Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Habakuku 1:1-4

Uthenga umene mneneri Habakuku analandira mʼmasomphenya.

Dandawulo la Habakuku

Kodi inu Yehova, ndidzakhala ndikukupemphani thandizo kwa nthawi yayitali motani,
    koma wosayankha?
Kapena kufuwulira kwa inu kuti, “Chiwawa kuno!”
    koma wosatipulumutsa?
Chifukwa chiyani mukundionetsa zinthu zoyipa?
    Chifukwa chiyani mukundionetsa mavutowa?
Ndikuona chiwonongeko ndi chiwawa;
    pali ndewu ndi kukangana kwambiri.
Kotero malamulo anu atha mphamvu,
    ndipo chilungamo sichikugwira ntchito.
Anthu oyipa aposa olungama,
    kotero apotoza chilungamo.

Habakuku 2:1-4

Ndidzakhala pa malo anga aulonda,
    ndi kuyima pa mitumbira ya nkhondo;
ndidzadikira kuti ndimve zimene Iye adzandiwuze,
    ndi yankho limene ndidzapatsidwe pa madandawulo anga.

Yankho la Yehova

Tsono Yehova anandiyankha, nati:

“Lemba masomphenyawa
    ndipo uwalembe mooneka bwino pa mapale
    kuti wowerenga awawerenge mosavuta.
Pakuti masomphenyawa akudikira nthawi yake;
    masomphenyawa akunena zamʼtsogolo
    ndipo sizidzalephera kuchitika.
Ngakhale achedwe kukwaniritsidwa, uwayembekezere;
    zidzachitika ndithu ndipo sadzachedwa.

“Taona, mdani wadzitukumula;
    zokhumba zake sizowongoka,
    koma wolungama adzakhala ndi moyo mwachikhulupiriro.

Masalimo 119:137-144

Tsade

137 Yehova ndinu wolungama,
    ndipo malamulo anu ndi abwino.
138 Maumboni amene munatipatsa ndi olungama;
    ndi odalirika ndithu.
139 Ndikusautsidwa kwambiri mʼkati mwanga
    chifukwa adani anu amanyalanyaza mawu anu.
140 Mawu anu ndi woyera kwambiri
    nʼchifukwa chake mtumiki wanune ndimawakonda.
141 Ngakhale ndili wamngʼono ndi wonyozeka,
    sindiyiwala malangizo anu.
142 Chilungamo chanu nʼchamuyaya,
    ndipo malamulo anu nʼchoona.
143 Mavuto ndi masautso zandigwera,
    koma ndimakondwera ndi malamulo anu.
144 Umboni wanu ndi wabwino nthawi zonse;
    patseni nzeru zomvetsa zinthu kuti ine ndikhale ndi moyo.

2 Atesalonika 1:1-4

Paulo, Silivano ndi Timoteyo.

Kulembera mpingo wa ku Tesalonika, umene uli mwa Mulungu Atate athu ndi Ambuye Yesu Khristu.

Chisomo ndi mtendere kwa inu kuchokera kwa Mulungu Atate ndi Ambuye Yesu Khristu.

Kuyamika ndi Pemphero

Ife tiyenera kuyamika Mulungu nthawi zonse chifukwa cha inu abale. Ndipo tiyenera kutero chifukwa chikhulupiriro chanu chikukulirakulirabe, ndiponso chikondi chimene aliyense wa inu ali nacho pa mnzake chikuchulukirachulukirabe. Nʼchifukwa chake, timayankhula monyadira mʼmipingo yonse ya Mulungu za kupirira kwanu ndi chikhulupiriro chanu pakati pa masautso onse ndi mayesero amene mukudutsamo.

2 Atesalonika 1:11-12

11 Nʼchifukwa chake timakupemphererani nthawi zonse, kuti Mulungu wathu akusandutseni oyenera mayitanidwe ake, ndi kuti mwa mphamvu zake akwaniritse cholinga chanu chilichonse chabwino ndi chilichonse chochitika mwachikhulupiriro. 12 Ife timapempherera zimenezi kuti dzina la Ambuye athu Yesu lilemekezedwe mwa inu, ndi inu mulemekezedwe mwa Iyeyo. Zonsezi zidzachitika chifukwa cha chisomo cha Mulungu wathu ndi Ambuye Yesu Khristu.

Luka 19:1-10

Zakeyu Apulumutsidwa

19 Yesu analowa mu Yeriko napitirira. Kunali munthu kumeneko dzina lake Zakeyu; iye anali mkulu wa wolandira msonkho ndipo anali wolemera. Iye ankafuna kuona Yesu kuti ndani, koma pokhala wamfupi sanathe chifukwa cha gulu la anthu. Choncho iye anathamangira patsogolo ndipo anakwera mu mtengo wamkuyu kuti amuone Iye, pakuti Yesu ankadutsa njira imeneyo.

Yesu atafika pa malopo, anayangʼana mmwamba ndipo anati kwa iye, “Zakeyu, tsika msangamsanga. Ine ndiyenera kukhala mʼnyumba mwako lero.” Ndipo nthawi yomweyo anatsika ndipo anamulandira mosangalala.

Anthu onse ataona zimenezi anayamba kungʼungʼudza, nati, “Iye akupita kuti akakhale mlendo wa wochimwa.”

Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.”

Yesu anati kwa iye, “Lero chipulumutso chafika mʼnyumba ino, chifukwa munthu uyu nayenso ndi mwana wa Abrahamu. 10 Pajatu Mwana wa Munthu anabwera kudzafunafuna ndi kupulumutsa chotayikacho.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.