Add parallel Print Page Options

Mwambo Wodzoza Aaroni ndi Ana Ake

Yehova anawuza Mose kuti, “Tenga Aaroni ndi ana ake, zovala zawo, mafuta wodzozera, ngʼombe yayimuna kuti ikhale nsembe yopepesera machimo, nkhosa ziwiri zazimuna ndi dengu la buledi wopanda yisiti, ndipo usonkhanitse gulu la anthu pa khomo la tenti ya msonkhano.” Mose anachita zomwe Yehova anamulamula ndipo gulu la anthu linasonkhana pa khomo la tenti ya msonkhano.

Mose anawuza gulu la anthuwo kuti, “Izi ndi zimene Yehova walamulira kuti zichitike.” Pamenepo Mose anabwera ndi Aaroni ndi ana ake nawasambitsa ndi madzi. Anamuveka Aaroni mwinjiro, ndi kumumanga lamba mʼchiwuno. Anamuvekanso mkanjo wa efodi ndi efodiyo. Anamangira lamba efodiyo amene analukidwa mwaluso uja, motero efodiyo analimba mʼchiwunomo. Anamuvekanso chovala chapachifuwa ndipo mʼchovalacho anayikamo Urimu ndi Tumimu. Kenaka anamuveka Aaroniyo nduwira kumutu ndipo patsogolo pa nduwirayo anayikapo duwa lagolide, chizindikiro chopatulika monga momwe Yehova analamulira Mose.

10 Pamenepo Mose anatenga mafuta wodzozera nadzoza tenti ya msonkhano pamodzi ndi zonse zimene zinali mʼmenemo, ndipo potero anazipatula. 11 Anawaza mafuta ena pa guwa kasanu ndi kawiri, nalidzoza guwalo pamodzi ndi ziwiya zake zonse. Anadzozanso beseni ndi tsinde lake, nazipatula. 12 Anathira mafuta wodzozera ena pamutu pa Aaroni ndipo anamudzoza ndi kumupatula. 13 Kenaka anabwera ndi ana a Aaroni. Anawaveka minjiro, ndi kuwamanga malamba mʼchiwuno ndi kuwaveka nduwira kumutu monga momwe Yehova analamulira Mose.

14 Kenaka Mose anabwera ndi ngʼombe yayimuna ya nsembe yopepesera machimo, ndipo Aaroni ndi ana ake anasanjika manja awo pamutu pa ngʼombeyo. 15 Mose anapha ngʼombeyo, ndi kutenga magazi ena angʼombeyo ndi kupaka ndi chala chake pa nyanga zaguwa lansembe, naliyeretsa. Magazi otsalawo anawakhuthulira pa tsinde laguwalo. Motero anachita mwambo wopepesera machimo. 16 Mose anatenganso mafuta onse okuta matumbo, mafuta ophimba chiwindi, ndiponso impsyo zonse ziwiri pamodzi ndi mafuta ake, nazitentha pa guwapo. 17 Koma nyama yangʼombeyo, chikopa chake ndi matumbo ake anaziwotcha kunja kwa msasa monga momwe Yehova analamulira Mose.

18 Kenaka anabwera ndi nkhosa yayimuna ya nsembe yopsereza, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake. 19 Ndipo Mose anapha nkhosayo ndi kuwaza magazi ake mbali zonse zaguwalo. 20 Anayidula nkhosayo nthulinthuli ndipo anatentha mutu wake, nthulizo ndi mafuta. 21 Anatsuka matumbo ake ndi miyendo yake, ndi kutentha nkhosa yonseyo pa guwa lansembe kuti ikhale nsembe yopsereza, fungo lokoma, nsembe yachakudya yoperekedwa kwa Yehova monga Yehovayo analamulira Mose.

