Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Beginning

Read the Bible from start to finish, from Genesis to Revelation.
Duration: 365 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Eksodo 19-21

Pa Phiri la Sinai

19 Ana a Israeli aja anafika ku chipululu cha Sinai pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere mʼdziko la Igupto. Atachoka ku Refidimu, anafika ku Sinai, ndipo Aisraeli anamangako misasa yawo moyangʼanana ndi phirilo.

Mose anakwera ku phiri kukakumana ndi Mulungu ndipo Yehova anamuyitana nati, “Ukawuze zidzukulu za Yakobo, ana onse a Israeli kuti, ‘Inu eni munaona zimene ndinawachitira Aigupto ndiponso mmene ndinakunyamulirani, monga mmene chiwombankhanga chimanyamulira ana ake pa mapiko,’ ndikukubweretsani kwa Ine. Tsopano, ngati mumveradi mawu anga ndi kusunga pangano langa, mudzakhala chuma changa chapamtima pakati pa mitundu yonse. Ngakhale kuti dziko lonse lapansi ndi langa, inu mudzakhala ansembe achifumu ndi mtundu woyera mtima. Awa ndi mawu amene uyenera kuwawuza Aisraeli.”

Ndipo Mose anabwerera ndi kuyitanitsa akuluakulu. Atabwera anawafotokozera mawu amene Yehova anamulamulira kuti adzanene. Anthu onse anayankha pamodzi kuti, “Ife tidzachita zonse zimene Yehova wanena.” Choncho Mose anabweza yankho lawo kwa Yehova.

Yehova anati kwa Mose, “Ine ndibwera kwa iwe mu mtambo wakuda kuti anthu adzandimve ndikuyankhula ndi iwe. Choncho adzakukhulupirira nthawi zonse.” Kenaka Mose anawuza Yehova zimene anthu ananena.

10 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Pita kwa anthu onse ndi kuwayeretsa lero ndi mawa. Achape zovala zawo 11 ndipo akhale atakonzeka pofika tsiku lachitatu, chifukwa tsiku limenelo Yehova adzatsika pa phiri la Sinai anthu onse akuona. 12 Uwalembere malire anthuwo kuzungulira phirilo ndipo uwawuze kuti, ‘Samalani musakwere phirilo kapena kukhudza tsinde lake. Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndithu. 13 Aliyense wokhudza phiri adzaphedwa ndi miyala kapena kumulasa ndi mivi. Palibe amene adzamukhudze. Palibe munthu amene adzaloledwa kukhala ndi moyo ngakhale nyama. Iwo adzayenera kuphedwa.’ Koma anthu adzapita ku phirilo akadzamva kulira kwa lipenga la nyanga yankhosa.”

14 Tsono Mose anatsika phiri lija nafika kwa anthu aja ndi kuwayeretsa. Iwo anachapa zovala zawo. 15 Kenaka iye anati kwa anthu, “Konzekerani tsiku lachitatu, musagone pamodzi ndi mkazi.”

16 Mʼmamawa wa tsiku lachitatu kunali mabingu, ziphaliwali ndi mtambo wakuda umene unaphimba phiri, ndiponso lipenga lolira kwambiri. Aliyense ku misasa kuja ananjenjemera ndi mantha. 17 Ndipo Mose anatsogolera anthu kutuluka mʼmisasa kukakumana ndi Mulungu, ndipo anayima mʼmunsi mwa phiri. 18 Phiri la Sinai linakutidwa ndi utsi, chifukwa Yehova anatsika ndi moto pa phiripo. Utsi unakwera ngati wochokera mʼngʼanjo yamoto ndipo phiri lonse linagwedezeka kwambiri. 19 Liwu la lipenga linkakulirakulira. Tsono Mose anayankhula ndipo Yehova anamuyankha ndi mabingu.

20 Yehova anatsika nafika pamwamba pa phiri la Sinai, ndipo anayitana Mose kuti apite pa phiripo. Choncho Mose anakwera, 21 ndipo Yehova anati kwa iye, “Tsika ukawachenjeze anthu kuti asayesere kudutsa malire kuti adzandione chifukwa ambiri a iwo adzafa. 22 Ngakhale ansembe amene amatumikira pamaso pa Yehova ayenera kudziyeretsa kuopa kuti ndingadzawalange.”

23 Mose anati kwa Yehova, “Anthu sangakwere phiri la Sinai chifukwa inu munatichenjeza. Lembani malire kuzungulira phiri ndipo mulipatule kuti likhale loyera.”

24 Yehova anayankha, “Tsika ukamutenge Aaroni. Koma ansembe ndi anthu asayesere kubzola malire kuti abwere kwa Yehova chifukwa Iye adzawalanga.”

25 Ndipo Mose anatsika ndi kukawawuza anthuwo.

Malamulo Khumi

20 Ndipo Mulungu anayankhula mawu onse awa nati:

“Ine ndine Yehova Mulungu wako amene ndinakutulutsa ku Igupto, mʼdziko la ukapolo.

“Usakhale ndi milungu ina koma Ine ndekha.”

