Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 102:1-17

Pemphero la munthu wosautsidwa, pamene walefuka, nakhuthulira pamaso pa Yehova kulira kwakeko.

102 Yehova imvani pemphero langa;
    kulira kwanga kopempha thandizo kufike kwa Inu.
Musandibisire nkhope yanu
    pamene ndili pa msautso.
Munditcherere khutu;
    pamene ndiyitana ndiyankheni msanga.

Pakuti masiku anga akupita ngati utsi;
    mafupa anga akunyeka ngati nkhuni zoyaka.
Mtima wanga wakanthidwa ndipo ukufota ngati udzu;
    ndipo ndimayiwala kudya chakudya changa.
Chifukwa cha kubuwula kwanga kofuwula
    ndatsala chikopa ndi mafupa okhaokha.
Ndili ngati kadzidzi wa ku chipululu,
    monga kadzidzi pakati pa mabwinja.
Ndimagona osapeza tulo; ndakhala
    ngati mbalame yokhala yokha pa denga.
Tsiku lonse adani anga amandichita chipongwe;
    iwo amene amandinyoza, amagwiritsa ntchito dzina langa ngati temberero.
Pakuti ndimadya phulusa ngati chakudya changa
    ndi kusakaniza chakumwa changa ndi misozi
10 chifukwa cha ukali wanu waukulu,
    popeza Inu mwandinyamula ndi kunditayira kumbali.
11 Masiku anga ali ngati mthunzi wa kumadzulo;
    Ine ndikufota ngati udzu.

12 Koma Inu Yehova, muli pa mpando wanu waufumu kwamuyaya;
    kudziwika kwanu ndi kokhazikika ku mibado yonse.
13 Inu mudzadzuka ndi kuchitira chifundo Ziyoni
    pakuti ndi nthawi yoti muonetse kukoma mtima kwanu pa iyeyo;
    nthawi yoyikika yafika.
14 Pakuti miyala yake ndi yokondedwa kwa atumiki anu;
    fumbi lake lokha limawachititsa kuti amve chisoni.
15 Mitundu ya anthu idzaopa dzina la Yehova,
    mafumu onse a dziko lapansi adzalemekeza ulemerero wanu.
16 Pakuti Yehova adzamanganso Ziyoni
    ndi kuonekera mu ulemerero wake.
17 Iye adzayankha pemphero la anthu otayika;
    sadzanyoza kupempha kwawo.

Yeremiya 29:24-32

Kalata ya Semaya

24 Ukamuwuze Semaya wa ku Nehelamu kuti, 25 “Yehova Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli akuti: Iwe unatumiza kalata mʼdzina lako kwa anthu onse a mu Yerusalemu, kwa Zefaniya mwana wa wansembe Maseya, ndi kwa ansembe onse. Unalemba mu kalatayo kuti, 26 ‘Yehova wakusankha kukhala wansembe mʼmalo mwa Yehoyada kuti ukhale wamkulu woyangʼanira Nyumba ya Yehova. Munthu aliyense wamisala amene akudziyesa kuti ndi mneneri uzimuponya mʼndende ndi kumuveka goli lachitsulo. 27 Nanga tsono chifukwa chiyani simunamuchitire zimenezi Yeremiya wa ku Anatoti, amene amakhala ngati mneneri pakati panu? 28 Yeremiyayo watitumizira uthenga uwu kuno ku Babuloni: Ukapolo wanu ukhala wa nthawi yayitali. Choncho mangani nyumba ndipo muzikhalamo; limani minda ndipo mudye zipatso zake.’ ”

29 Koma wansembe Zefaniya anayiwerenga kalatayo pamaso pa mneneri Yeremiya. 30 Ndipo Yehova anawuza Yeremiya kuti, 31 “Tumiza uthenga uwu kwa akapolo onse: ‘Yehova akuti zokhudza Semaya wa ku Nehelamu: Semaya wakuloserani, ngakhale kuti Ine sindinamutume, ndipo wakunyengani kuti muzikhulupirira bodza. 32 Nʼchifukwa chake Ine Yehova ndikuti: Mʼbanja lakelo sipadzakhala munthu pakati pa mtundu uno wa anthu amene adzaone zinthu zabwino zimene ndidzachitira anthu anga chifukwa analalika zondiwukira,’ ” akutero Yehova.

Aefeso 6:10-20

Zida Zankhondo za Mulungu

10 Potsiriza ndikuti, dzilimbitseni mwa Ambuye ndi mwa mphamvu zake zazikulu. 11 Valani zida zonse za Mulungu kuti muthe kuyima ndi kukana machenjerero a Satana. 12 Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga. 13 Choncho valani zida zonse za Mulungu, kuti pamene tsiku loyipa kwambiri lifika, mudzathe kuyima chilili, ndipo mutatha kuchita zonse, mudzayimabe mwamphamvu. 14 Tsono imani mwamphamvu, mutamangira choonadi ngati lamba mʼchiwuno mwanu, mutavala chilungamo ngati chitsulo chotchinjiriza pa chifuwa. 15 Valani Uthenga Wabwino wamtendere ku mapazi anu ngati nsapato. 16 Kuwonjezera pa zonsezi, nyamulani chishango cha chikhulupiriro, ndipo ndi chimenechi mudzatha kuzimitsa mivi yonse yoyaka moto ya oyipayo. 17 Valani chipewa cha chipulumutso ndi kutenga lupanga la mzimu, limene ndi Mawu a Mulungu. 18 Ndipo mupemphere mwa Mzimu nthawi zonse, mʼmitundu yonse ya mapemphero ndi zopempha. Ndipo pozindikira izi, khalani achangu kupempherera oyera mtima nthawi zonse.

19 Mundipempherere inenso, kuti nthawi iliyonse pamene nditsekula pakamwa panga, andipatse mawu kuti ndiwulule zinsinsi za Uthenga Wabwino mopanda mantha. 20 Ndine kazembe wa Uthenga Wabwinowu ngakhale ndili womangidwa mʼndende. Pempherani kuti ndilalikire mopanda mantha, monga ndiyenera.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.