The Daily Audio Bible
Today's audio is from the NLT. Switch to the NLT to read along with the audio.
Davide ndi Mefiboseti
9 Davide anafunsa kuti, “Kodi alipo amene watsala mʼbanja la Sauli kuti ndimuchitire chifundo chifukwa cha Yonatani?”
2 Tsono panali mtumiki wina wa banja la Sauli wotchedwa Ziba. Iwo anamuyitana kuti aonekere pamaso pa Davide, ndipo mfumu inamufunsa kuti, “Kodi ndiwe Ziba?”
Iyeyo anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”
3 Mfumu inafunsa kuti, “Kodi palibe amene watsala wa banja la Sauli amene ndingamuchitire chifundo cha Mulungu?”
Ziba anayankha mfumu kuti, “Alipo mwana wa Yonatani, koma ndi wolumala mapazi ake onse.”
4 Mfumu inafunsa kuti, “Ali kuti?”
Ziba anayankha kuti, “Iye ali ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli ku Lodebara.”
5 Kotero mfumu inamubweretsa kuchokera ku Lodebara, ku nyumba ya Makiri mwana wa Amieli.
6 Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli atafika kwa Davide, anawerama pansi kupereka ulemu kwa iye.
Davide anati, “Mefiboseti!”
Iye anayankha kuti, “Ine mtumiki wanu.”
7 Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.”
8 Mefiboseti anawerama pansi ndipo anati, “Mtumiki wanu ndine yani kuti musamale galu wakufa ngati ine?”
9 Kenaka Davide anayitanitsa Ziba, mtumiki wa Sauli, ndipo anati, “Ine ndapereka kwa chidzukulu cha mbuye wako chilichonse chimene chinali cha Sauli ndi banja lake. 10 Iwe ndi ana ndi antchito anu muzimulimira mʼdziko lake ndipo muzibweretsa zokololazo kuti chidzukulu cha mbuye wako chikhale ndi chakudya. Ndipo Mefiboseti, chidzukulu cha mbuye wako adzadya ndi ine nthawi zonse.” (Tsono Ziba anali ndi ana aamuna khumi ndi asanu ndi antchito makumi awiri).
11 Ndipo Ziba anati kwa mfumu, “Mtumiki wanu adzachita chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mudzalamulire wantchito wanu kuti achite.” Kotero Mefiboseti ankadya ndi Davide monga mmodzi wa ana a mfumu.
12 Mefiboseti anali ndi mwana wamngʼono wamwamuna wotchedwa Mika, ndipo onse a banja la Ziba anali antchito a Mefiboseti. 13 Ndipo Mefiboseti anakhala mu Yerusalemu chifukwa nthawi zonse amadya ndi mfumu. Iye anali wolumala mapazi ake onse.
Davide agonjetsa Aamoni
10 Patapita nthawi, mfumu ya Aamoni inamwalira, ndipo mwana wake Hanuni analowa ufumu mʼmalo mwake. 2 Davide anaganiza kuti, “Ine ndidzachitira chifundo Hanuni mwana wa Nahasi chifukwa abambo ake anandichitira zabwino.” Choncho Davide anatumiza anthu kuti akamupepesere kwa Hanuni chifukwa cha imfa ya abambo ake.
Anthu amene Davide anawatuma atafika kwa Hanuni mʼdziko la Aamoni, 3 atsogoleri a ankhondo a Aamoni anawuza Hanuni mbuye wawo kuti, “Kodi mukuganiza kuti Davide akupereka ulemu kwa abambo anu potumiza anthuwa kwa inu kudzapepesa? Kodi Davide sanawatumize anthuwa kuti adzaone mzinda wanu ndi kuchita ukazitape ndi cholinga chofuna kuwulanda?” 4 Choncho Hanuni anagwira anthu amene Davide anawatuma aja ndipo anameta munthu aliyense mbali imodzi ya ndevu zake, ndi kudula zovala zake pakati mʼchiwuno mpaka matako kuonekera, ndipo anawabweza kwawo.
