Old/New Testament
Kaini ndi Abele
4 Adamu anagona malo amodzi ndi Hava mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Kaini, ndipo anati, “Ndi thandizo la Yehova ndapeza mwana wamwamuna.” 2 Kenaka anabereka mʼbale wake Abele.
Abele anali woweta nkhosa ndipo Kaini anali mlimi. 3 Patapita nthawi, Kaini anatenga zipatso za ku munda nakazipereka kwa Yehova monga nsembe. 4 Nayenso Abele anatenga ana ankhosa oyamba kubadwa pamodzi ndi mafuta ake nakazipereka ngati nsembe kwa Yehova. Yehova anakondwera ndi Abele ndi nsembe yake. 5 Koma sanakondwere ndi Kaini ndi nsembe yake. Kotero Kaini anakwiya kwambiri ndipo nkhope yake inagwa.
6 Choncho Yehova anati kwa Kaini, “Chifukwa chiyani wakwiya ndipo bwanji nkhope yako yagwa? 7 Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”
8 Tsiku lina Kaini anati kwa mʼbale wake Abele, “Tiye tipite ku munda.” Ndipo ali ku mundako, Kaini anawukira mʼbale wake namupha.
9 Ndipo Yehova anamufunsa Kaini kuti, “Ali kuti mʼbale wako Abele?”
Iye anayankha kuti, “Sindikudziwa. Kodi ine ndine wosunga mʼbale wanga?”
10 Yehova anati, “Kodi wachita chiyani? Tamvera! Magazi a mʼbale wako akulirira kwa Ine kuchokera mʼnthaka. 11 Ndipo tsopano ndiwe wotembereredwa ndipo wachotsedwa mʼdziko limene nthaka yake inatsekula pakamwa pake kulandira magazi a mʼbale wako amene unakhetsa. 12 Udzalima munda koma nthakayo sidzakupatsanso zokolola zake. Udzakhala wosakhazikika; womangoyendayenda pa dziko lapansi.”
13 Kaini anati kwa Yehova, “Chilango changa ndi chachikulu kuposera mphamvu zanga. 14 Lero mukundipirikitsa pa dziko ndi pamaso panu; ndidzakhala wosakhazikika, woyendayenda, ndipo aliyense amene adzandipeze adzandipha.”
15 Koma Yehova anamuwuza kuti, “Sizidzatero ayi; aliyense amene adzaphe Kaini adzalangidwa ndi kulipiritsidwa kasanu ndi kawiri.” Pamenepo Yehova anayika chizindikiro pa Kaini kuti aliyense womupeza asamuphe. 16 Ndipo Kaini anachoka pamaso pa Yehova nakakhala ku dziko la Nodi, kummawa kwa Edeni.
Banja la Kaini
17 Kaini anagona malo amodzi ndi mkazi wake ndipo mkaziyo anakhala woyembekezera nabala Enoki. Kaini nthawi imeneyo nʼkuti akumanga mzinda ndipo anawutcha dzina la mwana wake Enoki. 18 Enoki anabereka Iradi; Iradi anabereka Mehuyaeli, ndipo Mehuyaeli anabereka Metusela, ndipo Metusela anabereka Lameki.
19 Lameki anakwatira akazi awiri, wina dzina lake linali Ada ndi winayo dzina lake linali Zila. 20 Ada anabereka Yabala; iyeyu anali kholo la onse okhala mʼmatenti ndi oweta ziweto. 21 Dzina la mʼbale wake linali Yubala; iyeyu anali kholo la onse oyimba zeze ndi chitoliro. 22 Zila nayenso anali ndi mwana wamwamuna, dzina lake Tubala-Kaini. Iyeyu anali kholo la amisiri onse osula zida za mkuwa ndi chitsulo. Mlongo wake wa Tubala-Kaini anali Naama.
23 Lameki anawuza akazi akewo kuti,
“Ada ndi Zila, ndimvereni;
inu akazi anga imvani mawu anga.
Ine ndinapha munthu chifukwa anandipweteka.
Ndinapha mnyamatayo chifukwa anandimenya.
