Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la matamando la Davide.
145 Ndidzakukwezani Mulungu wanga, Mfumu yanga;
ndidzatamanda dzina lanu ku nthawi za nthawi.
2 Ndidzakutamandani tsiku ndi tsiku
ndi kulemekeza dzina lanu ku nthawi za nthawi.
3 Yehova ndi wamkulu ndi woyenera matamando onse;
ukulu wake palibe angawumvetsetse.
4 Mʼbado wina udzayamikira ntchito yanu kwa mʼbado wina;
Iwo adzafotokoza za machitidwe anu amphamvu.
5 Adzayankhula ulemerero wokongola waufumu wanu,
ndipo ine ndidzalingalira za ntchito zanu zodabwitsa.
17 Yehova ndi wolungama mʼnjira zake zonse,
ndi wokonda zonse zimene anazipanga.
18 Yehova ali pafupi ndi onse amene amamuyitana,
onse amene amamuyitana Iye mʼchoonadi.
19 Iye amakwaniritsa zokhumba za iwo amene amamuopa;
amamva kulira kwawo ndi kuwapulumutsa.
20 Yehova amayangʼana onse amene amamukonda
koma adzawononga anthu onse oyipa.
21 Pakamwa panga padzayankhula zotamanda Yehova.
Cholengedwa chilichonse chitamande dzina lake loyera
ku nthawi za nthawi.
Chipewa Chaufumu cha Yoswa
9 Yehova anayankhula nane kuti, 10 “Landira mphatso kuchokera kwa anthu amene abwera ku ukapolo, Helidai, Tobiya ndi Yedaya, amene achokera ku Babuloni. Tsiku lomwelo pita ku nyumba ya Yosiya mwana wa Zefaniya. 11 Tenga siliva ndi golide upange chipewa chaufumu, ndipo uchiyike pamutu pa mkulu wa ansembe, Yoswa mwana wa Yehozadaki. 12 Muwuze kuti zimene akunena Yehova Wamphamvuzonse ndi izi: ‘Taonani, munthu wotchedwa Nthambi ndi ameneyu, ndipo adzaphuka pomwe alipo ndi kumanga Nyumba ya Yehova. 13 Ndiye amene adzamange Nyumba ya Yehova, adzalandira ulemerero waufumu ndipo adzalamulira pa mpando wake waufumu. Adzakhalanso wansembe pa mpando wake waufumu. Ndipo padzakhala mtendere.’ 14 Chipewa cha ufumucho adzachipereka kwa Helemu, Tobiya, Yedaya, ndi kwa Heni mwana wa Zefaniya, kuti chikhale chikumbutso mʼNyumba ya Yehova. 15 Anthu okhala kutali adzabwera kudzathandiza kumanga Nyumba ya Yehova, ndipo iwe udzadziwa kuti Yehova Wamphamvuzonse wandituma kwa iwe. Zimenezi zidzachitika ngati mudzamvera mwachangu Yehova Mulungu wanu.”
10 Bwanamkubwayo atakodola Paulo ndi kulola kuti ayankhule, Pauloyo anati, “Ine ndikudziwa kuti inu mwakhala mukuweruza dziko lino zaka zambiri, kotero ndikukondwera kuti ndikudziteteza ndekha pamaso panu. 11 Inu mukhoza kupeza umboni wake. Sipanapite masiku khumi ndi awiri chipitireni changa ku Yerusalemu kukapembedza. 12 Amene akundiyimba mlanduwa sanandipeze mʼNyumba ya Mulungu ndi kutsutsana ndi wina aliyense kapena kuyambitsa chisokonezo mʼsunagoge kapena pena paliponse mu mzindamo. 13 Ndipo sangathe kupereka umboni wa mlandu umene akundiyimba inewu. 14 Komatu ine ndikuvomera kuti ndimapembedza Mulungu wa makolo athu, monga wotsatira wa Njirayo, imene iwo akuyitchula mpatuko. Ine ndimakhulupirira chilichonse chimene chimagwirizana ndi malamulo ndiponso zimene zinalembedwa ndi Aneneri. 15 Ine ndili nacho chiyembekezo chomwecho chimene iwo ali nacho mwa Mulungu, kuti kudzakhala kuuka kwa akufa kwa olungama ndiponso kwa ochimwa. 16 Kotero ine ndimayesetsa kuti ndikhale ndi chikumbumtima chosanditsutsa pamaso pa Mulungu ndi anthu onse.
17 “Patapita zaka zambiri, ndinabwera ku Yerusalemu kudzapereka mphatso kwa anthu osauka a mtundu wanga komanso kudzapereka nsembe. 18 Pamene ndinkachita zimenezi, iwo anandipeza mʼbwalo la Nyumba ya Mulungu nditachita mwambo wodziyeretsa. Panalibe gulu la anthu kapena kuti ndimachita za chisokonezo chilichonse. 19 Koma pali Ayuda ena ochokera ku Asiya, amene amayenera kukhala pano pamaso panu, kundiyimba mlandu ngati ali ndi kalikonse konditsutsa ine. 20 Kapena awa amene ali panowa anene mlandu umene anapeza mwa ine, pamene ndinayima pamaso pa Bwalo lawo Lalikulu. 21 Koma cholakwa changa chingathe kukhala chokhachi chakuti, nditayima pamaso pawo ndinafuwula kuti, ‘Mukundiweruza ine lero chifukwa ndimakhulupirira kuti akufa adzauka.’ ”
22 Kenaka Felike, amene amadziwa bwino za Njirayo, anayamba wayimitsa mlanduwo, nati, “Ndidzagamula mlandu wako akabwera mkulu wa asilikali Lusiya.” 23 Iye analamulira woyangʼanira asilikali 100 kuti alondere Paulo, koma azimupatsako ufulu ndiponso kulola abwenzi ake kuti adzimusamalira.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.