5 Atamufotokozera Davide zimenezi, iye anatuma amithenga kukakumana ndi anthuwo chifukwa anali ndi manyazi kwambiri. Mfumu inati, “Mukhale ku Yeriko mpaka ndevu zanu zitakula, ndipo kenaka mubwere kuno.”
6 Aamoni atazindikira kuti amukwiyitsa kwambiri Davide, anakapeza ankhondo oyenda pansi aganyu okwanira 20,000 kuchokera ku Asiriya wa ku Beti Rehobu ndi Aramu-Zoba, komanso ankhondo 1,000 kwa mfumu Maaka ndiponso ankhondo 22,000 ochokera ku Tobu.
7 Davide atamva zimenezi, anatumiza Yowabu ndi gulu lonse la ankhondo amphamvu. 8 Aamoni anatuluka ndi kukhala mʼmizere ya nkhondo pa chipata cha mzinda wawo, pamene Aaramu a ku Aramu-Zoba ndi Rehobu ndi ankhondo a ku Tobu ndi Maaka anali kwa wokha ku malo wopanda mitengo.
9 Yowabu ataona kuti kunali mizere ya ankhondo kutsogolo kwake ndi kumbuyo kwake, iye anasankha ena mwa ankhondo a Israeli odziwa kuchita bwino nkhondo ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aaramu. 10 Iye anayika ankhondo ena otsalawo mʼmanja mwa Abisai mʼbale wake ndipo anawayika kuti amenyane ndi Aamoni. 11 Yowabu anati, “Ngati Aaramu andipose mphamvu, iwe ubwere udzandipulumutse. Koma ngati Aamoni akupose mphamvu, ine ndidzabwera kudzakupulumutsa. 12 Limba mtima ndipo timenyane nawo mopanda mantha chifukwa cha anthu athu ndi mizinda ya Mulungu wathu. Yehova achite chomukomera pamaso pake.”
13 Choncho Yowabu ndi ankhondo amene anali naye anapita kukamenyana ndi Aaramu, ndipo iwo anathawa pamaso pake. 14 Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai ndi kulowa mu mzinda. Nkhondo itatha, Yowabu anabwerera ku Yerusalemu.
15 Aaramu ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, anasonkhananso. 16 Hadadezeri anatumiza amithenga kukayitana Aaramu amene anali ku tsidya la Mtsinje, iwo anapita ku Helamu motsogozedwa ndi Sobaki mkulu wa ankhondo a Hadadezeri.
17 Davide atawuzidwa zimenezi, iye anasonkhanitsa Aisraeli onse ndi kuwoloka Yorodani ndipo anapita ku Helamu. Aaramu anayima mʼmizere yawo yankhondo kukakumana ndi Davide ndipo anamenyana naye. 18 Koma iwo anathawa pamaso pa Aisraeli, ndipo Davide anapha anthu okwera pa magaleta 700 ndi ankhondo oyenda pansi 40,000. Davide anaphanso Sobaki mtsogoleri wawo wankhondo ndipo anafera pomwepo. 19 Mafumu onse amene anali pansi pa Hadadezeri ataona kuti agonjetsedwa ndi Aisraeli, iwo anachita mtendere ndi Aisraeli ndipo anakhala pansi pawo.
Motero Aaramu anaopa kuthandizanso Aamoni.
Davide ndi Batiseba
11 Nthawi ya mphukira, nthawi imene mafumu amapita ku nkhondo, Davide anatumiza Yowabu ndi ankhondo a mfumu pamodzi ndi gulu lonse lankhondo la Aisraeli. Iwo anawononga Aamoni ndi kuzungulira mzinda wa Raba. Koma Davide anatsala ku Yerusalemu.
