Hebreaid 5
Beibl William Morgan
5 Canys pob archoffeiriad wedi ei gymryd o blith dynion, a osodir dros ddynion yn y pethau sydd tuag at Dduw, fel yr offrymo roddion ac aberthau dros bechodau: 2 Yr hwn a ddichon dosturio wrth y rhai sydd mewn anwybodaeth ac amryfusedd; am ei fod yntau hefyd wedi ei amgylchu â gwendid. 3 Ac o achos hyn y dylai, megis dros y bobl, felly hefyd drosto ei hun, offrymu dros bechodau. 4 Ac nid yw neb yn cymryd yr anrhydedd hwn iddo ei hun, ond yr hwn a alwyd gan Dduw, megis Aaron. 5 Felly Crist hefyd nis gogoneddodd ei hun i fod yn Archoffeiriad; ond yr hwn a ddywedodd wrtho, Tydi yw fy Mab; myfi heddiw a’th genhedlais di. 6 Megis y mae yn dywedyd mewn lle arall, Offeiriad wyt ti yn dragywydd yn ôl urdd Melchisedec. 7 Yr hwn yn nyddiau ei gnawd, gwedi iddo, trwy lefain cryf a dagrau, offrwm gweddïau ac erfyniau at yr hwn oedd abl i’w achub ef oddi wrth farwolaeth, a chael ei wrando yn yr hyn a ofnodd; 8 Er ei fod yn Fab, a ddysgodd ufudd‐dod trwy’r pethau a ddioddefodd: 9 Ac wedi ei berffeithio, efe a wnaethpwyd yn Awdur iachawdwriaeth dragwyddol i’r rhai oll a ufuddhant iddo; 10 Wedi ei gyfenwi gan Dduw yn Archoffeiriad yn ôl urdd Melchisedec. 11 Am yr hwn y mae i ni lawer i’w dywedyd, ac anodd eu traethu, o achos eich bod chwi yn hwyrdrwm eich clustiau. 12 Canys lle dylech fod yn athrawon o ran amser, y mae arnoch drachefn eisiau dysgu i chwi beth ydyw egwyddorion dechreuad ymadroddion Duw: ac yr ydych yn rhaid i chwi wrth laeth, ac nid bwyd cryf. 13 Canys pob un a’r sydd yn ymarfer â llaeth, sydd anghynefin â gair cyfiawnder; canys maban yw. 14 Eithr bwyd cryf a berthyn i’r rhai perffaith, y rhai oherwydd cynefindra y mae ganddynt synnwyr wedi ymarfer i ddosbarthu drwg a da.
Ahebri 5
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero
5 Mkulu wa ansembe aliyense amasankhidwa kuchokera pakati pa anthu ndipo amayikidwa kuti aziwayimirira pamaso pa Mulungu, kuti azipereka mphatso ndi nsembe chifukwa cha machimo. 2 Popeza kuti iye mwini ali ndi zofowoka zake, amatha kuwalezera mtima amene ali osadziwa ndi osochera. 3 Chifukwa cha ichi, iye amadziperekera nsembe chifukwa cha machimo ake omwe ndiponso chifukwa cha machimo a anthu ena.
4 Palibe amene amadzipatsa yekha ulemu wotere, koma amachita kuyitanidwa ndi Mulungu monga momwe anayitanidwira Aaroni. 5 Nʼchifukwa chake Khristu sanadzipatse yekha ulemu wokhala Mkulu wa ansembe. Koma Mulungu anamuwuza kuti,
“Iwe ndiwe Mwana wanga;
Ine lero ndakhala Atate ako.”
6 Ndipo penanso anati,
“Iwe ndiwe wansembe mpaka muyaya,
monga mwa unsembe wa Melikizedeki.”
7 Yesu, pa nthawi imene anali munthu pa dziko lapansi pano, anapereka mapemphero ake ndi zopempha mofuwula ndi misozi kwa Iye amene akanamupulumutsa ku imfa, ndipo anamumvera chifukwa anagonjera modzipereka. 8 Ngakhale Iye anali Mwana wa Mulungu anaphunzira kumvera pomva zowawa. 9 Atasanduka wangwiro kotheratu, anakhala gwero la chipulumutso chosatha kwa onse omvera Iye. 10 Ndipo Mulungu anamuyika kukhala Mkulu wa ansembe, monga mwa dongosolo la unsembe wa Melikizedeki.
Awachenjeza kuti Asataye Chikhulupiriro
11 Tili ndi zambiri zoti tinganene pa zimenezi, koma ndi zovuta kukufotokozerani chifukwa ndinu ochedwa kuphunzira. 12 Ngakhale kuti pa nthawi ino munayenera kukhala aphunzitsi, pakufunikabe munthu wina kuti abwerezenso kudzakuphunzitsani maphunziro oyambira a choonadi cha Mulungu. Ndinu ofunika mkaka osati chakudya cholimba! 13 Aliyense amene amangodya mkaka okha, akanali mwana wakhanda, sakudziwa bwino chiphunzitso cha chilungamo. 14 Koma chakudya cholimba ndi cha anthu okhwima msinkhu, amene pogwiritsa ntchito nzeru zawo, aphunzira kusiyanitsa chabwino ndi choyipa.
William Morgan Welsh Bible Edition © British & Foreign Bible Society 1992.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.