Add parallel Print Page Options

Paska

16 Samalirani mwezi wa Abibu ndi kukondwerera Paska wa Yehova Mulungu wanu, chifukwa pa mwezi wa Abibu, usiku, Iye anakutulutsani mu Igupto. Mumuphere Yehova Mulungu wanu nsembe ya Paska, chiweto chochokera pa nkhosa zanu kapena ngʼombe zanu kumalo kumene Yehova adzasankha kuti akhazikeko dzina lake. Musadyere pamodzi ndi buledi wopanga ndi yisiti, koma kwa masiku asanu ndi awiri muzidya buledi wopanda yisiti, buledi wa masautso, chifukwa munachoka ku Igupto mwamsangamsanga kuti pa masiku onse a moyo wanu muzikumbukira nthawi imene munanyamukira ku Igupto. Yisiti asapezeke kwa masiku asanu ndi awiri pa katundu wanu mʼdziko lanu lonse. Ndipo musasunge nyama imene mwapereka nsembe madzulo a tsiku loyamba mpaka mmawa.

Musamangopereka nsembe ya Paska mu mzinda wina uliwonse umene Yehova Mulungu wanu wakupatsani, koma ku malo wokhawo amene Iye adzawasankhe kukhazikitsako Dzina lake. Kumeneko ndiye muzikapereka nsembe ya Paska madzulo, pamene dzuwa likulowa, pa tsiku lokumbukira kutuluka mu Igupto. Muyiwotche ndi kuyidya pa malo pamene Yehova Mulungu wanu adzasankhe. Kenaka mmawa mubwerere ku matenti anu. Kwa masiku asanu ndi limodzi muzidya buledi wopanda yisiti ndipo pa tsiku lachisanu ndi chiwiri muzikhala ndi msonkhano wa Yehova Mulungu wanu ndipo musamagwire ntchito iliyonse.

Chikondwerero cha Masabata

Muziwerenga masabata asanu ndi awiri kuyambira pamene mwatenga chikwakwa ndi kuyamba kumweta tirigu wachilili. 10 Pamenepo muzichita Chikondwerero cha Masabata pamaso pa Yehova Mulungu wanu popereka chopereka chaufulu mofanana ndi madalitso amene Yehova Mulungu wakupatsani 11 Ndipo inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi a mʼmizinda mwanu, alendo, ana ndi akazi amasiye okhala pakati panu, mukondwere pamaso pa Yehova Mulungu wanu ku malo amene adzawasankhe kukhazikitsako dzina lake. 12 Kumbukirani kuti inunso munali akapolo ku Igupto, ndiye muzitsatira malangizo awa mosamalitsa.

Chikondwerero cha Misasa

13 Mukatha kukolola tirigu wanu ndi kupsinya vinyo wanu, muzikhala ndi Chikondwerero cha Misasa kwa masiku asanu ndi awiri. 14 Musangalale pa chikondwerero chanu, inu, ana anu aamuna, aakazi, antchito anu aamuna, adzakazi, Alevi, alendo, ana ndi akazi amasiye amene ali mʼmizinda yanu. 15 Kwa masiku asanu ndi awiri muzichita chikondwererochi kwa Yehova Mulungu wanu kumalo kumene Yehova adzasankhe. Pakuti Yehova Mulungu wanu adzakudalitsani inu pa zokolola zanu ndi pa ntchito za manja anu, ndipo chimwemwe chanu chidzakhala chathunthu.

16 Amuna onse azionekera pamaso pa Yehova Mulungu katatu pa chaka ku malo amene Iye adzasankha. Pa Chikondwerero cha Buledi wopanda Yisiti, pa Chikondwerero cha Masabata ndi pa Chikondwerero cha Misasa. Munthu aliyense asadzapite pamaso pa Yehova wopanda kanthu mʼmanja mwake. 17 Aliyense wa inu adzabweretse mphatso molingana ndi momwe Yehova Mulungu wanu wakudalitsirani.