2 Tsiku lina cha kumadzulo Davide anadzuka pa bedi lake ndipo ankayenda pamwamba pa nyumba yake. Ali pa dengapo anaona mkazi akusamba. Mkaziyo anali wokongola kwambiri. 3 Ndipo Davide anatuma munthu wina kuti akafufuze za iye. Munthuyo anati, “Kodi uyu si Batiseba, mwana wa Eliamu, mkazi wa Uriya Mhiti?” 4 Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake. 5 Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.”
6 Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide. 7 Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera. 8 Kenaka Davide anati kwa Uriya, “Pita ku nyumba yako ukapumule.” Choncho Uriya anachoka ku nyumba yaufumu, ndipo mfumuyo inatumiza mphatso kwa Uriya. 9 Koma Uriya anagona pa chipata cha nyumba yaufumu pamodzi ndi antchito onse a mbuye wake ndipo sanapite ku nyumba yake.
10 Davide atawuzidwa kuti, “Uriya sanapite ku nyumba yake.” Iye anafunsa kuti, “Kodi iwe sunachokera kutali? Nʼchifukwa chiyani sunapite ku nyumba yako?”
11 Uriya anayankha Davide kuti, “Bokosi la Chipangano ndi Israeli ndiponso Yuda akukhala mʼmatenti, ndipo mbuye wanga Yowabu ndi ankhondo anu mbuye wanga amanga misasa pa mtetete. Ine ndingapite bwanji ku nyumba yanga kukadya ndi kumwa ndiponso kugona ndi mkazi wanga? Pali inu wamoyo, ine sindidzachita chinthu chimenechi.”
12 Ndipo Davide anati kwa iye, “Ukhale konkuno tsiku lina limodzi, ndipo mawa ndikulola kuti upite.” Kotero Uriya anakhala mu Yerusalemu tsiku limenelo ndi tsiku linalo. 13 Davide anayitana Uriya nadya ndi kumwa naye, ndipo Davide anamuledzeretsa. Koma madzulo Uriya anapita kukagona pa mphasa pamodzi ndi antchito a mbuye wake. Iye sanapite ku nyumba yake.
14 Mmawa Davide analemba kalata kwa Yowabu ndipo anayitumiza ndi Uriya. 15 Mʼkalatayo analembamo kuti, “Uriya mumuyike patsogolo penipeni, pamene pali nkhondo yoopsa. Ndipo mumusiye yekha kuti akanthidwe ndi kufa.”
16 Kotero Yowabu atawuzinga mzindawo, anamuyika Uriya pamalo pamene amadziwa kuti pali asilikali amphamvu. 17 Ankhondo a mu mzindawo atabwera kudzamenyana ndi Yowabu, anthu ena a gulu la ankhondo la Davide anaphedwa ndipo Uriya Mhiti uja anaphedwanso.
18 Yowabu anatumiza wamthenga kwa Davide kukafotokoza mwatsatanetsatane za nkhondoyo. 19 Iye anamulangiza wa mthengayo kuti, “Pamene ukatsiriza kufotokozera mfumu za ku nkhondozi, 20 mfumu ikapsa mtima, ndipo akakakufunsa kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani munapita pafupi ndi mzindawo kukamenya nkhondo? Inu simunadziwe kuti atha kukuponyerani mivi kuchokera pa khoma? 21 Kodi anapha Abimeleki mwana wa Yerubeseti ndani? Kodi mkazi sanamuponyere mphero kuchokera pa khoma? Kotero kuti anakafera ku Tebezi. Nʼchifukwa chiyani munafika pafupi ndi khoma?’ Ngati iye akafunsa zimenezi, iwe ukanene kwa iye kuti, ‘Mtumiki wanunso Uriya Mhiti wafa.’ ”
22 Mthengayo ananyamuka, ndipo atafika anamuwuza Davide zonse zimene Yowabu anamutuma kuti akanene. 23 Mthengayo anati kwa Davide, “Anthuwo anatiposa mphamvu ndipo anabwera kudzalimbana nafe poyera, koma ife tinawabwezera ku chipata cha mzindawo. 24 Ndipo anthu oponya mivi anatiponyera kuchokera pa khoma, anthu ena a mfumu afa. Kuwonjezera apo, mtumiki wanu Uriya Mhiti wafanso.”