“Usadzipangire chofanizira chinthu chilichonse chakumwamba kapena cha pa dziko lapansi kapena cha mʼmadzi a pansi pa dziko. Usazigwadire kapena kuzipembedza, pakuti Ine Yehova Mulungu wako, ndine Mulungu wansanje, wolanga ana chifukwa cha tchimo la makolo awo mpaka mʼbado wachitatu ndi wachinayi wa iwo amene amadana nane. Koma ndimaonetsa chikondi chosasinthika ku mibado miyandamiyanda ya anthu amene amandikonda, ndi kusunga malamulo anga.

“Usagwiritse ntchito molakwika dzina la Yehova Mulungu wako, pakuti Yehova adzamutenga kukhala wochimwa aliyense amene akugwiritsa ntchito dzina lakelo molakwika.

“Uzisunga tsiku la Sabata kuti likhale lopatulika. Uzigwira ntchito zako zonse masiku asanu ndi limodzi. 10 Koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndi Sabata, tsiku loperekedwa kwa Yehova Mulungu wako. Tsiku limeneli musagwire ntchito iliyonse, inuyo kapena mwana wanu wamwamuna kapena mwana wanu wamkazi, wantchito wanu wamwamuna kapena mdzakazi wanu, ziweto zanu kapena mlendo amene akukhala mʼmudzi mwanu. 11 Pakuti Yehova anapanga kumwamba ndi dziko lapansi, nyanja ndi zonse zimene zili mʼmenemo mʼmasiku asanu ndi limodzi. Iye anapuma pa tsiku lachisanu ndi chiwiri. Kotero Yehova anadalitsa tsiku la Sabata kuti likhale loyera.

12 “Lemekeza abambo ako ndi amayi ako kuti ukhale ndi moyo wautali mʼdziko limene Yehova Mulungu wako akukupatsa.

13 “Usaphe.

14 “Usachite chigololo.

15 “Usabe.

16 “Usapereke umboni womunamizira mnzako.

17 “Usasirire nyumba ya mnzako. Usasirire mkazi wa mnzako kapena wantchito wake wamwamuna kapena mdzakazi wake, ngʼombe yake kapena bulu wake, kapena chilichonse cha mnzako.”

18 Pamene anthu ankamva mabingu ndi kuona ziphaliwali ndi kumvanso lipenga ndi kuona utsi umene umafuka mʼphiri, ananjenjemera ndi mantha. Ndipo iwo anayima patali. 19 Ndipo anati kwa Mose, “Iwe utiyankhule ndipo tidzamvera. Koma usalole kuti Mulungu atiyankhule, tingafe.”

20 Koma Mose anati kwa anthuwo, “Musachite mantha. Mulungu wabwera kudzakuyesani kuti mukhale ndi mtima woopa Mulungu kuti musamuchimwire.”

21 Anthu aja anayima patali koma Mose anayandikira mtambo wakuda kumene kunali Mulungu.

Za Mafano ndi Maguwa Ansembe

22 Ndipo Yehova anati kwa Mose, “Awuze izi Aisraeli: ‘Inu mwaona nokha kuti Ine ndakuyankhulani kuchokera kumwamba. 23 Choncho musadzipangire milungu yasiliva kapena yagolide kuti muziyipembedza pamodzi ndi Ine.’ ”

24 Mundimangire guwa ladothi ndipo muziperekapo nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe zanu. Pamalo paliponse pamene Ine ndidzakonza kuti muzinditamandirapo, ndidzabwera ndi kukudalitsani. 25 Ngati mudzandimangira guwa lansembe lamiyala, musagwiritse ntchito miyala yosema, pakuti mudzalidetsa mukadzagwiritsa ntchito zida. 26 Musamakwere pa makwerero popita pa guwa langa lansembe kuti mungaonetse maliseche anu.

21 “Uwawuze Aisraeli malamulo awa:

Antchito a Chihebri

“Mukagula kapolo wa Chihebri, azikugwirirani ntchito zaka zisanu ndi chimodzi. Koma mʼchaka cha chisanu ndi chiwiri muzimumasula, ndipo asalipire kanthu. Ngati anabwera yekha, amasulidwenso yekha. Koma ngati anali ndi mkazi pamene ankabwera, mkaziyo apite nayenso. Ngati bwana wake amupatsa mkazi ndipo mkaziyo anabereka ana aamuna kapena aakazi, mkazi ndi anawo adzakhala a bwanayo ndipo mwamuna yekhayo ndiye adzamasulidwe.

“Koma ngati kapoloyo alengeza kuti, ‘Ine sindikufuna kumasulidwa chifukwa ndimakonda mbuye wanga, mkazi wanga ndi ana,’ mbuye wakeyo abwere naye kwa Yehova. Abwere naye pa chitseko kapena pa mphuthu zachitseko ndipo abowole khutu lake ndi chitsulo. Ndipo iye adzakhala kapolo wake moyo wake wonse.

