehova alemekezeke
kuti ife tione chimwemwe chanu!’
Koma ndi iwowo amene adzachite manyazi.
6 Imvani mfuwu mu mzinda,
imvani phokoso mʼNyumba ya Mulungu!
Limenelo ndi liwu la Yehova,
kulanga adani ake onse.
7 “Mzinda uli ngati amayi apakati amene asanayambe kumva zowawa
wachira kale;
asanayambe kumva ululu,
wabala kale mwana wamwamuna.
8 Ndani anamvapo zinthu zoterezi?
Ndani anazionapo zinthu zoterezi?
Kodi dziko nʼkupangika tsiku limodzi,
kapena mtundu wa anthu nʼkubadwa tsiku limodzi?
Komatu Ziyoni atangoyamba kumva zowawa
nthawi yomweyo anabereka ana ake.
9 Kodi Ine ndingangofikitsa amayi apakati mpaka nthawi yake yochira,
koma osalola kuti abaledi mwana?” akutero Yehova.
“Kodi ndingatseke mimba
pa nthawi yoti abeleke?” akutero Mulungu wako.
10 “Kondwera nayeni Yerusalemu ndipo musangalale chifukwa cha Iye,
inu nonse amene mumakonda Yerusalemu,
kondwera nayeni kwambiri,
nonse amene mumamulira.
11 Pakuti mudzagawana naye ulemerero wake
ngati kuyamwa ndi kukhuta mkaka wambiri
wa mʼmawere
a chitonthozo chake.”
12 Yehova akuti,
“Ndidzamupatsa mtendere ngati mtsinje wa madzi,
ndiponso chuma cha anthu a mitundu ina ngati mtsinje wosefukira.
Mudzakhala ngati mwana woyamwa amene amayi ake amunyamulira pambalipa,
kapena kumufungata pa miyendo yake.
13 Monga momwe amayi amasangalatsira mwana wawo,
moteronso Ine ndidzakusangalatsani;
ndipo mudzasangalala chifukwa cha Yerusalemu.”
14 Mukadzaona zimenezi mitima yanu idzakondwera. Mudzabiriwira ngati udzu.
Zimenezi zidzakulimbikitsani ndi kukupatsani moyo wamphamvu.
Mudzadziwa kuti ndimathandiza amene amanditumikira
ndi kuti ndimakwiyira adani anga.
15 Taonani, Yehova akubwera ngati moto,
ndipo magaleta ake ali ngati kamvuluvulu;
Iye adzaonetsa mkwiyo wake nadzalanga adani ake
ndi malawi amoto.
16 Pakuti Yehova adzalanga anthu onse
ndi moto ndi lupanga,
Yehova adzapha anthu ambiri.
17 Yehova akuti, “Amene amadzipatula ndi kudziyeretsa okha kuti apite ku minda, ali ndi mtsogoleri awo, nʼkumadya nyama ya nkhumba, mbewa ndi zinthu zina zonyansa, onsewa adzafera limodzi.”
18 “Ndipo Ine, chifukwa cha zochita zawo ndi maganizo awo, ndili pafupi kubwera kudzasonkhanitsa mitundu yonse ya anthu ndi ziyankhulo zonse. Iwo adzabwera ndi kuona ulemerero wanga.
19 “Ndidzayika chizindikiro pakati pawo, ndipo ndidzatumiza ena mwa iwowa amene anapulumuka kuti apite kwa anthu a mitundu ina inu ku Tarisisi, ku Libiya ndi ku Ludi (akatswiri a mauta) ku Tubala ndi Grisi, ndi ku mayiko akutali a mbali mwa nyanja amene sanamvepo za mbiri yanga kapena kuona ulemerero wanga. Iwo adzalalika za ulemerero wanga pakati pa anthu a mitundu ina. 20 Ndipo adzabwera nawo abale anu onse ngati mphatso yopereka kwa Yehova kuchokera kwa anthu a mitundu yonse. Iwo adzakwera nawo kupita ku Yerusalemu, phiri langa loyera ku Yerusalemu monga nsembe kwa Yehova, atakwera akavalo, magaleta ndi ngolo, ndi pa abulu ndi ngamira,” akutero Yehova. “Adzabwera nawo ngati momwe Aisraeli amabwerera ndi zopereka zachakudya ku Nyumba ya Yehova mu ziwiya zoyeretsedwa monga mwa mwambo. 21 Ndipo ndidzasankha ena mwa iwonso kukhala ansembe ndi Alevi,” akutero Yehova.
22 “Monga momwe mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano zimene ndidzapanga zidzakhala mpaka muyaya pamaso panga, ndi chonchonso dzina lanu ndi zidzukulu zanu zidzakhalire.” Akutero Yehova. 23 “Anthu a mitundu yonse adzabwera kudzandipembedza ku Yerusalemu, pa chikondwerero chilichonse cha pokhala pa mwezi watsopano ndi tsiku la Sabata lililonse,” akutero Yehova. 24 “Akamachoka adzaona mitembo ya anthu amene anandiwukira Ine. Mphutsi zawo sizidzafa, kapena moto wawo sudzazimitsidwa. Anthu a mitundu ina yonse powaona adzanyansidwa nawo.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.