25 Davide anamuwuza mthengayo kuti, “Ukanene izi kwa Yowabu: ‘Zimenezi zisakukhumudwitse; lupanga limapha wina nthawi zinanso wina. Limbikitsa nkhondo pa mzindawo ndipo uwuwononge!’ Ukanene zimenezi pomulimbikitsa Yowabu.”
26 Mkazi wa Uriya atamva kuti mwamuna wake wafa, analira maliro. 27 Nthawi yolira maliro itatha, Davide anamubweretsa ku nyumba yake, ndipo anakhala mkazi wake nabala mwana wamwamuna. Koma Yehova sanakondwe ndi zimene Davide anachitazo.
Mpesa ndi Nthambi
15 “Ine ndine mpesa weniweni, ndipo Atate anga ndiye mwini munda. 2 Iye amadula nthambi iliyonse ya mwa Ine imene sibala chipatso, koma nthambi iliyonse imene imabala chipatso amayisadzira bwino kuti ibale zipatso zambiri. 3 Inu ndinu oyera kale chifukwa cha mawu amene ndayankhula inu. 4 Khalani mwa Ine, monga Ine ndili mwa inu. Palibe nthambi imene ingabereke chipatso pa yokha ngati sinalumikizike ku mpesa. Chomwechonso inu simungathe kubereka chipatso pokhapokha mutakhala mwa Ine.
5 “Ine ndine mpesa; inu ndinu nthambi zake. Ngati munthu akhala mwa Ine ndi Ine mwa iye, adzabereka zipatso zambiri; popanda Ine simungathe kuchita kanthu. 6 Ngati wina aliyense sakhala mwa Ine, iyeyo ali ngati nthambi imene yatayidwa ndi kufota. Nthambi zotero zimatoledwa, kuponyedwa pa moto ndi kupsa. 7 Ngati inu mukhala mwa Ine ndipo mawu anga akhala mwa inu, pemphani chilichonse chimene mukufuna ndipo mudzapatsidwa. 8 Atate anga amalemekezedwa mukamabereka zipatso zochuluka, ndipo potero mudzionetsa kuti ndinu ophunzira anga.
9 “Monga momwe Atate amandikondera Ine, Inenso ndakukondani. Tsopano khalani mʼchikondi changa. 10 Ngati mumvera malamulo anga, mudzakhala mʼchikondi changa, monga Ine ndimamvera malamulo a Atate anga, ndipo ndimakhala mʼchikondi chawo. 11 Ine ndakuwuzani izi kuti chimwemwe changa chikhale mwa Inu, kuti chimwemwe chanu chikhale chokwanira. 12 Lamulo langa ndi ili: ‘Kondanani wina ndi mnzake monga Ine ndakonda inu.’ 13 Palibe munthu ali ndi chikondi choposa ichi, choti munthu nʼkutaya moyo wake chifukwa cha abwenzi ake. 14 Inu ndinu abwenzi anga ngati muchita zimene Ine ndikulamulani. 15 Ine sindikutchulaninso antchito, chifukwa wantchito sadziwa zimene bwana wake akuchita. Mʼmalo mwake Ine ndakutchani abwenzi pakuti zilizonse zimene ndinaphunzira kwa Atate, Ine ndakudziwitsani. 16 Inu simunandisankhe Ine, koma Ine ndinakusankhani kuti mupite ndi kukabereka zipatso, zipatso zake za nthawi yayitali. Choncho Atate adzakupatsani chilichonse chimene mudzapempha mʼdzina langa. 17 Lamulo langa ndi ili: ‘Muzikondana.’