“Ngati munthu agulitsa mwana wake wamkazi kukhala mdzakazi, mwanayo asamasulidwe monga achitira ndi akapolo aamuna. Koma ngati mkaziyo sakukondweretsa bwana wake amene wamusankha kuti amukwatire, amulole kuti awomboledwe. Bwanayo alibe mphamvu zomugulitsa kwa anthu achilendo, chifukwa iyeyo waphwanya pangano lake lomukwatira iye. Ngati anamusankha kuti akhale mkazi wa mwana wake, ayenera kumusunga ngati mwana wake wamkazi. 10 Ngati akwatira mkazi wina, asamumane woyambayo chakudya ngakhale chovala ndipo apiritirize kugona naye ngati mkazi wake. 11 Koma ngati sangathe kumuchitira zonsezi, ndiye amuleke apite popanda kulipira kanthu.

Munthu Akapwetekedwa

12 “Munthu aliyense amene amenya mnzake namupha, iyenso ayenera kuphedwa. 13 Koma ngati sanachite dala, ndipo Mulungu analola kuti zichitike, iyeyo athawire ku malo kumene ndidzakupatsani. 14 Koma ngati munthu akonza chiwembu ndi kupha mnzake mwadala, ameneyo muchotseni ngakhale ku guwa langa lansembe ndipo aphedwe.

15 “Munthu aliyense amene amenya abambo ake kapena mayi ake ayenera kuphedwa.

16 “Munthu aliyense amene aba munthu mnzake, ndi kukamugulitsa, kapena kumangomusunga, ayenera kuphedwa.

17 “Aliyense amene atemberera abambo ake kapena amayi ake ayenera kuphedwa.

18 “Ngati anthu awiri akangana ndipo wina amenya mnzake ndi mwala kapena nkhonya koma wosamupha, womenyedwayo akadwala nagona pa bedi, 19 kenaka nachira ndi kuyamba kuyenda ndi ndodo kutuluka kunja kwa nyumba yake, ndiye kuti womenya mnzakeyo sadzayimbidwa mlandu. Komabe adzayenera kulipira womenyedwayo chifukwa cha nthawi imene anagona pa bedi ija, ndiponso ayenera kumusala mpaka atachiritsitsa.

20 “Ngati munthu amenya kapolo wake wamwamuna kapena mdzakazi ndi ndodo, kapolo uja ndikufa chifukwa cha kumenyedwako, munthuyo ayenera kulangidwa. 21 Koma ngati kapolo uja akhala ndi moyo tsiku lonse kapena masiku awiri, ndiye kuti mbuye uja asalangidwe chifukwa kapolo ndi chuma chake.

22 “Ngati anthu akumenyana ndi kupweteka mayi woyembekezera, mayiyo napita padera, koma osavulala, wolakwayo ayenera kulipira chilichonse chimene mwamuna wake wa mkaziyo adzalamula ndipo bwalo lamilandu lavomereza. 23 Koma ngati wavulazidwa kwambiri, ndiye malipiro ake adzakhala motere: moyo kulipa moyo, 24 diso kulipira diso, dzino kulipira dzino, mkono kulipa mkono, phazi kulipa phazi. 25 Kutentha ndi moto kulipa kutentha ndi moto, bala kulipa bala, mkwingwirima kulipa mkwingwirima.

26 “Ngati munthu amenya wantchito wake wa mwamuna kapena mdzakazi wake pa diso ndi kuliwononga, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a diso lake. 27 Ndipo ngati agulula dzino la wantchito wamwamuna kapena mdzakazi, wantchitoyo amasulidwe ngati malipiro a dzino lake.

28 “Ngati ngʼombe ipha munthu wamwamuna kapena wamkazi ndi nyanga yake, iponyedwe miyala ndipo nyama yake isadyedwe. Ndipo mwini ngʼombeyo asayimbidwe mlandu. 29 Koma ngati ngʼombeyo inali ndi chizolowezi chogunda anthu ndipo mwini wakeyo anachenjezedwa koma iye sanayimange ndipo yapha mwamuna kapena mkazi, ngʼombeyo iponyedwe miyala ndipo mwini wakeyo aphedwenso. 30 Koma ngati wauzidwa kuti alipire, iye apereke zimene wauzidwazo kuti awombole moyo wake. 31 Lamulo ili ligwirenso ntchito ngati ngʼombeyo yagunda mwana wamwamuna kapena wamkazi. 32 Ngati ngʼombeyo yagunda kapolo wamwamuna kapena mdzakazi, mwini ngʼombeyo apereke masekeli makumi atatu a siliva kwa mwini kapoloyo, ndipo ngʼombeyo iponyedwe miyala.

33 “Munthu akasiya dzenje lapululu kapena akakumba dzenje koma wosaphimbapo, ndipo ngʼombe kapena bulu nʼkugweramo, 34 mwini dzenjelo amulipire mwini chiweto chakufacho koma iye atenge chiwetocho.

35 “Ngati ngʼombe ya munthu wina ipha ngʼombe ya mnzake, ngʼombe yamoyo ija igulitsidwe ndipo anthu awiriwo agawane pakati ndalama yake. Achite chimodzimodzi ndi ngʼombe yakufa ija. 36 Koma zikadziwika kuti ngʼombeyo inali ndi khalidwe logunda, ndipo mwini wake samayitsekera mʼkhola, mwini ngʼombeyo alipire ngʼombe ina yamoyo koma atenge yakufayo.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.