22 Kenaka Mose anapereka nkhosa yayimuna ina pamwambo wodzoza ansembe, ndipo Aaroni ndi ana ake aamuna anasanjika manja awo pamutu pake. 23 Mose anayipha nkhosayo ndipo anatenga magazi ake ena ndi kupaka ndewere za khutu la kudzanja lamanja la Aaroni, pa chala chake chachikulu cha kudzanja lamanja, ndi pa chala chake chachikulu cha phazi lakumanja. 24 Pambuyo pake Mose anabwera ndi ana aamuna a Aaroni ndi kupaka magazi pa ndewere za makutu awo akumanja, pa zala zawo zazikulu za dzanja lamanja, ndiponso pa zala zawo zazikulu za kuphazi lakumanja. Kenaka iye anawaza magazi otsalawo mbali zonse za guwalo. 25 Anatenganso mafuta ake, mafuta a ku mchira wake, mafuta okuta matumbo, mafuta okuta chiwindi, impsyo zonse ziwiri ndi mafuta ake ndiponso ntchafu yakumanja. 26 Ndipo mʼdengu la buledi wopanda yisiti limene linali pamaso pa Yehova, anatengamo buledi mmodzi, buledi mmodzi wokhala ndi mafuta a olivi, ndi buledi wopyapyala mmodzi. Zonsezi anaziyika pa mafuta aja ndi pa ntchafu ya ku dzanja lamanja ija. 27 Mose anapereka zonsezi mʼmanja mwa Aaroni ndi ana ake amene anazipereka kwa Yehova kuti zikhale nsembe yoweyula. 28 Kenaka Mose anazitenga mʼmanja mwawo ndipo anazipsereza pa guwa lansembe pamwamba penipeni pamodzi ndi nsembe yopsereza ija kuti ikhale nsembe yopereka pamwambo wodzoza ansembe, kuti ipereke fungo lokoma, chopereka chachakudya kwa Yehova. 29 Mose anatenga chidale cha nkhosa yayimuna, chomwe ndi gawo lake pamwambo wodzoza ansembe, ndipo anachiweyula pamaso pa Yehova kuti chikhale nsembe yoweyula monga momwe Yehova analamulira Mose.

30 Kenaka Mose anatenga mafuta wodzozera ansembe ndi magazi amene anali pa guwa nawaza pa Aaroni ndi zovala zake ndiponso ana ake aja ndi zovala zawo. Motero Mose anapatula Aaroni ndi zovala zake, ndiponso ana ake ndi zovala zawo.

31 Mose anawuza Aaroni ndi ana ake kuti, “Phikani nyamayo pa khomo la tenti ya msonkhano, ndipo mudyere pomwepo pamodzi ndi buledi amene ali mʼdengu la zopereka za pamwambo wodzoza ansembe monga Yehova analamulira kuti, ‘Aaroni ndi ana ake azidya zimenezi.’ 32 Ndipo nyama ndi buledi zotsalazo, muziwotche. 33 Musatuluke kunja kwa tenti ya msonkhano kwa masiku asanu ndi awiri mpaka masiku amwambo wokudzozani unsembe atatha, pakuti mwambowu ndi wa masiku asanu ndi awiri. 34 Zimene zachitika lerozi analamula ndi Yehova kuti zichitike ngati nsembe yopepesera machimo anu. 35 Muzikhala pa khomo la tenti ya msonkhano usana ndi usiku kwa masiku asanu ndi awiri. Ndipo muzichita zimene Yehova wakulamulani kuti musafe, pakuti zimenezi ndi zomwe Yehova wandilamulira.” 36 Choncho Aaroni ndi ana ake anachita zonse zimene Yehova analamula kudzera mwa Mose.

The Ordination of Aaron and His Sons(A)

The Lord said to Moses, “Bring Aaron and his sons,(B) their garments,(C) the anointing oil,(D) the bull for the sin offering,[a](E) the two rams(F) and the basket containing bread made without yeast,(G) and gather the entire assembly(H) at the entrance to the tent of meeting.” Moses did as the Lord commanded him, and the assembly gathered at the entrance to the tent of meeting.

