Beginning
Mkazi Wachiwerewere
17 Mmodzi wa angelo asanu ndi awiri aja amene anali ndi mbale zisanu ndi ziwiri anadza nati kwa ine, “Bwera ndikuonetse chilango cha mkazi wadama wotchuka uja amene akukhala pambali pa madzi ambiri. 2 Mafumu a dziko lapansi amachita naye chigololo ndipo okhala pa dziko lapansi analedzera ndi vinyo wa zigololo zake.”
3 Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 4 Mkaziyo anavala zovala za pepo ndi zofiira nadzikongoletsa ndi golide, miyala yapamwamba ndi ngale. Ananyamula chikho chagolide mʼdzanja lake, chodzaza ndi zinthu zonyansa ndi fungo loyipa la zigololo zake. 5 Pa mphumi pake panalembedwa dzina lodabwitsa:
BABULONI WAMKULU
MAYI WA AKAZI ADAMA
NDI WAZOYIPITSA ZA DZIKO LAPANSI.
6 Ndinaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a oyera mtima, magazi a amene anachitira umboni Yesu.
Nditamuona mkaziyo ndinadabwa kwambiri. 7 Kenaka mngelo uja anati kwa ine, “Bwanji ukudabwa? Ndikufotokozera chinsinsi cha mkaziyu ndi chinsinsi cha chirombo chimene wakwerapochi chokhala ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. 8 Chirombo chimene wachionachi chinalipo kale koma tsopano kulibe ndipo chidzatuluka ku chidzenje chakuya ndi kupita kukawonongedwa. Anthu okhala pa dziko lapansi amene mayina awo sanalembedwe mʼbuku lamoyo kuyambira pa kulengedwa kwa dziko lapansi adzadabwa pamene adzaona chirombocho, chifukwa chinalipo kale, tsopano kulibe, komabe chidzabwera.
9 “Zimenezi zikufunika kuganizira mwanzeru. Mitu isanu ndi iwiriyo ndi mapiri asanu ndi awiri pomwe mkazi uja amakhalirapo. Yomweyonso ndi mafumu asanu ndi awiri. 10 Mafumu asanu anagwa, imodzi ilipo ndipo ina sinabwere; koma pamene idzafika, idzayenera kukhala kwa kanthawi kochepa. 11 Chirombo chomwe chinalipo kale ndipo tsopano kulibe ndiyo mfumu yachisanu ndi chitatu. Iyo ndi ya mʼgulu la asanu ndi awiriwo ndipo ikupita kukawonongedwa.
12 “Nyanga khumi unaziona zija ndi mafumu khumi amene sanapatsidwe ulamuliro, koma adzapatsidwa ulamuliro pamodzi ndi chirombo kwa ora limodzi. 13 Mafumuwo ali ndi cholinga chimodzi ndipo adzapereka mphamvu ndi ulamuliro wawo kwa chirombocho. 14 Iwo adzachita nkhondo ndi Mwana Wankhosa, koma Mwana Wankhosayo adzawagonjetsa chifukwa Iye ndi Mbuye wa ambuye ndi Mfumu ya mafumu, ndipo amene adzakhala ndi Iye ndi oyitanidwa ake, osankhidwa ndi otsatira ake okhulupirika.”
15 Kenaka mngeloyo anati kwa ine, “Madzi amene unawaona pamene mkazi wadamayo anakhalapo ndiwo anthu ochuluka, mitundu ndi ziyankhulo. 16 Nyanga khumi ndi chirombo unazionazo zidzadya mkazi wadamayo. Zidzamufwifwitsa ndi kumusiya wamaliseche; zidzadya nyama yake ndi kumutentha ndi moto. 17 Pakuti Mulungu wayika ichi mʼmitima mwawo kuti akwaniritse cholinga chake povomerezana kupereka mphamvu zawo zolamulira kwa chirombo, kufikira Mawu a Mulungu atakwaniritsidwa. 18 Mkazi unamuonayo ndi mzinda waukulu umene ulamulira mafumu a dziko lapansi.”
Kugwa kwa Babuloni
18 Zitatha izi ndinaona mngelo wina akutsika kuchokera kumwamba. Iye anali ndi ulamuliro waukulu, ndipo dziko lapansi linawala ndi ulemerero. 2 Mngeloyo anafuwula ndi mawu amphamvu kuti:
“ ‘Wagwa! Wagwa Babuloni Wamkulu!’
Wasandulika mokhalamo ziwanda
ndi kofikako mizimu yonse yoyipa
ndi mbalame zonse zonyansa
ndi zodetsedwa.
3 Pakuti mayiko onse amwa
vinyo ozunguza mutu wazigololo zake.
Mafumu a dziko lapansi achita naye chigololo,
ndipo amalonda a dziko lapansi analemera kuchokera pa zolakalaka zake zosefukira.”
Awachenjeza kuti Athawe Chiweruzo cha Babuloni
4 Ndiponso ndinamva mawu ena kuchokera kumwamba akuti:
“ ‘Anthu anga tulukani, mwa iye,’
mungachimwe naye
kuti musadzalandire nawo gawo lililonse la miliri yake;
5 pakuti machimo ake awunjikana mpaka kumwamba,
ndipo Mulungu wakumbukira milandu yake.
