Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.
80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
2 kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
bwerani ndi kutipulumutsa.
3 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
4 Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka
kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?
5 Mwawadyetsa buledi wa misozi;
mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.
6 Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,
ndipo adani athu akutinyoza.
7 Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,
mwana wa munthu amene mwalera nokha.
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;
titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.
19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
nkhope yanu itiwalire
kuti tipulumutsidwe.
23 Ndipo ndi ndani wofanana ndi anthu anu Aisraeli, mtundu wokhawo pa dziko lapansi umene Mulungu wake anapita kukawuwombola monga anthu akeake ndi kukadzitchukitsa yekha pochita zinthu zodabwitsa zazikulu, pothamangitsa mitundu ina ndi milungu yawo pamaso pa anthu ake, amene Inu munawawombola ku Igupto? 24 Inu mwawapanga anthu anu Aisraeli kukhala anuanu kwamuyaya, ndipo Inu, Inu Yehova ndinu Mulungu wawo.
25 “Ndipo tsopano Yehova Mulungu, sungani kwamuyaya lonjezo limene mwachita ndi mtumiki wanu ndi banja lake. Chitani monga mwalonjezera, 26 kotero dzina lanu lidzakhala lotchuka mpaka muyaya. Ndipo anthu adzanena kuti, ‘Yehova Wamphamvuzonse ndi Mulungu wa Israeli!’ Ndipo banja la mtumiki wanu Davide lidzakhazikika pamaso panu.
27 “Inu Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli, mwaululira mtumiki wanu ponena kuti, ‘Ine ndidzakumangira iwe nyumba!’ Nʼchifukwa chake ine mtumiki wanu ndalimba mtima kupemphera motere. 28 Inu Ambuye Wamphamvuzonse, ndinu Mulungu! Mawu anu ndi odalirika, ndipo mwalonjeza zinthu zabwinozi kwa mtumiki wanu. 29 Ndipo tsopano chikukomereni kudalitsa banja la mtumiki wanu, kuti likhale mpaka muyaya pamaso panu. Pakuti Inu, Yehova Wamphamvuzonse, mwayankhula, ndipo ndi mʼdalitso wanu banja la mtumiki wanu lidzakhala lodalitsika mpaka muyaya.”
31 “Iye wochokera kumwamba ndi wapamwamba pa onse: iye wochokera mʼdziko lapansi ndi wa dziko lapansi, ndipo amayankhula monga mmodzi wa adziko lapansi. Iye wochokera kumwamba ndi wopambana onse. 32 Iye achita umboni pa zimene waziona ndi kuzimva, koma palibe avomereza umboni wake. 33 Munthu amene amawulandira akutsimikizira kuti Mulungu ndi woona. 34 Pakuti amene Mulungu wamutuma amayankhula mawu a Mulungu; Mulungu wamupatsa Mzimu Woyera mopanda malire. 35 Atate amakonda Mwana ndipo apereka zonse mʼmanja mwake. 36 Aliyense wokhulupirira Mwanayo ali ndi moyo wosatha, koma iye amene samvera Mwanayo sadzawuona moyo, pakuti mkwiyo wa Mulungu umakhala pa iye.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.