Moses said to the assembly, “This is what the Lord has commanded to be done.(I) Then Moses brought Aaron and his sons forward and washed them with water.(J) He put the tunic on Aaron, tied the sash around him, clothed him with the robe and put the ephod on him. He also fastened the ephod with a decorative waistband, which he tied around him.(K) He placed the breastpiece(L) on him and put the Urim and Thummim(M) in the breastpiece. Then he placed the turban(N) on Aaron’s head and set the gold plate, the sacred emblem,(O) on the front of it, as the Lord commanded Moses.(P)

10 Then Moses took the anointing oil(Q) and anointed(R) the tabernacle(S) and everything in it, and so consecrated them. 11 He sprinkled some of the oil on the altar seven times, anointing the altar and all its utensils and the basin with its stand, to consecrate them.(T) 12 He poured some of the anointing oil on Aaron’s head and anointed(U) him to consecrate him.(V) 13 Then he brought Aaron’s sons(W) forward, put tunics(X) on them, tied sashes around them and fastened caps on them, as the Lord commanded Moses.(Y)

14 He then presented the bull(Z) for the sin offering,(AA) and Aaron and his sons laid their hands on its head.(AB) 15 Moses slaughtered the bull and took some of the blood,(AC) and with his finger he put it on all the horns of the altar(AD) to purify the altar.(AE) He poured out the rest of the blood at the base of the altar. So he consecrated it to make atonement for it.(AF) 16 Moses also took all the fat around the internal organs, the long lobe of the liver, and both kidneys and their fat, and burned it on the altar. 17 But the bull with its hide and its flesh and its intestines(AG) he burned up outside the camp,(AH) as the Lord commanded Moses.

18 He then presented the ram(AI) for the burnt offering, and Aaron and his sons laid their hands on its head. 19 Then Moses slaughtered the ram and splashed the blood against the sides of the altar. 20 He cut the ram into pieces and burned the head, the pieces and the fat.(AJ) 21 He washed the internal organs and the legs with water and burned the whole ram on the altar. It was a burnt offering, a pleasing aroma, a food offering presented to the Lord, as the Lord commanded Moses.

22 He then presented the other ram, the ram for the ordination,(AK) and Aaron and his sons laid their hands on its head.(AL) 23 Moses slaughtered the ram and took some of its blood and put it on the lobe of Aaron’s right ear, on the thumb of his right hand and on the big toe of his right foot.(AM) 24 Moses also brought Aaron’s sons forward and put some of the blood on the lobes of their right ears, on the thumbs of their right hands and on the big toes of their right feet. Then he splashed blood against the sides of the altar.(AN) 25 After that, he took the fat(AO), the fat tail, all the fat around the internal organs, the long lobe of the liver, both kidneys and their fat and the right thigh. 26 And from the basket of bread made without yeast, which was before the Lord, he took one thick loaf, one thick loaf with olive oil mixed in, and one thin loaf,(AP) and he put these on the fat portions and on the right thigh. 27 He put all these in the hands of Aaron and his sons, and they waved them before the Lord(AQ) as a wave offering. 28 Then Moses took them from their hands and burned them on the altar on top of the burnt offering as an ordination offering, a pleasing aroma, a food offering presented to the Lord. 29 Moses also took the breast, which was his share of the ordination ram,(AR) and waved it before the Lord as a wave offering, as the Lord commanded Moses.

30 Then Moses(AS) took some of the anointing oil and some of the blood from the altar and sprinkled them on Aaron and his garments(AT) and on his sons and their garments. So he consecrated(AU) Aaron and his garments and his sons and their garments.

31 Moses then said to Aaron and his sons, “Cook the meat at the entrance to the tent of meeting(AV) and eat it there with the bread from the basket of ordination offerings, as I was commanded: ‘Aaron and his sons are to eat it.’ 32 Then burn up the rest of the meat and the bread. 33 Do not leave the entrance to the tent of meeting for seven days, until the days of your ordination are completed, for your ordination will last seven days.(AW) 34 What has been done today was commanded by the Lord(AX) to make atonement for you. 35 You must stay at the entrance to the tent of meeting day and night for seven days and do what the Lord requires,(AY) so you will not die; for that is what I have been commanded.”

36 So Aaron and his sons did everything the Lord commanded through Moses.

Footnotes

  1. Leviticus 8:2 Or purification offering; also in verse 14

And the Lord spake unto Moses, saying,

Take Aaron and his sons with him, and the garments, and the anointing oil, and a bullock for the sin offering, and two rams, and a basket of unleavened bread;

And gather thou all the congregation together unto the door of the tabernacle of the congregation.

And Moses did as the Lord commanded him; and the assembly was gathered together unto the door of the tabernacle of the congregation.

And Moses said unto the congregation, This is the thing which the Lord commanded to be done.

