Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 137

137 Mʼmbali mwa mitsinje ya ku Babuloni tinakhala pansi ndi kulira
    pamene tinakumbukira Ziyoni.
Kumeneko, pa mitengo ya misondozi
    tinapachika apangwe athu,
pakuti anthu otigwira ukapolo anatipempha kuti tiyimbe nyimbo.
    Otizunza athu anafuna nyimbo zachisangalalo;
    iwo anati, “Tiyimbireni imodzi mwa nyimbo za ku Ziyoni!”

Tingayimbe bwanji nyimbo za Yehova
    mʼdziko lachilendo?
Ndikakuyiwala iwe Yerusalemu,
    dzanja langa lamanja liyiwale luso lake.
Lilime langa limamatire ku nkhama za mʼkamwa mwanga
    ndikapanda kukukumbukira iwe Yerusalemu,
ngati sindiyesa iwe
    chimwemwe changa chachikulu.

Kumbukirani, Inu Yehova, zimene Aedomu anachita
    pa tsiku limene Yerusalemu anagonja.
Iwowo anafuwula kuti, “Mugwetseni pansi, mugwetseni pansi
    mpaka pa maziko ake!”

Iwe mwana wa mkazi wa Babuloni, woyenera kuwonongedwa,
    wodalitsika ndi yemwe adzakubwezera
    pa zimene watichitira.
Amene adzagwira makanda ako
    ndi kuwakankhanthitsa pa miyala.

Maliro 5

Inu Yehova, kumbukirani zimene zinatichitikira;
    yangʼanani ndipo muone kunyozeka kwathu.
Apereka cholowa chathu kwa obwera,
    nyumba zathu kwa alendo.
Takhala amasiye ndi wopanda abambo,
    amayi athu ali ngati akazi amasiye.
Tiyenera kugula madzi amene timamwa,
    nkhuni zathunso nʼzogula.
Otilondola atigwira pakhosi;
    tafowoka ndipo sakutilola kupumula.
Tinadzipereka kwa Aigupto ndi kwa Asiriya
    kuti tipeze chakudya.
Makolo athu anachimwa ndipo anafa kale,
    koma chilango chawo chili pa ife.
Akapolo akutilamulira,
    ndipo palibe ndi mmodzi yemwe angatimasule mʼdzanja lawo.
Timapeza chakudya chathu poyika miyoyo yathu pa chiswe
    chifukwa cha lupanga mʼchipululu.
10 Khungu lathu latentha ngati uvuni mʼngʼanjo,
    chifukwa cha kuwawa kwa njala.
11 Amayi agwiriridwa mu Ziyoni,
    ndi anamwali mʼmizinda ya Yuda.
12 Akalonga athu akuwapachika pomangirira manja awo,
    akuluakulu sakuwalemekeza.
13 Achinyamata akukakamizidwa kupera tirigu;
    anyamata akudzandira ndi mitolo ya nkhuni.
14 Akuluakulu anachokapo pa chipata cha mzinda;
    achinyamata aleka nyimbo zawo.
15 Chimwemwe chachoka mʼmitima yathu;
    kuvina kwathu kwasanduka maliro.
16 Chipewa chathu chaufumu chagwa pamutu pathu.
    Tsoka kwa ife, chifukwa tachimwa!
17 Mitima yathu yakomoka chifukwa cha zimenezi,
    chifukwa cha zinthu zimenezi maso athu sakuona bwino,
18 pakuti phiri la Ziyoni, limene lasanduka bwinja,
    nkhandwe zikungoyendayendapo.

19 Inu Yehova, lamulirani kwamuyaya;
    mpando wanu waufumu udzakhalabe ku mibadomibado.
20 Chifukwa chiyani mumatiyiwala nthawi zonse?
    Chifukwa chiyani mwatitaya nthawi yayitali chotere?
21 Yehova mutitembenuzire kwa Inu, kuti tibwerere;
    mukonzenso masiku athu akhale monga akale,
22 pokhapokha ngati mwatitaya kotheratu,
    ndi kuti mwatikwiyira kobzola muyeso.

Marko 11:12-14

Yesu Atemberera Mkuyu

12 Mmawa mwake pamene amachoka ku Betaniya, Yesu anamva njala. 13 Ataonera patali mtengo wamkuyu uli ndi masamba, anapita kuti akaone ngati unali ndi chipatso chilichonse. Atafika, sanapezemo kanthu koma masamba, chifukwa sinali nthawi ya nkhuyu. 14 Ndipo Iye anati kwa mtengo, “Palibe amene adzadyenso chipatso kuchokera kwa iwe.” Ndipo ophunzira ake anamva Iye akunena izi.

Marko 11:20-24

Mkuyu Wofota

20 Mmamawa, pamene ankayenda, anaona mtengo wamkuyu uja utafota kuyambira ku mizu. 21 Petro anakumbukira nati kwa Yesu, “Aphunzitsi, taonani! Mtengo wamkuyu munawutemberera uja wafota!”

22 Yesu anayankha kuti, “Khalani ndi chikhulupiriro mwa Mulungu. 23 Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati wina aliyense angalamule phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye mʼnyanja,’ ndipo wosakayika mu mtima mwake koma kukhulupirira kuti chimene akunena chidzachitika, chidzachitikadi kwa iyeyo. 24 Nʼchifukwa chake ndikukuwuzani kuti chilichonse chimene mupempha mʼpemphero, khulupirirani kuti mwalandira, ndipo chidzakhala chanu.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.