Oweruza

18 Musankhe oweruza ndi akuluakulu a fuko lanu lililonse mu mzinda uliwonse umene Yehova Mulungu wanu akukupatsani, ndipo adzaweruza anthuwa mwachilungamo. 19 Musamakhotetse chiweruzo kapena kukondera. Musamalandire chiphuphu pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu a nzeru ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. 20 Tsatani chilungamo chokhachokha basi kuti mukhale ndi moyo ndi kutenga dziko limene Yehova Mulungu wanu akukupatsani.

Kupembedza Milungu Ina

21 Musazike mtengo wina uliwonse wa mafano a Asera pambali pa guwa lansembe la Yehova Mulungu wanu, 22 ndipo musayimike mwala wachipembedzo pakuti Yehova Mulungu wanu amadana nazo zimenezi.

The Passover(A)

16 Observe the month of Aviv(B) and celebrate the Passover(C) of the Lord your God, because in the month of Aviv he brought you out of Egypt by night. Sacrifice as the Passover to the Lord your God an animal from your flock or herd at the place the Lord will choose as a dwelling for his Name.(D) Do not eat it with bread made with yeast, but for seven days eat unleavened bread, the bread of affliction,(E) because you left Egypt in haste(F)—so that all the days of your life you may remember the time of your departure from Egypt.(G) Let no yeast be found in your possession in all your land for seven days. Do not let any of the meat you sacrifice on the evening(H) of the first day remain until morning.(I)

You must not sacrifice the Passover in any town the Lord your God gives you except in the place he will choose as a dwelling for his Name. There you must sacrifice the Passover in the evening, when the sun goes down, on the anniversary[a](J) of your departure from Egypt. Roast(K) it and eat it at the place the Lord your God will choose. Then in the morning return to your tents. For six days eat unleavened bread and on the seventh day hold an assembly(L) to the Lord your God and do no work.(M)

The Festival of Weeks(N)

Count off seven weeks(O) from the time you begin to put the sickle to the standing grain.(P) 10 Then celebrate the Festival of Weeks to the Lord your God by giving a freewill offering in proportion to the blessings the Lord your God has given you. 11 And rejoice(Q) before the Lord your God at the place he will choose as a dwelling for his Name(R)—you, your sons and daughters, your male and female servants, the Levites(S) in your towns, and the foreigners,(T) the fatherless and the widows living among you.(U) 12 Remember that you were slaves in Egypt,(V) and follow carefully these decrees.

The Festival of Tabernacles(W)

13 Celebrate the Festival of Tabernacles for seven days after you have gathered the produce of your threshing floor(X) and your winepress.(Y) 14 Be joyful(Z) at your festival—you, your sons and daughters, your male and female servants, and the Levites, the foreigners, the fatherless and the widows who live in your towns. 15 For seven days celebrate the festival to the Lord your God at the place the Lord will choose. For the Lord your God will bless you in all your harvest and in all the work of your hands, and your joy(AA) will be complete.

16 Three times a year all your men must appear(AB) before the Lord your God at the place he will choose: at the Festival of Unleavened Bread,(AC) the Festival of Weeks and the Festival of Tabernacles.(AD) No one should appear before the Lord empty-handed:(AE) 17 Each of you must bring a gift in proportion to the way the Lord your God has blessed you.

Judges

18 Appoint judges(AF) and officials for each of your tribes in every town the Lord your God is giving you, and they shall judge the people fairly.(AG) 19 Do not pervert justice(AH) or show partiality.(AI) Do not accept a bribe,(AJ) for a bribe blinds the eyes of the wise and twists the words of the innocent. 20 Follow justice and justice alone, so that you may live and possess the land the Lord your God is giving you.

Worshiping Other Gods

21 Do not set up any wooden Asherah pole(AK) beside the altar you build to the Lord your God,(AL) 22 and do not erect a sacred stone,(AM) for these the Lord your God hates.

Footnotes

  1. Deuteronomy 16:6 Or down, at the time of day