Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 119:97-104

Memu

97 Ndithu, ine ndimakonda malamulo anu!
    Ndimalingaliramo tsiku lonse.
98 Malamulo anu amachititsa kuti ndikhale wanzeru kuposa adani anga,
    popeza malamulowo ali ndi ine nthawi zonse.
99 Ndimamvetsa zinthu kwambiri kuposa aphunzitsi anga onse
    popeza ndimalingalira umboni wanu.
100 Ndili ndi nzeru zochuluka zomvetsera zinthu kuposa anthu okalamba,
    popeza ndimamvera malangizo anu.
101 Ndimaletsa miyendo yanga kuyenda mʼnjira iliyonse yoyipa
    kuti ndithe kumvera mawu anu.
102 Sindinapatuke kuchoka pa malamulo anu,
    pakuti Inu mwini munandiphunzitsa.
103 Mawu anu ndi otsekemera ndikawalawa,
    otsekemera kuposa uchi mʼkamwa mwanga!
104 Ndimapeza nzeru zodziwira zinthu kuchokera mʼmalangizo anu;
    kotero ndimadana ndi njira iliyonse yoyipa.

Yeremiya 26:16-24

16 Pamenepo ndunazo pamodzi ndi anthu onse anawuza ansembe ndi aneneri kuti, “Munthu uyu sayenera kuphedwa! Pakuti wayankhula kwa ife mʼdzina la Yehova Mulungu wathu.”

17 Akuluakulu ena a mʼdzikomo anayimirira ndi kuwuza gulu lonse la anthu kuti, 18 “Mʼmasiku a Hezekiya mfumu ya ku Yuda, Mika wa ku Moreseti ankalosera. Iye ankawuza anthu kuti Yehova Wamphamvuzonse akuti,

“ ‘Ziyoni adzatipulidwa ngati munda,
    Yerusalemu adzasanduka bwinja,
    ndipo phiri la Nyumba ya Mulungu lidzasanduka nkhalango yowirira.’

19 Kodi Hezekiya mfumu ya ku Yuda ndi anthu onse anamupha amene uja? Kodi suja mfumu inaopa Yehova ndi kupempha kuti ayikomere mtima? Ndipo suja Yehova anasintha maganizo ake nʼkuleka kuwalanga monga mʼmene anakonzera? Ifetu tikudziyitanira tsoka lalikulu!”

20 (Panalinso munthu wina, Uriya mwana wa Semaya wa ku Kiriati-Yeyarimu, amene ankalosera mʼdzina la Yehova. Iyeyu analosera za mzinda uno ndi dziko lino monga mmene wachitira Yeremiya. 21 Mfumu Yehoyakimu, ankhondo ake onse ndi nduna zake anamva mawu akewo, ndipo anafuna kumupha. Koma Uriya atamva zimenezi, anachita mantha nathawira ku Igupto. 22 Komabe Mfumu Yehoyakimu anatuma Elinatani mwana wa Akibori pamodzi ndi anthu ena, ku Igupto. 23 Iwo anakamutenga Uriya ku Igupto kuja nabwera naye kwa Mfumu Yehoyakimu. Iye anamupha ndi lupanga ndipo mtembo wake anakawutaya ku manda a anthu wamba).

24 Koma Ahikamu mwana wa Safani ndiye anateteza Yeremiya, motero sanamupereke kwa anthu kuti amuphe.

2 Timoteyo 2:14-26

Kuthana ndi Aphunzitsi Onyenga

14 Uziwakumbutsa anthu a Mulungu zinthu izi. Uwachenjeze pamaso pa Mulungu kuti asamakangane pa za mawu. Zimenezi nʼzopanda phindu ndipo zimangowononga amene akumvawo. 15 Uyesetse kukhala wovomerezeka pamaso pa Mulungu monga wantchito wopanda chifukwa chochitira manyazi amene amalalikira mawu achoonadi molondola. 16 Upewe nkhani zopanda pake, zosalemekeza Mulungu, chifukwa anthu oyankhula zotere amanka napotokerapotokera. 17 Chiphunzitso chawo chidzafalikira ngati chilonda. Mwa anthuwa muli Humenayo ndi Fileto. 18 Iwowa apatuka pa choonadi. Iwo amaphunzitsa kuti kuuka kwa akufa kunachitika kale, motero amawononga chikhulupiriro cha anthu ena. 19 Komabe maziko olimba, amene Mulungu anawayika ngokhazikika, ndipo mawu olembedwapo ndi awa: “Yehova amadziwa amene ndi ake,” ndiponso, “Aliyense amene amavomereza dzina la Ambuye ayenera kusiya zoyipa.”

20 Mʼnyumba yayikulu simukhala ziwiya zagolide ndi zasiliva zokha, koma mumakhalanso zamtengo ndi zadothi. Zina zimakhala za ntchito yapamwamba, zina za ntchito wamba. 21 Munthu akadziyeretsa nʼkusiya ntchito za wambazi, adzakhala chiwiya cha ntchito yapamwamba, woyeretsedwa, ndi waphindu kwa Ambuye wake, wokonzeka kugwira ntchito iliyonse yabwino.

22 Thawa zilakolako zoyipa zachinyamata. Funafuna chilungamo, chikhulupiriro, chikondi ndi mtendere pamodzi ndi amene akuyitanira pa dzina la Ambuye ndi mtima osadetsedwa. 23 Ukane matsutsano oyipa ndi opusa, chifukwa amayambitsa mikangano. 24 Ndiponso mtumiki wa Ambuye asamakangane ndi anthu, koma azikhala wachifundo kwa aliyense, wodziwa kuphunzitsa, osati wokalipakalipa. 25 Otsutsana naye awalangize mofatsa, mwina Mulungu adzawapatsa mwayi woti asinthike ndi kuzindikira choonadi. 26 Motero nzeru zawo zidzabweramo, ndipo adzathawa msampha wa mdierekezi, amene anawagwira ukapolo kuti azichita zofuna zake.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.