6 Bwezerani Iye monga momwe iye anakuchitirani.
Mubwezereni mowirikiza pa zimene anachita.
Mumusakanizire magawo awiri kuchokera mʼchikho chake.
7 Mumuzunze, kumumvetsa chisoni kwambiri
monga mwaulemerero ndi zolakalaka
zimene anadzaza mu mtima mwake. Iye anadzikuza nʼkumati,
‘Ndinakhala monga mfumu yayikazi,
ine sindine wamasiye
ndipo sindidzalira maliro.’
8 Chifukwa chake miliri yake idzamugonjetsa tsiku limodzi;
imfa, kulira maliro ndi njala.
Iye adzanyeka ndi moto
pakuti wamphamvu ndi Mulungu Ambuye amene wamuweruza.
Tsoka la Babuloni
9 “Mafumu a dziko lapansi, amene anachita naye chigololo nachita naye pamodzi zosangalatsa moyo uno, akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzalira nakhuza maliro ake. 10 Iwo adzayima kutali nalira chifukwa choopsedwa ndi mazunzo ake.
“ ‘Tsoka! Tsoka mzinda waukulu
iwe, Babuloni mzinda wamphamvu!
Mu ora limodzi chiwonongeko chako chafika!’
11 “Amalonda a dziko lapansi adzalira nakhuza maliro ake chifukwa palibenso amene akugula katundu wawo, 12 katundu wagolide, siliva, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale; nsalu zoyera kwambiri zapamwamba ndi zofiira; nsalu zasilika ndi zapepo; mitengo iliyonse yonunkhira ndi zinthu zilizonse zopangidwa ndi mnyanga, kapena matabwa ogulidwa ndi ndalama zambiri kapena mkuwa kapena chitsulo ndi mwala wonyezimira; 13 zokometsera zakudya, mure, lubani ndi zofukiza zina, vinyo ndi mafuta a olivi, ufa wosalala ndi tirigu; ngʼombe ndi nkhosa; akavalo ndi ngolo; ndi anthu adzagulitsidwa ukapolo.
14 “Iwo adzanena kuti, ‘Chipatso chimene unachilakalaka chakuchokera. Chuma chako chonse ndi ulemerero zatha, sizidzapezekanso.’ 15 Amalonda amene anagulitsa zinthu izi napeza chuma kuchokera kwa iye adzayima patali potero ataopsedwa ndi mazunzo ake. Adzalira ndi kukhuza maliro 16 ndipo adzalira mokuwa kuti,
“ ‘Tsoka! Tsoka! Mzinda waukulu,
iwe wovala nsalu zoyera kwambiri, zapepo ndi zofiira,
ndi wonyezimira ndi golide, miyala yamtengo wapamwamba ndi ngale!
17 Chuma chambiri choterechi chafika powonongeka mu ora limodzi!’
“Oyendetsa sitima ndi onse oyenda pa sitima ya pamadzi, ogwira ntchito mʼsitima ndi onse amene amadalira nyanja pamoyo wa tsiku ndi tsiku adzayima patali potero. 18 Akadzaona utsi wa kunyeka kwake, adzakuwa kuti, ‘Kodi panalinso mzinda wina ngati mzinda waukuluwu?’ 19 Adzathira fumbi pamitu pawo ndipo adzalira nakhuza maliro kuti,
“Tsoka! Tsoka mzinda waukulu iwe,
kumene onse anali ndi sitima pa nyanja
analemera kudzera mʼchuma chake!
Mu ora limodzi wawonongedwa.
20 “Kondwerani chifukwa cha iye inu kumwamba!
Kondwerani oyera mtima
ndi atumwi ndi aneneri!
Mulungu wamuweruza iye
monga momwe anakuchitirani inu.”
Chiwonongeko Chotsiriza cha Babuloni
21 Kenaka mngelo wamphamvu ananyamula mwala waukulu ngati mphero yayikulu nawuponya mʼnyanja nanena kuti,
“Mwa mphamvu chonchi
mzinda waukulu wa Babuloni udzaponyedwa pansi,
sudzapezekanso.
22 Mwa iwe simudzamvekanso liwu la woyimba zeze, ndi akatswiri a zoyimbayimba,
oyimba zitoliro, ndi lipenga.
Mwa iwe simudzapezekanso
mʼmisiri wina aliyense.
Mwa iwe simudzapezekanso
phokoso la mphero.
23 Kuwala kwa nyale
sikudzawunikanso mwa inu.
Mawu a mkwati ndi mkwatibwi
sadzamvekanso mwa iwe.
Amalonda anu anali akuluakulu a dziko lapansi.
Mitundu yonse inasokonezedwa ndi zamatsenga zako.
24 Mwa iye munapezeka magazi a aneneri ndi a oyera mtima,
ndi onse amene anaphedwa pa dziko lapansi.”
Babuloni Wagwa, Haleluya!
