Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Ana a Kora.
87 Iye wakhazikitsa maziko ake pa phiri loyera;
2 Yehova amakonda zipata za Ziyoni
kupambana malo onse okhalamo a Yakobo.
3 Za ulemerero wako zimakambidwa,
Iwe mzinda wa Mulungu:
Sela
4 “Ndidzanena za Rahabe ndi Babuloni
pakati pa iwo amene amandidziwa.
Dzikonso la Filisitiya, Turo pamodzi ndi Kusi,
ndipo ndidzati, ‘Uyu anabadwira mʼZiyoni.’ ”
5 Ndithudi, za Ziyoni adzanena kuti,
“Uyu ndi uyo anabadwira mwa iye,
ndipo Wammwambamwamba adzakhazikitsa iyeyo.”
6 Yehova adzalemba mʼbuku la kawundula wa anthu a mitundu ina:
“Uyu anabadwira mʼZiyoni.”
Sela
7 Oyimba ndi ovina omwe adzati,
“Akasupe anga onse ali mwa iwe.”
Kuweruzidwa kwa Mitundu ya Anthu
3 “Masiku amenewo ndiponso nthawi imeneyo,
nditadzabwezeretsanso Yerusalemu ndi Yuda mʼchimake,
2 ndidzasonkhanitsa anthu a mitundu yonse
ndipo ndidzawabweretsa ku Chigwa cha Yehosafati.
Kumeneko ndidzawaweruza
chifukwa cha cholowa changa, anthu anga Aisraeli,
pakuti anabalalitsa anthu anga pakati pa mitundu ya anthu
ndikugawa dziko langa.
3 Anagawana anthu anga pochita maere
ndipo anyamata anawasinthanitsa ndi akazi achiwerewere;
anagulitsa atsikana chifukwa cha vinyo
kuti iwo amwe.
4 “Kodi tsopano inu a ku Turo ndi Sidoni ndi madera onse a Filisitiya, muli ndi chiyani chotsutsana nane? Kodi mukundibwezera pa zinthu zimene ndakuchitirani? Ngati inu mukundibwezera, Ine ndidzabwezera zochita zanu mofulumira ndi mwachangu pa mitu yanu. 5 Pakuti munatenga siliva ndi golide wanga ndi kupita nacho chuma changa chamtengowapatali ku nyumba zanu zopembedzera mafano. 6 Inu munagulitsa anthu a ku Yuda ndi Yerusalemu kwa Agriki, kuti apite kutali ndi malire a dziko lawo.
7 “Taonani, Ine ndidzawachotsa kumalo kumene munawagulitsako, ndipo ndidzabwezera zimene mwachita pa mitu yanu. 8 Ndidzagulitsa ana anu aamuna ndi ana anu aakazi kwa anthu a ku Yuda, ndipo iwo adzawagulitsa kwa Aseba, mtundu wa anthu okhala kutali.” Yehova wayankhula.
Kumva Zowawa Chifukwa cha Chikhristu
12 Abale okondedwa musadabwe ndi mayesero owawa amene mukukumana nawo ngati kuti china chake chachilendo chakuchitikirani. 13 Koma kondwerani popeza mukumva zowawa pamodzi ndi Khristu, kuti mudzakondwere kwakukulu pamene ulemerero wake udzaonekera. 14 Ngati akuchitani chipongwe chifukwa cha dzina la Khristu, ndinu odala, ndiye kuti Mzimu waulemerero wa Mulungu uli pa inu. 15 Ngati mumva zowawa, zisakhale chifukwa cha kupha munthu, kapena kuba, kapena kuchita choyipa, kapena kulowerera za anthu ena, 16 koma ngati mumva zowawa chifukwa ndinu Mkhristu, musachite manyazi, koma muyamike Mulungu chifukwa cha dzinalo. 17 Pakuti nthawi yafika kuti chiweruzo chiyambe mʼnyumba ya Mulungu, ndipo ngati chiyamba ndi ife nanga podzafika kwa osamvera Uthenga Wabwino wa Mulungu, chidzakhala chotani? 18 Monga Malemba akuti,
“Ngati kuli kovuta kuti olungama apulumuke,
nanga munthu wochimwa, wosasamala za Mulungu adzatani?”
19 Nʼchifukwa chake, iwo amene akumva zowawa monga mwa chifuniro cha Mulungu, adzipereke okha mʼmanja mwa Mlengi wawo wokhulupirika ndi kumapitiriza kuchita zabwino.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.