Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Luka 1:46-55

Nyimbo ya Mariya

46 Ndipo Mariya anati:

“Moyo wanga ulemekeza Ambuye.
47     Ndipo mzimu wanga ukondwera mwa Mulungu Mpulumutsi wanga,
48 pakuti wakumbukira
    kudzichepetsa kwa mtumiki wake.
Kuyambira tsopano mibado yonse idzanditcha wodala,
49     pakuti Wamkuluyo wandichitira ine zinthu zazikulu,
    dzina lake ndi loyera.
50 Chifundo chake chifikira kwa iwo amene amuopa Iye
    kufikira mibadomibado.
51 Iye wachita zamphamvu ndi dzanja lake;
    Iye anabalalitsa iwo amene ali onyada mʼmaganizo awo.
52 Iye anachotsa olamulira pa mipando yawo yaufumu,
    koma wakweza odzichepetsa.
53 Iye wakhutitsa a njala ndi zinthu zabwino
    koma anachotsa olemera wopanda kanthu.
54 Iye anathandiza mtumiki wake Israeli,
    pokumbukira chifundo chake.
55 Kwa Abrahamu ndi zidzukulu zake ku nthawi zonse
    monga ananena kwa makolo athu.”

Yesaya 33:17-22

17 Nthawi imeneyo maso a ana adzaona mfumu ya maonekedwe wokongola
    ndi kuona dziko lotambasukira kutali.
18 Mu mtima mwanu muzidzalingalira zoopsa zinachitika kale zija:
    “Ali kuti mkulu wa Asilikali uja?
    Ali kuti wokhometsa misonkho uja?
    Ali kuti mkulu woyangʼanira nsanja?”
19 Simudzawaonanso anthu odzikuza aja,
    anthu aja achiyankhulo chosadziwika,
    chachilendo ndi chosamveka.

20 Taonani Ziyoni, mzinda wa zikondwerero zachipembedzo chathu;
    maso anu adzaona Yerusalemu,
    mzinda wamtendere, tenti imene sidzachotsedwa,
zikhomo zake sizidzazulidwa,
    kapena zingwe zake kuduka.
21 Kumeneko Yehova adzaonetsa ulemerero wake
    ndipo mzindawo udzakhala kasupe wa mitsinje yayikulu.
Ngalawa za zopalasa sizidzapitamo,
    sitima zapamadzi zikuluzikulu sizidzayendamo.
22 Pakuti Yehova ndi woweruza wathu,
    Yehova ndiye wotilamulira,
Yehova ndiye mfumu yathu;
    ndipo ndiye amene adzatipulumutse.

Chivumbulutso 22:6-7

Mngeloyo anandiwuza kuti, “Mawu awa ndi okhulupirika ndi owona. Ambuye Mulungu wa mizimu ya aneneri anatumiza mngelo wake kudzaonetsa atumiki ake zinthu zimene ziyenera kuchitika posachedwapa.”

Yesu Akubweranso

“Taonani, ndikubwera posachedwa! Wodala ndi amene asunga mawu oneneratu za kutsogolo a mʼbuku ili.”

Chivumbulutso 22:18-20

18 Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, “Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili. 19 Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili.”

20 Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, “Inde, Ine ndikubwera posachedwa.”

Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.