Dziko Lapansi Limada Ophunzira a Yesu
18 “Ngati dziko lapansi lidana nanu, dziwani kuti linayamba kudana ndi Ine. 19 Inu mukanakhala anthu a dziko lapansi, dziko lapansi likanakukondani ngati anthu ake omwe. Koma mmene zilili, inu si anthu a dziko lapansi. Ine ndakusankhani kuchokera mʼdziko lapansi, nʼchifukwa chake dziko lapansi limakudani. 20 Kumbukirani mawu amene ndinayankhula nanu akuti, ‘Palibe wantchito amene amaposa bwana wake.’ Ngati anandizunza Ine, iwo adzakuzunzaninso inu. Ngati anamvera chiphunzitso changa, iwo adzamvera chanunso. 21 Iwo adzakuchitani zimenezi chifukwa cha dzina langa, popeza sakudziwa amene anandituma Ine. 22 Ine ndikanapanda kubwera ndi kuyankhula nawo, sakanakhala ndi mlandu. Koma tsopano alibe choti nʼkukanira mlandu wawo. 23 Iye amene amadana ndi Ine amadananso Atate anga. 24 Ine ndikanapanda kuchita pakati pawo zinthu zimene wina aliyense sanachitepo, iwo sakanakhala ochimwa. Koma tsopano aona zodabwitsa izi, komabe akundida Ine pamodzi ndi Atate anga. 25 Koma zatere kuti zikwaniritse zimene zinalembedwa mʼmalamulo awo: ‘Iwo anandida Ine popanda chifukwa.’
Ntchito ya Mzimu Woyera
26 “Nkhoswe ikadzabwera imene Ine ndidzakutumizireni kuchokera kwa Atate, ndiye Mzimu Woyera wachoonadi amene achokera kwa Atate, Iyeyo adzandichitira umboni Ine. 27 Inunso mudzandichitira umboni Ine, popeza mwakhala nane kuchokera pachiyambi.”
Zayini
49 Kumbukirani mawu anu kwa mtumiki wanu,
popeza mwandipatsa chiyembekezo.
50 Chitonthozo changa pa masautso anga ndi ichi:
lonjezo lanu limasunga moyo wanga.
51 Odzikuza amandinyoza popanda chowaletsa,
koma sindichoka pa malamulo anu.
52 Ndimakumbukira malamulo anu Yehova akalekale,
ndipo mwa iwo ndimapeza chitonthozo.
53 Ndayipidwa kwambiri chifukwa cha oyipa
amene ataya malamulo anu.
54 Zophunzitsa zanu ndi mitu ya nyimbo yanga
kulikonse kumene ndigonako.
55 Usiku ndimakumbukira dzina lanu Yehova,
ndipo ndidzasunga malamulo anu.
56 Ichi ndicho ndakhala ndikuchita:
ndimasunga malangizo anu.
Heti
57 Yehova, Inu ndiye gawo langa;
ndalonjeza kumvera mawu anu.
58 Ndimafunafuna nkhope yanu ndi mtima wanga wonse;
mundikomere mtima monga mwa lonjezo lanu.
59 Ndinalingalira za njira zanga
ndipo ndatembenuza mayendedwe anga kutsatira umboni wanu.
60 Ndidzafulumira ndipo sindidzazengereza
kumvera malamulo anu.
61 Ngakhale oyipa andimange ndi zingwe,
sindidzayiwala lamulo lanu.
62 Ndimadzuka pakati pa usiku kuyamika Inu
chifukwa cha malamulo anu olungama.
63 Ine ndine bwenzi la onse amene amakukondani,
kwa onse amene amatsatira malangizo anu.
64 Dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chanu chosasinthika,
phunzitseni malamulo anu.
16 Zolinga za mu mtima ndi za munthu,
koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.
2 Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake,
koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.
3 Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova,
ndipo zolinga zako zidzachitikadi.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.