And Moses brought Aaron and his sons, and washed them with water.

And he put upon him the coat, and girded him with the girdle, and clothed him with the robe, and put the ephod upon him, and he girded him with the curious girdle of the ephod, and bound it unto him therewith.

And he put the breastplate upon him: also he put in the breastplate the Urim and the Thummim.

And he put the mitre upon his head; also upon the mitre, even upon his forefront, did he put the golden plate, the holy crown; as the Lord commanded Moses.

10 And Moses took the anointing oil, and anointed the tabernacle and all that was therein, and sanctified them.

11 And he sprinkled thereof upon the altar seven times, and anointed the altar and all his vessels, both the laver and his foot, to sanctify them.

12 And he poured of the anointing oil upon Aaron's head, and anointed him, to sanctify him.

13 And Moses brought Aaron's sons, and put coats upon them, and girded them with girdles, and put bonnets upon them; as the Lord commanded Moses.

14 And he brought the bullock for the sin offering: and Aaron and his sons laid their hands upon the head of the bullock for the sin offering.

15 And he slew it; and Moses took the blood, and put it upon the horns of the altar round about with his finger, and purified the altar, and poured the blood at the bottom of the altar, and sanctified it, to make reconciliation upon it.

16 And he took all the fat that was upon the inwards, and the caul above the liver, and the two kidneys, and their fat, and Moses burned it upon the altar.

17 But the bullock, and his hide, his flesh, and his dung, he burnt with fire without the camp; as the Lord commanded Moses.

18 And he brought the ram for the burnt offering: and Aaron and his sons laid their hands upon the head of the ram.

19 And he killed it; and Moses sprinkled the blood upon the altar round about.

20 And he cut the ram into pieces; and Moses burnt the head, and the pieces, and the fat.

21 And he washed the inwards and the legs in water; and Moses burnt the whole ram upon the altar: it was a burnt sacrifice for a sweet savour, and an offering made by fire unto the Lord; as the Lord commanded Moses.

22 And he brought the other ram, the ram of consecration: and Aaron and his sons laid their hands upon the head of the ram.

23 And he slew it; and Moses took of the blood of it, and put it upon the tip of Aaron's right ear, and upon the thumb of his right hand, and upon the great toe of his right foot.

24 And he brought Aaron's sons, and Moses put of the blood upon the tip of their right ear, and upon the thumbs of their right hands, and upon the great toes of their right feet: and Moses sprinkled the blood upon the altar round about.

25 And he took the fat, and the rump, and all the fat that was upon the inwards, and the caul above the liver, and the two kidneys, and their fat, and the right shoulder:

26 And out of the basket of unleavened bread, that was before the Lord, he took one unleavened cake, and a cake of oiled bread, and one wafer, and put them on the fat, and upon the right shoulder:

27 And he put all upon Aaron's hands, and upon his sons' hands, and waved them for a wave offering before the Lord.

28 And Moses took them from off their hands, and burnt them on the altar upon the burnt offering: they were consecrations for a sweet savour: it is an offering made by fire unto the Lord.

29 And Moses took the breast, and waved it for a wave offering before the Lord: for of the ram of consecration it was Moses' part; as the Lord commanded Moses.

30 And Moses took of the anointing oil, and of the blood which was upon the altar, and sprinkled it upon Aaron, and upon his garments, and upon his sons, and upon his sons' garments with him; and sanctified Aaron, and his garments, and his sons, and his sons' garments with him.

31 And Moses said unto Aaron and to his sons, Boil the flesh at the door of the tabernacle of the congregation: and there eat it with the bread that is in the basket of consecrations, as I commanded, saying, Aaron and his sons shall eat it.

32 And that which remaineth of the flesh and of the bread shall ye burn with fire.

33 And ye shall not go out of the door of the tabernacle of the congregation in seven days, until the days of your consecration be at an end: for seven days shall he consecrate you.

34 As he hath done this day, so the Lord hath commanded to do, to make an atonement for you.

35 Therefore shall ye abide at the door of the tabernacle of the congregation day and night seven days, and keep the charge of the Lord, that ye die not: for so I am commanded.

36 So Aaron and his sons did all things which the Lord commanded by the hand of Moses.