Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 7:10-16

10 Yehova anayankhulanso ndi Ahazi, 11 “Pempha chizindikiro kwa Yehova Mulungu wako, chikhale chozama ngati manda kapena chachitali ngati mlengalenga.”

12 Koma Ahazi anati, “Ine sindipempha; sindikufuna kuyesa Yehova.”

13 Apo Yesaya anati, “Imva tsopano, iwe nyumba ya Davide! Kodi sikokwanira kutopetsa anthu? Kodi mudzayeseranso kutopetsa Mulungu wanga? 14 Nʼchifukwa chake Ambuye mwini adzakupatsani chizindikiro: Onani, namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli. 15 Azidzadya chambiko ndi uchi, mpaka atadziwa kukana choyipa ndi kusankha chabwino. 16 Koma nthawi yokana choyipa ndi kusankha chabwino kwa mwanayo isanafike, mayiko a mafumu awiri amene amakuopsaniwo adzakhala atasanduka bwinja.

Masalimo 80:1-7

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.

80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
    Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
    kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
    bwerani ndi kutipulumutsa.

Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
    mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
    kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
Mwawadyetsa buledi wa misozi;
    mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
    ndipo adani athu akutinyoza.

Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Masalimo 80:17-19

17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,
    mwana wa munthu amene mwalera nokha.
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;
    titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.

19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Aroma 1:1-7

Ndine Paulo, mtumiki wa Khristu Yesu, woyitanidwa ndi Mulungu kukhala mtumwi. Ndinapatulidwa kuti ndilalikire Uthenga Wabwino wa Mulungu umene analonjeza kale mʼMalemba Oyera kudzera mwa aneneri ake. Uthengawu ndi wonena za Mwana wake amene mwa umunthu wake anali wochokera mwa Davide. Iyeyu ndi amene anatsimikizidwa kukhala Mwana wa Mulungu mwamphamvu za Mzimu Woyera pamene anauka kwa akufa. Kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu, ife tinalandira chisomo chokhala atumwi oyitana anthu a mitundu yonse kuti amukhulupirire ndi kumumvera mwachikhulupiriro kuti dzina lake lilemekezedwe. Inunso muli mʼgulu la Amitundu oyitanidwawo kukhala ake a Yesu Khristu.

Ndikulembera kwa onse okhala ku Roma amene Mulungu amakukondani nakuyitanani kuti mukhale oyera mtima.

Chisomo ndi mtendere zochokera kwa Mulungu Atate athu ndi kwa Ambuye Yesu Khristu zikhale ndi inu.

Mateyu 1:18-25

Kubadwa kwa Yesu Khristu

18 Kubadwa kwa Yesu Khristu kunali motere: Amayi ake, Mariya, anapalidwa ubwenzi ndi Yosefe, koma asanagone malo amodzi, anapezeka ali woyembekezera mwana mwa mphamvu ya Mzimu Woyera. 19 Popeza Yosefe mwamuna wake anali munthu wolungama, sanafune kumuchititsa manyazi pomuleka poyera. Choncho anaganiza zomuleka mosaonetsera.

20 Koma akuganiza zimenezi, taonani, mngelo wa Ambuye anamuonekera mʼmaloto nati, “Yosefe mwana wa Davide, usaope kumutenga Mariya kukhala mkazi wako, chifukwa mwana akuyembekezerayo ndi wochokera kwa Mzimu Woyera. 21 Ndipo adzabala mwana wamwamuna, udzamutcha dzina lake Yesu; pakuti Iyeyo adzapulumutsa anthu ake ku machimo awo.”

22 Zonsezi zinachitika kukwaniritsa zimene Ambuye ananena mwa mneneri kuti, 23 “Onani namwali adzakhala woyembekezera ndipo adzabala mwana wamwamuna, ndipo mwanayo adzamutcha Imanueli,” kutanthauza kuti, “Mulungu ali nafe.”

24 Yosefe atadzuka, anachita zomwe mngelo wa Ambuye uja anamulamulira. Iye anamutenga Mariya kukhala mkazi wake. 25 Koma sanagone malo amodzi mpaka mwanayo atabadwa ndipo anamutcha dzina lake Yesu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.