Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Chilengedwe Chatsopano
17 “Taonani, ndikulenga
mlengalenga mwatsopano ndi dziko lapansi latsopano.
Zinthu zakale sizidzakumbukika,
zidzayiwalika kotheratu.
18 Koma inu mukhale osangalala ndi okondwa mpaka muyaya
chifukwa cha zimene ndikulenga,
pakuti ndikulenga Yerusalemu kukhala malo wosangalatsa
ndipo anthu ake adzakhala achimwemwe.
19 Ine ndidzakondwa chifuwa cha Yerusalemu
ndipo ndidzasangalala chifukwa cha anthu anga.
Kumeneko sikudzamvekanso kulira
ndi mfuwu wodandaula.
20 “Ana sadzafa ali akhanda
ndipo nkhalamba zonse zidzakwaniritsa zaka zawo zonse.
Wamngʼono mwa iwo
adzafa ali ndi zaka 100.
Amene adzalephere kufika zaka 100
adzatengedwa kukhala
wotembereredwa.
21 Anthu adzamanga nyumba ndi kukhalamo,
adzadzala mpesa ndipo adzadya zipatso zake.
22 Sadzamanganso nyumba anthu ena nʼkukhalamo,
kapena kudzala ndi ena nʼkudya.
Pakuti anthu anga adzakhala ndi moyo
wautali ngati mitengo.
Osankhidwa anga adzakondwera ndi ntchito
ya manja awo nthawi yayitali.
23 Sadzagwira ntchito pachabe
kapena kubereka ana kuti aone tsoka;
chifukwa adzakhala anthu odalitsidwa ndi Yehova,
iwowo pamodzi ndi adzukulu awo omwe.
24 Ndidzawayankha ngakhale asanathe nʼkupempha komwe.
Pamene akuyankhula kumene Ine ndidzakhala nditamva kale.
25 Mʼmbulu ndi mwana wankhosa wamkazi zidzadyera pamodzi.
Mkango udzadya udzu monga ngʼombe,
koma fumbi ndiye chidzakhale chakudya cha njoka.
Pa phiri langa lopatulika sipadzakhala
chinthu chopweteka kapena chowononga,”
akutero Yehova.
Nyimbo za Mayamiko
12 Tsiku limenelo aliyense wa inu adzati:
“Ndikukuyamikani, Inu Yehova;
chifukwa ngakhale munandipsera mtima,
mkwiyo wanu wachoka,
ndipo mwanditonthoza.
2 Zoonadi, Mulungu ndiye Mpulumutsi wanga;
ndidzamudalira ndipo sindidzachita mantha.
Yehova ndiye mphamvu yanga ndi nyimbo yanga;
Iye wakhala chipulumutso changa.”
3 Mudzakondwera popeza Yehova
ali ngati chitsime cha chipulumutso chanu.
4 Tsiku limenelo mudzati:
“Yamikani Yehova, tamandani dzina lake;
mulengeze ntchito zake pakati pa mitundu ya anthu,
ndipo mulalike kuti dzina lake ndi lopambana.
5 Imbirani Yehova, pakuti wachita ntchito zazikulu;
zimenezi zidziwike pa dziko lonse lapansi.
6 Fuwulani ndi kuyimba mwachimwemwe, inu anthu a ku Ziyoni;
pakuti Woyerayo wa Israeli ndi wamkulu pakati panu.”
Awachenjeza za Kusagwira Ntchito
6 Abale, tikukulamulani mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, kuti mupewe mʼbale aliyense amene ndi waulesi ndi wachisokonezo, wosafuna kutsata zimene tinakuphunzitsani. 7 Pakuti inu mukudziwa zimene muyenera kuchita pofuna kutitsatira. Ife sitinali alesi pamene tinali nanu 8 ndipo sitinadye chakudya cha aliyense osalipira. Komatu tinkagwira ntchito mwamphamvu usiku ndi usana kuti tisakhale cholemetsa kwa aliyense. 9 Sitinachite zimenezi chifukwa choti tinalibe mphamvu zolamula kuti mutithandize koma kuti tikhale chitsanzo choti mutsatire. 10 Pakuti ngakhale pamene tinali nanu, tinakupatsani lamulo lakuti, “Munthu wosafuna kugwira ntchito, asadye.”
11 Ife tikumva kuti pakati panu pali ena amene ndi alesi. Iwo safuna kugwira ntchito, koma amangolowerera pa za eni. 12 Mʼdzina la Ambuye Yesu Khristu, tikuwalamula ndi kuwakakamiza kuti azigwira ntchito mwabata ndi kumadya chakudya chodzigwirira ntchito okha. 13 Koma inu abale, musatope nʼkuchita zabwino.
Zizindikiro za Masiku Otsiriza
5 Ena mwa ophunzira ake ankachita ndemanga za mmene Nyumba ya Mulungu anayikongoletsera ndi miyala yokongola ndiponso zinthu zina zomwe anthu anapereka kwa Mulungu. Koma Yesu anati, 6 “Koma zimene mukuziona panozi, nthawi idzafika pamene ngakhale mwala umodzi omwe sudzakhala pa unzake; uliwonse udzagwetsedwa pansi.”
7 Iwo anafunsa kuti, “Aphunzitsi, kodi zonsezi zidzachitika liti? Ndipo tidzaonera chiyani kuti zili pafupi kuchitika?”
8 Iye anayankha kuti, “Chenjerani kuti musanyengedwe. Pakuti ambiri adzabwera mʼdzina langa nadzati ‘Ine ndine Iye’ ndi kuti ‘Nthawi yayandikira.’ Musadzawatsate iwo. 9 Mukadzamva zankhondo ndi zipolowe, musadzachite mantha. Zinthu izi ziyenera kuchitika poyamba, koma chimaliziro sichidzafika nthawi yomweyo.”
10 Kenaka anawawuza kuti, “Mtundu wa anthu udzawukirana ndi mtundu wina, ndi ufumu kuwukira ufumu wina. 11 Kudzakhala zivomerezi zazikulu, njala ndi miliri mʼmalo osiyanasiyana, ndi zinthu zoopsa ndi zizindikiro zamphamvu kuchokera kumwamba.
12 “Koma zonsezi zisanachitike, adzakugwirani ndi kukuzunzani. Adzakuperekani ku masunagoge ndi ku ndende, ndipo adzakutengerani pamaso pa mafumu ndi olamulira, ndipo zonsezi zidzachitika chifukwa cha dzina langa. 13 Umenewu udzakhala mwayi wanu ochitira umboni. 14 Koma tsimikizani mtima kuti musadzade nkhawa za momwe mudzadzitchinjirizire. 15 Pakuti Ine ndidzakupatsani mawu ndi nzeru kotero kuti palibe mmodzi wa adani anu adzathe kuwakana kapena kuwatsutsa. 16 Inu mudzaperekedwa ndi makolo anu, abale, anansi ndi abwenzi anu ndipo ena mwa inu adzakuphani. 17 Anthu onse adzakudani chifukwa cha Ine. 18 Koma palibe tsitsi limodzi la mʼmutu mwanu lidzawonongeke. 19 Mukadzalimbikira ndiye mudzapeze moyo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.