24 Ngati wopha Kaini amulipsira kasanu nʼkawiri,
ndiye kuti wopha ine Lameki adzamulipsira kokwanira 77.”
25 Adamu anagonanso malo amodzi ndi mkazi wake, ndipo anabereka mwana wamwamuna namutcha Seti, kutanthauza kuti, “Mulungu wandipatsa mwana wina mʼmalo mwa Abele, popeza Kaini anamupha.” 26 Seti naye anali ndi mwana wa mwamuna, ndipo anamutcha Enosi.
Pa nthawi imeneyi anthu anayamba kupemphera mʼdzina la Yehova.
Mibado Kuyambira pa Adamu Mpaka Nowa
5 Ndondomeko ya mibado ya Adamu ndi iyi:
Pamene Mulungu analenga munthu, anamulenga mʼchifaniziro cha Mulungu. 2 Iye analenga mwamuna ndi mkazi. Anawadalitsa ndipo anawatcha “Munthu.”
3 Pamene Adamu anali ndi zaka 130, anabereka mwana wamwamuna wofanana naye ndipo anamutcha Seti. 4 Atabadwa Seti, Adamu anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 5 Zaka zonse za Adamu zinali 930 ndipo anamwalira.
6 Pamene Seti anali ndi zaka 105, anabereka Enosi. 7 Atabadwa Enosi, Seti anakhala ndi moyo zaka zina 807 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 8 Zaka zonse za Seti zinali 912 ndipo anamwalira.
9 Pamene Enosi anali ndi zaka 90, anabereka Kenani. 10 Atabadwa Kenani, Enosi anakhala ndi moyo zaka zina 815 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 11 Zaka zonse za Enosi pamodzi zinali 905 ndipo anamwalira.
12 Pamene Kenani anali ndi zaka 70, anabereka Mahalaleli. 13 Atabadwa Mahalaleli, Kenani anakhala ndi moyo zaka zina 840 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 14 Zaka zonse za Kenani zinali 910, ndipo anamwalira.
15 Pamene Mahalaleli anali ndi zaka 65, anabereka Yaredi. 16 Atabadwa Yaredi, Mahalaleli anakhala ndi moyo zaka zina 830 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 17 Zaka zonse za Mahalaleli zinali 895 ndipo anamwalira.
18 Pamene Yaredi anali ndi zaka 162, anabereka Enoki. 19 Atabadwa Enoki, Yaredi anakhala ndi moyo zaka zina 800 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 20 Zaka zonse za Yaredi zinali 962 ndipo anamwalira.
21 Pamene Enoki anali ndi zaka 65, anabereka Metusela. 22 Atabadwa Metusela, Enoki anayenda ndi Mulungu zaka 300 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 23 Zaka zonse za Enoki zinali 365. 24 Enoki anayenda ndi Mulungu; ndipo iye sanaonekenso chifukwa Mulungu anamutenga.
25 Pamene Metusela anali ndi zaka 187, anabereka Lameki. 26 Ndipo atabadwa Lameki, Metusela anakhala ndi moyo zaka zina 782 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 27 Zaka zonse za Metusela zinali 969, ndipo anamwalira.
28 Pamene Lameki anali ndi zaka 182, anabereka mwana wamwamuna. 29 Ndipo anamutcha Nowa ndipo anati, “Iyeyu adzatipumulitsa ku ntchito zathu zolemetsazi, zolima nthaka imene Yehova anayitemberera.” 30 Atabadwa Nowa, Lameki anakhala zaka zina 595 ndipo anabereka ana ena aamuna ndi aakazi. 31 Zaka zonse za Lameki zinali 777, ndipo kenaka anamwalira.
32 Pamene Nowa anali ndi zaka 500, anabereka Semu, Hamu ndi Yafeti.
Kuyipa kwa Mtundu wa Anthu
6 Anthu atayamba kuchuluka pa dziko lapansi ndi kubereka ana aakazi, 2 ana aamuna a Mulungu anaona kuti ana aakazi a anthuwo anali okongola. Ndipo anakwatira aliyense amene anamusankha. 3 Tsono Yehova anati, “Sindilola kuti chipwirikiti chikuchitikachi chipitirire mpaka muyaya, pakuti iye ndi munthu; masiku a moyo wake adzakhala zaka 120.”
