Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 65

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Nyimbo.

65 Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni;
    kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.
Inu amene mumamva pemphero,
    kwa inu anthu onse adzafika.
Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo,
    Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
Odala iwo amene inu muwasankha
    ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu!
Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu,
    za mʼNyumba yanu yoyera.

Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo,
    Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi
    ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu,
    mutadziveka nokha ndi mphamvu.
Amene munakhalitsa bata nyanja
    kukokoma kwa mafunde ake,
    ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu;
    kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera.
    Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.

Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira;
    Inuyo mumalilemeretsa kwambiri.
Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi
    kuti upereke tirigu kwa anthu,
    pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
10 Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake,
    mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
11 Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka,
    ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
12 Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira;
    mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
13 Madambo akutidwa ndi zoweta
    ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu;
    izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.

Yoweli 2:1-11

Chilango cha Mulungu

Lizani lipenga mu Ziyoni.
    Chenjezani pa phiri langa loyera.
Onse okhala mʼdziko anjenjemere,
    pakuti tsiku la Yehova likubwera,
layandikira;
    tsiku la mdima ndi chisoni,
    tsiku la mitambo ndi la mdima wandiweyani.
Ngati mʼbandakucha umene wakuta mapiri,
    gulu lalikulu ndi la ankhondo amphamvu likubwera,
gulu limene nʼkale lomwe silinaonekepo
    ngakhale kutsogolo kuno silidzaonekanso.
Patsogolo pawo moto ukupsereza,
    kumbuyo kwawo malawi amoto akutentha zinthu.
Patsogolo pawo dziko lili ngati munda wa Edeni,
    kumbuyo kwawo kuli ngati chipululu,
    kulibe kanthu kotsalapo.
Maonekedwe awo ali ngati akavalo;
    akuthamanga ngati akavalo ankhondo.
Akulumpha pamwamba pa mapiri
    ndi phokoso ngati la magaleta,
ngati moto wothetheka wonyeketsa ziputu,
    ngati gulu lalikulu la ankhondo lokonzekera nkhondo.

Akangowaona, anthu a mitundu ina amazunzika mu mtima;
    nkhope iliyonse imagwa.
Amathamanga ngati ankhondo;
    amakwera makoma ngati asilikali.
Onse amayenda pa mizere,
    osaphonya njira yawo.
Iwo sakankhanakankhana,
    aliyense amayenda molunjika.
Amadutsa malo otchingidwa
    popanda kumwazikana.
Amakhamukira mu mzinda,
    amathamanga mʼmbali mwa khoma.
Amakwera nyumba ndi kulowamo;
    amalowera pa zenera ngati mbala.

10 Patsogolo pawo dziko limagwedezeka,
    thambo limanjenjemera,
dzuwa ndi mwezi zimachita mdima,
    ndipo nyenyezi zimaleka kuwala.
11 Yehova amabangula
    patsogolo pawo,
gulu lake lankhondo ndi losawerengeka,
    ndipo amphamvu ndi amene amamvera kulamula kwake.
Tsiku la Yehova ndi lalikulu;
    ndi loopsa.
    Ndani adzapirira pa tsikulo?

2 Timoteyo 3:10-15

Paulo Alimbikitsa Timoteyo

10 Tsono iwe, umadziwa zonse zimene ndimaphunzitsa, makhalidwe anga, cholinga changa, chikhulupiriro changa, kuleza mtima kwanga, chikondi changa, ndi kupirira kwanga, 11 mazunzo anga, masautso anga, monga zinandichitikira ku Antiokeya, ku Ikoniya ndi ku Lusitra. Ndinazunzika kwambiri. Koma Ambuye anandipulumutsa pa zonsezi. 12 Kunena zoona, munthu aliyense amene akufuna kukhala moyo wolemekeza Mulungu mwa Khristu Yesu, adzazunzikadi, 13 pomwe anthu oyipa ndi onyenga adzanka nayipirayipira, kunamiza ena, iwo nʼkumanamizidwanso. 14 Koma iwe pitiriza zimene waziphunzira ndi kuzivomereza, chifukwa ukudziwa amene anakuphunzitsa zimenezi. 15 Kuyambira uli wamngʼono wakhala ukudziwa Malemba Oyera, amene akhoza kukupatsa nzeru zokupulumutsa kudzera mʼchikhulupiriro cha mwa Yesu Khristu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.