Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Nyimbo.
65 Matamando akudikira Inu Mulungu mu Ziyoni;
kwa inu malumbiro athu adzakwaniritsidwa.
2 Inu amene mumamva pemphero,
kwa inu anthu onse adzafika.
3 Pamene tinathedwa nzeru ndi machimo,
Inu munakhululukira mphulupulu zathu.
4 Odala iwo amene inu muwasankha
ndi kuwabweretsa pafupi kukhala mʼmabwalo anu!
Ife tadzazidwa ndi zinthu zabwino za mʼNyumba mwanu,
za mʼNyumba yanu yoyera.
5 Mumatiyankha ife ndi ntchito zodabwitsa zachilungamo,
Inu Mulungu Mpulumutsi wathu,
chiyembekezo cha mathero onse a dziko lapansi
ndi cha nyanja zomwe zili kutali kwambiri,
6 amene munapanga mapiri ndi mphamvu zanu,
mutadziveka nokha ndi mphamvu.
7 Amene munakhalitsa bata nyanja
kukokoma kwa mafunde ake,
ndi phokoso la anthu a mitundu ina.
8 Iwo amene akukhala kutali amaopa zizindikiro zozizwitsa zanu;
kumene dzuwa limatulukira ndi kumene dzuwa limalowera.
Inu mumafuna nyimbo zachimwemwe.
9 Inu mumasamalira dziko lapansi ndi kulithirira;
Inuyo mumalilemeretsa kwambiri.
Mtsinje wa Mulungu ndi wodzaza ndi madzi
kuti upereke tirigu kwa anthu,
pakuti Inu munakhazikitsa zimenezi.
10 Mwadzaza nthaka yake ndi madzi ndi kusalaza migula yake,
mwayifewetsa ndi mvula yamawawa ndi kudalitsa mbewu zake.
11 Inu mumaveka chaka ndi zinthu zochuluka,
ndipo ngolo zanu zimasefukira ndi zinthu zochuluka.
12 Malo a udzu a mʼchipululu amasefukira;
mapiri avekedwa ndi chisangalalo.
13 Madambo akutidwa ndi zoweta
ndi zigwa zavekedwa ndi tirigu;
izo pamodzi zikufuwula ndi kuyimba mwachimwemwe.
1 Yehova anayankhula ndi Yoweli mwana wa Petueli.
Kubwera kwa Dzombe
2 Inu akuluakulu, imvani izi;
mvetserani, nonse amene mumakhala mʼdziko.
Kodi zinthu zokhala ngati izi zinayamba zaonekapo mʼnthawi yanu,
kapena mʼnthawi ya makolo anu?
3 Muwafotokozere ana anu,
ndipo ana anuwo afotokozere ana awo,
ndipo ana awo adzafotokozere mʼbado winawo.
4 Chimene dzombe losamera mapiko lasiya
dzombe lowuluka ladya;
chimene dzombe lowuluka lasiya
dzombe lalingʼono ladya;
chimene dzombe lalingʼono lasiya
chilimamine wadya.
5 Dzukani, inu zidakwa ndipo mulire!
Lirani mofuwula, inu nonse amene mumamwa vinyo;
lirani mofuwula chifukwa cha vinyo watsopano,
pakuti wachotsedwa pakamwa panu.
6 Mtundu wa anthu wathira nkhondo dziko langa,
wamphamvu ndi wosawerengeka;
uli ndi mano a mkango,
zibwano za mkango waukazi.
7 Wawononga mphesa zanga
ndipo wathyola mitengo yanga ya mkuyu.
Wakungunula makungwa ake
ndi kuwataya,
kusiya nthambi zake zili mbee.
8 Lirani ngati namwali wovala chiguduli,
chifukwa cha mwamuna wa utsikana wake.
9 Chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
sizikuperekedwa ku nyumba ya Yehova.
Ansembe akulira,
amene amatumikira pamaso pa Yehova.
