Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

New Testament in a Year

Read the New Testament from start to finish, from Matthew to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Mateyu 13:31-58

Fanizo la Mbewu ya Mpiru ndi Yisiti

31 Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. 32 Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”

33 Iye anawawuzanso fanizo lina nati: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma.”

34 Yesu anayankhula zinthu zonsezi kwa gulu la anthu mʼmafanizo ndipo Iye sananene kalikonse kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. 35 Kotero zinakwaniritsidwa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri kuti,

“Ndidzatsekula pakamwa panga ndi mafanizo,
    ndidzawulula zinthu zobisika
    chiyambire kukhazikidwa kwa dziko lapansi.”

Yesu Awatanthauzira Fanizo la Namsongole

36 Kenaka Iye anasiya gulu la anthu ndi kukalowa mʼnyumba. Ophunzira ake anapita kwa Iye nati, “Timasulireni fanizo la namsongole mʼmunda.”

37 Iye anayankha nati, “Munthu amene anafesa mbewu yabwino ndi Mwana wa Munthu. 38 Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo. 39 Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo.

40 “Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. 41 Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa. 42 Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano. 43 Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate awo. Amene ali ndi makutu amve.”

Fanizo la Chuma Chobisika ndi la Ngale

44 “Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.

45 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. 46 Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.”

Fanizo la Khoka

47 “Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba. 48 Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya. 49 Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. 50 Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

51 Yesu anawafunsa kuti, “Kodi mwamvetsetsa zonsezi?”

Iwo anayankha kuti, “Inde.”

52 Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”

Amupeputsa Yesu ku Nazareti

53 Yesu atatsiriza mafanizowa anachoka kumeneko. 54 Atafika ku mudzi kwawo anayamba kuphunzitsa mʼmasunagoge awo ndipo iwo anadabwa nati, “Munthu uyu anayitenga kuti nzeru iyi ndi mphamvu zodabwitsazi? 55 Kodi si mwana wa wopala matabwa? Kodi dzina la amayi ake si Mariya ndipo kodi abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? 56 Kodi alongo ake onse sali ndi ife? Tsono ndi kuti kumene anazitenga zinthu izi?” 57 Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye.

Koma Yesu anawawuza kuti, “Mneneri sapatsidwa ulemu ku mudzi kwawo ndi ku nyumba kwawo.”

58 Ndipo Iye sanachite zodabwitsa zambiri kumeneko chifukwa cha kusowa kwa chikhulupiriro kwawo.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.