Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba pokwera ku Yerusalemu.
124 Akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
anene tsono Israeli,
2 akanapanda kukhala mbali yathu Yehova,
potiwukira anthuwo,
3 iwo atatipsera mtima,
akanatimeza amoyo;
4 chigumula chikanatimiza,
mtsinje ukanatikokolola,
5 madzi a mkokomo
akanatikokolola.
6 Atamandike Yehova,
amene sanalole kuti tikhale chakudya cha mano awo.
7 Moyo wathu wawonjoka ngati mbalame
yokodwa mu msampha wa mlenje;
msampha wathyoka,
ndipo ife tapulumuka.
8 Thandizo lathu lili mʼdzina la Yehova
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi.
Nowa Atuluka Mʼchombo
8 Tsono Mulungu anakumbukira Nowa ndi nyama zonse zakuthengo ndi ziweto zimene anali nazo mu chombo. Yehova anatumiza mphepo pa dziko lapansi ndipo madzi anaphwera. 2 Tsono akasupe a madzi ambiri a pansi pa dziko ndi zitseko za madzi a kumwamba zinatsekedwa, ndipo mvula inaleka kugwa. 3 Madzi amaphwabe pa dziko lapansi. Pakutha pa masiku 150, madzi anatsika, 4 ndipo pa tsiku la 17 la mwezi wachisanu ndi chiwiri, chombo chija chinakakhazikika pa mapiri a Ararati. 5 Madzi anapitirira kuphwa mpaka mwezi wa khumi, ndipo pa tsiku loyamba la mwezi wa khumiwo msonga za mapiri zinayamba kuonekera.
6 Patapita masiku makumi anayi, Nowa anatsekula zenera limene anapanga mʼchombomo 7 natulutsa khwangwala, koma khwangwalayo ankangowuluka uku ndi uku mpaka madzi anawuma pa dziko lapansi. 8 Kenaka anatulutsa nkhunda kuti aone ngati madzi aphwa pa dziko. 9 Koma nkhunda sinapeze poti nʼkutera chifukwa panali madzi ponseponse pa dziko lapansi. Choncho inabwerera kwa Nowa mʼchombo. Nowa anatulutsa dzanja lake kunja ndi kutenga nkhundayo kuyibwezera mʼchombo mmene iye anali. 10 Choncho anadikirabe masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatulutsanso nkhundayo mʼchombo muja. 11 Pamene nkhunda inabwerera madzulo ake, inali itanyamula tsamba laliwisi la mtengo wa olivi. Motero Nowa anadziwa kuti madzi aphwadi pa dziko lapansi. 12 Iye anadikira masiku ena asanu ndi awiri ndipo anatumizanso nkhunda ija, koma nthawi imeneyi sinabwererenso kwa iye.
13 Pofika tsiku loyamba la mwezi woyamba wa chaka chimene Nowa anakwanitsa zaka 601, madzi anawuma pa dziko lapansi. Ndipo Nowa anachotsa denga la chombo ndipo anaona kuti kunja kwawuma. 14 Pokwana tsiku la 27 la mwezi wachiwiri dziko lapansi linawumiratu.
15 Tsono Mulungu anawuza Nowa kuti, 16 “Iwe, mkazi wako, ana ako pamodzi ndi akazi awo tulukani mʼchombomo. 17 Tulutsa zamoyo zonse zili ndi iwe, mbalame, nyama ndi zokwawa zonse kuti ziswane ndi kuchulukana pa dziko lapansi.”
18 Nowa anatuluka pamodzi ndi ana ake aamuna, mkazi wake ndi akazi a ana ake. 19 Nyama zonse, zokwawa zonse, mbalame zonse, chilichonse choyenda pa dziko lapansi, zinatuluka mʼchombo motsogozana monga mwa mitundu yawo.
Kufa ku Tchimo, Kukhala ndi Moyo mwa Khristu
6 Nanga tinene chiyani? Kodi tipitirire kuchimwa kuti chisomo chichulukebe? 2 Ayi. Mʼnjira iliyonse! Popeza tinafa ku tchimo, nanga tidzapitirira bwanji kukhalabe mʼmenemo? 3 Kodi simukudziwa kuti tonse amene tinabatizidwa mwa Khristu Yesu tinabatizidwa mu imfa yake? 4 Chifukwa chake ife tinayikidwa mʼmanda pamodzi ndi Iye mwa ubatizo. Tinalowa mu imfa ndi cholinga choti monga momwe Khristu anaukitsidwa kwa akufa ndi ulemerero wa Atate, ifenso tikakhale mʼmoyo watsopano.
5 Pakuti ngati ife tinakhala amodzi ndi Iye mu imfa yake, tidzakhalanso ndithu amodzi ndi Iye mu kuuka kwake. 6 Ife tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapachikidwa pamodzi ndi Iye kuti thupi la uchimo likhale lopanda mphamvu ndi kuti tisakakhalenso akapolo a tchimo 7 chifukwa aliyense amene anafa anamasuka ku tchimo.
8 Koma ngati tinafa pamodzi ndi Khristu, tikhulupirira kuti tidzakhalanso ndi moyo pamodzi ndi Iye. 9 Pakuti tikudziwa kuti popeza Khristu anaukitsidwa kwa akufa, Iye sangafenso. Imfa ilibenso mphamvu pa Iye. 10 Imfa imene Iye anafa, anafa ku tchimo kamodzi kokha, koma moyo umene akhala ndi wa kwa Mulungu.
11 Kotero inunso, mudzione nokha ngati akufa ku tchimo koma a moyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.