Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Memu
97 Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu!
Ndimalingaliramo tsiku lonse.
98 Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga,
popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.
99 Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse
popeza ndimalingalira umboni wanu.
100 Ndili ndi nzeru zochuluka zomvetsera zinthu kuposa anthu okalamba,
popeza ndimamvera malangizo anu.
101 Ndimaletsa miyendo yanga kuyenda mʼnjira iliyonse yoyipa
kuti ndithe kumvera mawu anu.
102 Sindinapatuke kuchoka pa malamulo anu,
pakuti Inu mwini munandiphunzitsa.
103 Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa,
otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!
104 Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu;
kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.
15 Yehova akuti,
“Kulira kukumveka ku Rama,
kulira kwakukulu,
Rakele akulirira ana ake.
Sakutonthozeka
chifukwa ana akewo palibe.”
16 Yehova akuti,
“Leka kulira
ndi kukhetsa misozi
pakuti udzalandira mphotho ya ntchito yako,”
akutero Yehova.
“Iwo adzabwerako ku dziko la adani.
17 Tsono chiyembekezo chilipo pa zamʼtsogolo,”
akutero Yehova.
“Ana ako adzabwerera ku dziko lawo.
18 “Ndithu ndamva Efereimu akubuwula kuti,
‘Ife tinali ngati ana angʼombe osamva.
Koma inu mwatiphunzitsa kumvera.
Mutibweze kuti tithe kubwerera,
chifukwa ndinu Yehova Mulungu wanga.
19 Popeza tatembenuka mtima,
ndiye tikumva chisoni;
popeza tazindikira
ndiye tikudziguguda pachifukwa.
Tachita manyazi ndipo tanyazitsidwa
chifukwa tinachimwa paubwana wathu.’
20 Kodi Efereimu si mwana wanga wokondedwa,
mwana amene Ine ndimakondwera naye?
Ngakhale nthawi zambiri ndimamudzudzula,
ndimamukumbukirabe.
Kotero mtima wanga ukumufunabe;
ndimamumvera chifundo chachikulu kwambiri,”
akutero Yehova.
21 “Muyike zizindikiro za mu msewu;
muyimike zikwangwani.
Yangʼanitsitsani msewuwo,
njira imene mukuyendamo.
Bwerera, iwe namwali wa Israeli,
bwerera ku mizinda yako ija.
22 Udzakhala jenkha mpaka liti,
iwe mwana wa mkazi wosakhulupirika?
Yehova walenga chinthu chatsopano pa dziko lapansi; mkazi ndiye tsopano aziteteza mwamuna.”
23 Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti, “Ndikadzabwera nawo anthuwa kuchokera ku ukapolo, anthu a mʼdziko la Yuda ndi amene akukhala mʼmizinda yake adzayankhulanso mawu akuti, ‘Yehova akudalitse, iwe malo achilungamo, iwe phiri lopatulika.’ 24 Anthu adzakhala ku Yuda ndi ku mizinda yake pamodzi ndi alimi ndi oweta nkhosa. 25 Ndidzatsitsimutsa anthu otopa ndipo ndidzadyetsa anthu anjala.”
26 Pamenepo ndinadzuka nʼkuyangʼana uku ndi uku. Tulo tanga tinali tokoma.
Bartumeyu Wosaona
46 Ndipo anafika ku Yeriko. Pamene Yesu ndi ophunzira ake, pamodzi ndi gulu lalikulu la anthu, ankatuluka mu mzinda, munthu wosaona, Bartumeyu (mwana wa Tumeyu), amakhala mʼmbali mwa msewu ali kupempha. 47 Pamene anamva kuti anali Yesu wa ku Nazareti, anayamba kufuwula kuti, “Yesu, Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
48 Ambiri anamukalipira ndi kumuwuza kuti akhale chete, koma iye anafuwulitsabe kuti, “Mwana wa Davide, mundichitire chifundo!”
49 Yesu anayima nati, “Muyitaneni.” Ndipo anamuyitana kuti, “Kondwera! Imirira! Akukuyitana.” 50 Anaponya mkanjo wake kumbali, analumpha nabwera kwa Yesu.
51 Yesu anamufunsa kuti, “Ukufuna ndikuchitire chiyani?”
Wosaonayo anayankha kuti, “Aphunzitsi, ndikufuna ndione.”
52 Yesu anati, “Pita, chikhulupiriro chako chakuchiritsa!” Nthawi yomweyo anapenya, nʼkumatsatira Yesu pa ulendowo.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.