Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 117

117 Tamandani Yehova, inu anthu a mitundu yonse;
    mulemekezeni Iye, inu mitundu ya anthu.
Pakuti chikondi chake pa ife ndi chachikulu,
    ndipo kukhulupirika kwa Yehova nʼkosatha.

Tamandani Yehova.

Yeremiya 30:18-24

18 Yehova akuti,

“Ndidzabwera nalo banja la Yakobo ku dziko lawo
    ndipo ndidzachitira chifundo malo ake okhalamo;
mzinda wa Yerusalemu udzamangidwanso pa bwinja pake,
    nyumba yaufumu idzamangidwanso pa malo pake penipeni.
19 Anthuwo adzayimba nyimbo zoyamika Yehova
    ndipo kudzamveka phokoso lachisangalalo.
Ndidzawachulukitsa,
    ndipo chiwerengero chawo sichidzatsika;
ndidzawapatsa ulemerero,
    ndipo sadzanyozedwanso.
20 Ana awo adzakhalanso monga mmene analili kale,
    ndipo gulu lawo ndidzalikhazikitsa pamaso panga;
    ndidzalanga onse owazunza.
21 Mtsogoleri wawo adzakhala mmodzi mwa iwo.
    Wodzawalamulira adzachokera pakati pawo.
Choncho ndidzawakokera kufupi ndi Ine ndipo iye adzandiyandikira.
    Ndani angalimbe mtima payekha kuyandikana nane
    popanda kuyitanidwa?”
            akutero Yehova.
22 “Choncho inu mudzakhala anthu anga,
    ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wanu.”

23 Taonani ukali wa Yehova wowomba
    ngati mphepo ya mkuntho.
Mphepo ya namondwe
    ikuwomba pa mitu ya anthu oyipa.
24 Mkwiyo woopsa wa Yehova sudzachoka
    mpaka atakwaniritsa zolinga
    za mu mtima mwake.
Mudzamvetsa zimenezi
    masiku akubwerawo.

Chivumbulutso 22:8-21

Ine Yohane, ndine amene ndinamva ndi kuona zinthu izi. Ndipo pamene ndinamva ndi kuona izi ndinagwa pansi kuti ndipembedze mngelo amene amandionetsa zimenezi. Koma mngeloyo anandiwuza kuti, “Usatero ayi! Ine ndine wotumikira monga iwe pamodzi ndi abale ako aneneri ndi onse amene amasunga mawu a mʼbuku pembedzani Mulungu.”

10 Kenaka anandiwuza kuti, “Usabise mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili chifukwa nthawi yayandikira. 11 Wochita zoyipa apitirire kuchita zoyipazo; wochita zonyansa apitirire kuchita zonyansazo; wochita zabwino apitirire kuchita zabwinozo; ndipo woyera mtima apitirire kukhala woyera mtima.”

Mawu Otsiriza: Kuyitanidwa ndi Chenjezo

12 “Taonani, ndikubwera posachedwa! Ndikubwera ndi mphotho zanga kuti ndidzapereke kwa aliyense malinga ndi zimene anachita. 13 Ine ndine Alefa ndi Omega, Woyamba ndi Wotsiriza, Chiyambi ndi Chimaliziro ndine.

14 “Odala amene achapa mikanjo yawo, kuti akhale ndi ufulu wopita ku mtengo wamoyo ndi kuti akalowe mʼzipata za mu mzindawo. 15 Kunja kuli agalu, amatsenga, achiwerewere, akupha anthu, opembedza mafano ndi aliyense amene amakonda bodza ndi kulichita.

16 “Ine Yesu, ndatuma mngelo wanga kuti achitire umboni uwu ku mipingo. Ine ndine Muzu ndi Chipatso cha Davide ndipo ndine Nthanda Yonyezimira.”

17 Mzimu Woyera ndi mkwatibwi akuti, “Bwerani!” Ndipo amene akumva anena kuti Bwerani! Iye amene ali ndi ludzu abwere, ndipo aliyense amene afuna alandire mphatso yaulere ya madzi amoyo.

18 Ndikuchenjeza aliyense amene akumva mawu onena zamʼtsogolo a mʼbukuli kuti, “Ngati wina awonjezerapo kalikonse, Mulungu adzamuwonjezera miliri imene yalembedwa mʼbuku ili. 19 Ndipo wina akachotsapo mawu onena zamʼtsogolo a mʼbuku ili, Mulungu adzachotsa gawo lake pa mtengo wamoyo ndi la mu mzinda woyera zimene zanenedwa mʼbuku ili.”

20 Iye amene akuchitira umboni pa zinthu izi akuti, “Inde, Ine ndikubwera posachedwa.”

Ameni. Bwerani Ambuye Yesu.

21 Chisomo cha Ambuye Yesu chikhale ndi anthu onse. Ameni.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.