4 Masiku amenewo komanso pambuyo pake, pa dziko lapansi panali Anefili, anthu amphamvu ndiponso otchuka. Anthuwa ndi amene ankabadwa ana a Mulungu aja atakwatira ana aakazi a anthu.
5 Pamene Yehova anaona kuti kuyipa kwa munthu pa dziko lapansi kunali kwakukulu ndi kuti nthawi zonse amalingalira ndi kukhumbira kuchita zoyipa zokhazokha, 6 Yehova anamva chisoni kuti analenga munthu ndi kumuyika pa dziko lapansi, ndipo anawawidwa mtima. 7 Choncho Yehova anati, “Ndidzafafaniza munthu, nyama, zonse zokwawa, ndi mbalame za mu mlengalenga pa dziko lapansi, pakuti ndikumva chisoni kuti ndinazilenga zimenezi.” 8 Koma Yehova anamukomera mtima Nowa.
Nowa ndi Chigumula
9 Mbiri ya Nowa inali yotere:
Nowa anali munthu wolungama ndi wopanda tchimo pakati pa anthu a mʼbado wake. Ndipo anayenda ndi Mulungu. 10 Nowa anabereka ana aamuna atatu: Semu, Hamu ndi Yafeti.
11 Chiwawa chinadzaza pa dziko lapansi kotero kuti dziko linakhala lowonongeka pamaso pa Mulungu. 12 Mulungu atayangʼana, anaona kuti dziko layipadi chifukwa cha makhalidwe oyipa a anthu onse pa dziko lapansi. 13 Ndipo Mulungu anati kwa Nowa, “Ndatsimikiza mtima kuti ndiwononge anthu onse, pakuti dziko lapansi ladzaza ndi ntchito zawo zoyipa. Ndithudi ndiwawononga pamodzi ndi zonse za pa dziko. 14 Tsono udzipangire chombo cha matabwa a mtengo wanjale; mʼkati mwake upange zipinda ndipo upake phula mʼkati ndi kunja. 15 Uchipange motere: Chombo chikhale mamita 140 mulitali, mamita 23 mulifupi ndi mamita 13 mu msinkhu wake. 16 Uchipangire denga ndi kuchimaliza ndi zenera la masentimita makumi asanu. Uyike khomo mʼmbali mwa chombocho ndi kupanga zipinda zosanjikana; chapansi, chapakati ndi chapamwamba. 17 Ndidzagwetsa mvula ya chigumula pa dziko lapansi kuti ndiwononge zamoyo zonse za pansi pa thambo ndipo chilichonse cha pa dziko lapansi chidzafa. 18 Koma ndidzachita pangano langa ndi iwe. Iwe, ana ako aamuna, mkazi wako ndi akazi a ana ako nonse mudzalowa mʼchombocho. 19 Iwe udzalowa mʼchombocho ndi zolengedwa zamoyo zonse ziwiriziwiri, chachimuna ndi chachikazi, kuti zisungike ndi moyo pamodzi ndi iwe. 20 Udzatenga ziwiriziwiri za mitundu yonse ya mbalame, mitundu yonse ya nyama, ndi mitundu yonse ya zokwawa kuti zikhale ndi moyo. 21 Udzatengenso chakudya cha mtundu uliwonse ndi kuchisunga kuti inu ndi nyamazo muzidzadya.”
22 Nowa anachita zonse monga Mulungu anamulamulira.
Anzeru a Kummawa
2 Atabadwa Yesu mʼBetelehemu wa ku Yudeya, mʼnthawi ya mfumu Herode, Anzeru a kummawa anabwera ku Yerusalemu 2 nafunsa kuti, “Ali kuti amene wabadwa kukhala mfumu ya Ayuda? Chifukwa tinaona nyenyezi yake kummawa ndipo tabwera kudzamupembedza.”
