Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.
21 Inu Yehova, mfumu ikusangalala mu mphamvu yanu,
chimwemwe chake nʼchachikuludi pa kupambana kumene mumapereka!
2 Inu mwayipatsa zokhumba za mtima wake
ndipo simunayimane zopempha za pa milomo yake.
Sela
3 Inu munayilandira ndi madalitso ochuluka
ndipo munayiveka chipewa chaufumu chagolide weniweni pa mutu wake.
4 Iye anakupemphani moyo, ndipo munamupatsa
masiku ochuluka kwamuyaya.
5 Kudzera mʼzigonjetso zimene munapereka, ulemerero wake ndi waukulu;
Inu mwapereka pa iyo ulemerero ndi ufumu.
6 Zoonadi Inu mwayipatsa madalitso amuyaya,
Inu mwayipatsa chisangalalo ndi chimwemwe chimene chili pamaso panu.
7 Pakuti mfumu imadalira Yehova;
kudzera mʼchikondi chake chosatha cha Wammwambamwamba,
iyo sidzagwedezeka.
8 Dzanja lanu lidzayimitsa adani anu onse;
dzanja lanu lamanja lidzagwira adani anu.
9 Pa nthawi ya kuonekera kwanu
mudzawasandutsa ngʼanjo yamoto yotentha.
Mu ukali wake Yehova adzawameza,
ndipo moto wake udzawatha.
10 Inu mudzawononga ana awo pa dziko lapansi,
zidzukulu zawo pakati pa anthu.
11 Ngakhale iwo akukonzereni chiwembu mwa kuchenjera kwawo
sadzapambana;
12 pakuti mudzawapirikitsa ndipo adzaonetsa misana yawo
pamene mudzawaloza ndi mivi yanu.
13 Mukwezeke Inu Yehova mʼmphamvu yanu,
ife tidzayimba nyimbo ndi kutamanda mphamvu yanu.
14 Usachite mantha, iwe Yakobo wofowoka ngati nyongolotsi,
iwe wochepa mphamvu Israeli,
chifukwa Ine ndidzakuthandiza,”
akutero Yehova Mpulumutsi wako, Woyerayo wa Israeli.
15 “Taona, ndidzakusandutsa ngati chipangizo chopunthira tirigu
chatsopano, chakunthwa ndi cha mano ambiri.
Udzanyenya mapiri ndi kuwaphwanyaphwanya,
ndipo zitunda adzazisandutsa ngati mankhusu.
16 Udzawapeta ndipo adzawuluka ndi mphepo komanso
adzamwazika ndi kamvuluvulu.
Koma iwe udzakondwera chifukwa Ine ndine Mulungu wako,
ndipo udzanyadira chifukwa cha Ine Woyerayo wa Israeli:
17 “Pamene amphawi ndi osauka akufunafuna madzi,
koma sakuwapeza;
ndipo kummero kwawo kwawuma ndi ludzu.
Ine Yehova ndidzayankha pemphero lawo;
Ine, Mulungu wa Israeli, sindidzawasiya.
18 Ndidzayendetsa mitsinje mʼmalo owuma,
ndi akasupe adzatumphuka mu zigwa.
Ndidzasandutsa chipululu kukhala dziwe la madzi
ndipo dziko lowuma kukhala akasupe a madzi.
19 Mʼchipululu ndidzameretsa
mkungudza, kasiya mchisu ndi mtengo wa Olivi.
Mʼdziko lowuma ndidzaza mitengo
ya payini, ya mkuyu ndi ya mlombwa,
20 kuti anthu aone ndi kudziwa;
inde, alingalire ndi kumvetsa,
kuti Yehova ndiye wachita zimenezi;
kuti Woyera wa Israeli ndiye anakonza zimenezi.
Paulo Mtumwi wa Anthu a Mitundu Ina
14 Abale anga, ine mwini ndikutsimikiza kuti inuyo ndinu abwino, odzaza ndi chidziwitso ndi okhoza kulangizana wina ndi mnzake. 15 Ine ndakulemberani inu molimba mtima pa fundo zina, kukhala ngati kukukumbutsaninso za zimenezo, chifukwa cha chisomo chimene Mulungu anandipatsa ine 16 kukhala mtumiki wa Khristu Yesu wa a mitundu ina ndi udindo wa wansembe, kulalikira Uthenga Wabwino wa Mulungu, kuti a mitundu ina akhale nsembe yolandiridwa kwa Mulungu, yopatsidwa ndi Mzimu Woyera.
17 Choncho, ine ndikunyadira mwa Khristu Yesu potumikira Mulungu wanga. 18 Ine sindidzayesera kuyankhula za kanthu kalikonse koma zimene Khristu wazichita kudzera mwa ine zotsogolera a mitundu ina kuti amvere Mulungu mwa zimene ndinanena ndi kuzichita 19 mwamphamvu ya zizindikiro ndi zodabwitsa kudzera mwamphamvu ya Mzimu Woyera. Choncho kuchokera ku Yerusalemu ndi kuzungulira ku Iluriko, ine ndalalikira kwathunthu Uthenga Wabwino wa Khristu. 20 Chakhala chilakolako changa nthawi zonse kuti ndilalikire Uthenga Wabwino kumene Khristu sadziwika, kuti ine ndisamange pa maziko a wina wake. 21 Koma monga kwalembedwa kuti,
“Iwo amene sanawuzidwe za Iye adzaona,
ndi iwo amene sanamve adzazindikira.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.