19 Zitatha izi, ndinamva chimene chinamveka ngati phokoso la gulu lalikulu mmwamba likufuwula kuti,
“Haleluya!
Chipulumutso ndi ulemerero ndi mphamvu ndi za Mulungu wathu,
2 pakuti chiweruzo chake ndi choona ndi cha chilungamo.
Iye waweruza mkazi wadama wotchuka uja
amene anayipitsa dziko lonse lapansi ndi zigololo zake.
Iye wabwezera pa mkaziyo magazi a atumiki ake.”
3 Ndipo anafuwulanso kuti,
“Haleluya!
Utsi wochokera kwa mkazi wadamayo udzakwera kumwamba mpaka muyaya.”
4 Akuluakulu 24 aja ndi zamoyo zinayi zija anadzigwetsa pansi kupembedza Mulungu amene anakhala pa mpando waufumu. Ndipo anafuwula kuti,
“Ameni, Haleluya!”
5 Kenaka mawu anachoka ku mpando waufumu kuti,
“Lemekezani Mulungu wathu
inu nonse atumiki ake,
inu amene mumamuopa,
nonse angʼono ndi akulu!”
6 Kenaka ndinamva chimene chinamveka ngati gulu lalikulu, ngati mkokomo wamadzi othamanga ndipo ngati kugunda kwakukulu kwa bingu, ndipo anati,
“Haleluya!
Pakuti Ambuye Mulungu wathu Wamphamvuzonse akulamulira.
7 Tiyeni tisangalale ndi kukondwera
ndi kumutamanda!
Pakuti nthawi ya ukwati wa Mwana Wankhosa yafika,
ndipo Mkwatibwi wakonzekeratu.
8 Wapatsidwa nsalu yoyera kwambiri, yowala ndi yosada
kuti avale.”
(Nsalu yoyera kwambiri ikuyimira ntchito zolungama za oyera mtima).
9 Kenaka mngelo anandiwuza kuti, “Lemba kuti, Odala amene ayitanidwa ku phwando la ukwati wa Mwana Wankhosa.” Ndipo anatinso, “Awa ndiwo mawu woona a Mulungu.”
10 Pamenepo ndinadzigwetsa pa mapazi ake kumupembedza. Koma anandiwuza kuti, “Usatero ayi, ine ndine mtumiki mnzako ngati iwe yemwe, ndiponso ngati abale ako amene asunga umboni wa Yesu. Pembedza Mulungu. Pakuti umboni wa Yesu ndiye mzimu wa uneneri.”
Wokwera pa Kavalo Woyera
11 Ndinaona kumwamba kutatsekuka ndipo patsogolo panga panali kavalo woyera, amene anakwerapo dzina lake linali Wokhulupirika ndiponso Woona. Poweruza ndi kuchita nkhondo, amachita molungama. 12 Maso ake anali ngati malawi amoto, ndipo pamutu pake panali zipewa zaufumu zambiri. Anali ndi dzina lolembedwa, lodziwika ndi Iye yekha, osati wina aliyense. 13 Iye anavala mkanjo woviyika mʼmagazi, ndipo dzina lake ndi Mawu a Mulungu. 14 Magulu ankhondo akumwamba ankamutsatira atakwera pa akavalo oyera, ndipo iwowo atavala nsalu zoyera kwambiri ndi zosada. 15 Mʼkamwa mwake munatuluka lupanga lakuthwa limene anati akaphe nalo mitundu ya anthu. Iye adzalamulira ndi ndodo yachitsulo. Iye anaponda choponderamo mphesa cha ukali wa Mulungu Wamphamvuzonse. 16 Pa chovala ndi pa ntchafu pake panalembedwa dzina ili:
MFUMU YA MAFUMU NDI MBUYE WA AMBUYE.
17 Ndipo ndinaona mngelo atayimirira pa dzuwa amene anafuwula ndi mawu okweza kwa mbalame zonse zowuluka mlengalenga kuti, “Bwerani, sonkhanani pamodzi ku phwando lalikulu la Mulungu. 18 Kuti mudye mnofu wa mafumu, wa akulu a ankhondo, ndi wa anthu amphamvu, wa akavalo ndi okwerapo awo, ndi wa anthu onse, mfulu ndi akapolo, angʼono ndi aakulu.”
19 Kenaka ndinaona chirombo chija ndi mafumu a dziko lapansi ndi magulu ankhondo atasonkhana pamodzi kuti achite nkhondo ndi wokwera pa kavalo ndi ankhondo ake. 20 Koma chirombocho chinagwidwa pamodzi ndi mneneri wonyenga uja amene anachita zizindikiro zodabwitsa pamaso pake. Ndi zizindikirozi anasocheretsa amene analembedwa chizindikiro cha chirombocho napembedza fano lake. Onse awiri anaponyedwa amoyo mʼnyanja yamoto yasulufule wotentha. 21 Ena onse anaphedwa ndi lupanga lija linatuluka mʼkamwa mwa wokwera pa kavalo uja, ndipo mbalame zonse zinadya mokwanira mnofu wa anthu akufawo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.