3 Mfumu Herode atamva zimenezi, anavutika mu mtima kwambiri pamodzi ndi anthu onse a mu Yerusalemu. 4 Ndipo anayitanitsa anthu onse, akulu ansembe ndi aphunzitsi amalamulo nawafunsa kuti, “Kodi Khristu adzabadwira kuti?” 5 Ndipo anamuyankha kuti, “Ku Betelehemu wa ku Yudeya chifukwa izi ndi zimene mneneri analemba kuti,
6 “ ‘Koma iwe Betelehemu, chigawo cha Yudeya,
sindiwe wamngʼonongʼono mwa olamulira a Yudeya;
pakuti otsogolera adzachokera mwa iwe,
amene adzaweta anthu anga Aisraeli.’ ”
7 Pomwepo Herode anawayitanira mseri Anzeruwo nawafunsitsa nthawi yeniyeni yomwe nyenyeziyo inaoneka. 8 Ndipo anawatumiza ku Betelehemu nawawuza kuti, “Pitani mukafufuze za mwanayo mosamalitsa. Ndipo mukamupeza mudzandiwuze kuti inenso ndikamupembedze.”
9 Atamva mawu a mfumu, ananyamuka ulendo wawo, ndipo taonani nyenyezi anayiona kummawa ija, inawatsogolera mpaka inayima pamwamba pa nyumba yomwe munali mwanayo. 10 Pamene iwo anaona nyenyeziyo, anasangalala kwambiri. 11 Pofika ku nyumbayo, anaona mwanayo pamodzi ndi amayi ake Mariya, ndipo anagwada namulambira Iye. Pomwepo anamasula chuma chawo ndi kupereka mphatso zawo za ndalama zagolide, lubani ndi mure. 12 Ndipo atachenjezedwa mʼmaloto kuti asapitenso kwa Herode, anabwerera ku dziko la kwawo podzera njira ina.
Athawira ku Igupto
13 Atachoka, taonani mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto nati, “Tadzuka, tenga mwanayo pamodzi ndi amayi ake ndipo muthawire ku Igupto. Mukakhale kumeneko mpaka nditakuwuza pakuti Herode adzafunafuna mwanayo kuti amuphe.” 14 Atadzuka, Yosefe anatenga mwanayo ndi amayi ake usiku omwewo napita ku Igupto, 15 nakhala kumeneko mpaka Herode atamwalira. Ndipo zinakwaniritsidwa zomwe ananena Ambuye mwa mneneri kuti, “Ndinayitana mwana wanga kuti atuluke mu Igupto.”
Kuphedwa kwa Ana mʼBetelehemu
16 Herode atazindikira kuti Anzeruwo anamupusitsa, anakwiya kwambiri. Ndipo anatumiza anthu kukapha ana onse aamuna a mʼBetelehemu ndi midzi yozungulira amene anali a zaka ziwiri kapena zocheperapo, molingana ndi nthawi imene Anzeruwo anamuwuza. 17 Pamenepo, zimene ananena mneneri Yeremiya zinakwaniritsidwa:
18 “Kulira kukumveka ku Rama,
kubuma ndi kulira kwakukulu,
Rakele akulirira ana ake;
sakutonthozeka,
chifukwa ana akewo palibe.”
Abwerera ku Nazareti
19 Atamwalira Herode, mngelo wa Ambuye anaonekera kwa Yosefe mʼmaloto ku Igupto 20 nanena kuti, “Nyamuka, tenga mwanayo ndi amayi ake ndipo mupite ku dziko la Israeli, popeza amene anafuna moyo wa mwanayo anamwalira.”
21 Tsono Yosefe atadzuka anatenga mwanayo ndi amayi ake kupita ku dziko la Israeli. 22 Koma atamva kuti Arikelao akulamulira mu Yudeya mʼmalo mwa abambo ake, Herode, anaopa kupitako. Atachenjezedwa mʼmaloto, anapita ku Galileya, 23 ndipo anakakhazikika mu mzinda wa Nazareti. Pamenepo zinakwaniritsidwa zonenedwa ndi aneneri kuti, “Adzatchedwa Mnazareti.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.