10 Minda yaguga,
nthaka yauma;
tirigu wawonongeka,
vinyo watsopano watha,
mitengo ya mafuta yauma.
11 Khalani ndi nkhawa, inu alimi,
lirani mofuwula inu alimi a mphesa;
imvani chisoni chifukwa cha tirigu ndi barele,
pakuti zokolola za mʼmunda zawonongeka.
12 Mpesa wauma
ndipo mtengo wamkuyu wafota;
makangadza, kanjedza ndi mitengo ya apulosi,
mitengo yonse ya mʼmunda yauma.
Ndithudi chimwemwe cha anthu
chatheratu.
Mulungu Ayitana Anthu kuti Atembenuke
13 Inu ansembe, valani ziguduli ndipo lirani;
lirani mofuwula, inu amene mumatumikira pa guwa lansembe.
Bwerani, fundani ziguduli usiku wonse,
inu amene mumatumikira pamaso pa Mulungu wanga;
pakuti chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa
sizikupezekanso mʼnyumba ya Mulungu wanu.
14 Lengezani tsiku lopatulika losala zakudya,
itanani msonkhano wopatulika.
Sonkhanitsani akuluakulu
ndi anthu onse okhala mʼdziko
ku nyumba ya Yehova Mulungu wanu
ndipo alirire Yehova.
15 Kalanga ine tsikulo!
Pakuti tsiku la Yehova layandikira;
lidzabwera ngati chiwonongeko chochokera kwa Wamphamvuzonse.
16 Kodi chakudya chathu sichachotsedwa
ife tikuona?
Kodi mʼnyumba ya Mulungu wathu
simulibe chimwemwe ndi chisangalalo?
17 Mbewu zikunyala
poti pansi ndi powuma.
Nyumba zosungiramo zinthu zawonongeka;
nkhokwe zapasuka
popeza tirigu wauma.
18 Taonani mmene zikulirira ziweto;
ngʼombe zikungoyenda uku ndi uku
chifukwa zilibe msipu;
ngakhalenso nkhosa zikusauka.
19 Kwa Inu Yehova ndilirira,
pakuti moto wapsereza msipu wakuthengo,
malawi amoto apsereza mitengo yonse ya mʼtchire.
20 Ngakhale nyama zakuthengo zikulirira Inu;
timitsinje tonse taphwa
ndipo moto wapsereza msipu wa kuthengo.
Zoopsa za Mʼmasiku Otsiriza
3 Koma dziwa izi: Mʼmasiku otsiriza kudzafika nthawi zoopsa kwambiri. 2 Anthu adzakhala odzikonda, okonda ndalama, odzitama, onyada, achipongwe, osamvera makolo awo, osayamika, wopanda chiyero. 3 Adzakhala wopanda chikondi, osakhululuka, osinjirira, osadziletsa, ankhanza, osakonda zabwino, 4 opereka anzawo kwa adani awo, osaopa zoyipa, odzitukumula, okonda zowasangalatsa mʼmalo mokonda Mulungu. 5 Adzakhala ndi maonekedwe achipembedzo koma mphamvu yake ndi kumayikana. Anthu amenewa uziwapewa.
6 Iwowa ndi anthu aja amene amayendayenda mʼmakomo a anthu nʼkumanyenga akazi ofowoka mʼmaganizo, olemedwa ndi machimo ndiponso otengeka ndi zilakolako zoyipa zamitundumitundu, 7 amaphunzira nthawi zonse koma samatha kuzindikira choonadi. 8 Monga momwe Yanesi ndi Yambere anawukira Mose, momwemonso anthu amenewa amawukira choonadi. Nzeru zawo ndi zowonongeka ndipo pa za chikhulupiriro, ndi okanidwa. 9 Koma sadzapita nazo patali kwambiri zimenezi, pakuti anthu onse adzaona kupusa kwawo monga anachitira Yanesi ndi Yambere.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.