Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
94 Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango,
Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.
2 Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi;
bwezerani kwa odzikuza zowayenera.
3 Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova,
mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?
4 Amakhuthula mawu onyada;
onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.
5 Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova;
amapondereza cholowa chanu.
6 Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko;
amapha ana amasiye.
7 Iwo amati, “Yehova sakuona;
Mulungu wa Yakobo salabadirako.”
8 Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu;
zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?
9 Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva?
Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?
10 Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga?
Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?
11 Yehova amadziwa maganizo a munthu;
Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.
12 Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza,
munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;
13 mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto,
mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.
14 Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake;
Iye sadzasiya cholowa chake.
15 Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo,
ndipo onse olungama mtima adzachitsata.
16 Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa?
Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?
17 Yehova akanapanda kundithandiza,
bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.
18 Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,”
chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.
19 Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga,
chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.
20 Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu
umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?
21 Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama
ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.
22 Koma Yehova wakhala linga langa,
ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.
23 Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo
ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo;
Yehova Mulungu wathu adzawawononga.
Chilala, Njala, Lupanga
14 Awa ndi mawu amene Yehova anamuwuza Yeremiya onena za chilala:
2 “Yuda akulira,
mizinda yake ikuvutika;
anthu ake adzigwetsa pansi mwachisoni,
kulira kwa Yerusalemu kwakula.
3 Anthu awo wolemekezeka akutuma antchito awo kuti akatunge madzi.
Apita ku zitsime
osapezako madzi.
Choncho amabwerera ndi mitsuko yopanda madzi.
Amanyazi ndi othedwa nzeru
adziphimba kumaso.
4 Popeza pansi pawumiratu
chifukwa kulibe madzi,
alimi ali ndi manyazi
ndipo amphimba nkhope zawo.
5 Ngakhale mbawala yayikazi
ikusiya mwana wake wakhanda ku thengo
chifukwa kulibe msipu.
6 Mbidzi zikuyima pa zitunda zopanda kanthu
nʼkumapuma wefuwefu ngati nkhandwe;
maso awo achita chidima
chifukwa chosowa msipu.”
7 Anthu akuti, “Ngakhale machimo athu akutitsutsa,
koma Inu Yehova chitanipo kanthu chifukwa cha dzina lanu.
Pakuti kusakhulupirika kwathu nʼkwakukulu;
ife takuchimwirani.
8 Inu Yehova amene Aisraeli amakukhulupirirani
ndi amene mumawapulumutsa pa nthawi ya masautso,
chifukwa chiyani mukukhala ngati mlendo mʼdziko muno?
Chifukwa chiyani muli ngati wapaulendo amene akungogona tsiku limodzi?
9 Chifukwa chiyani muli ngati munthu amene wadzidzimutsidwa,
kapena ngati wankhondo amene alibe mphamvu yopulumutsa?
Komabe Inu Yehova, muli pakati pathu,
ndipo tikudziwika ndi dzina lanu;
musatitaye ife!”
10 Zimene Yehova akunena za anthuwa ndi izi:
“Iwo amakonda kuyendayenda kwambiri;
samatha kudziretsa.
Nʼchifukwa chake Ine Yehova sindingawalandire,
ndipo tsopano ndidzakumbukira zoyipa zawo
ndi kuwalanga chifukwa cha machimo awo.”
17 “Awuze mawu awa:
“ ‘Maso anga akugwetsa misozi kosalekeza
usana ndi usiku;
chifukwa anthu anga okondedwa
apwetekeka kwambiri,
akanthidwa kwambiri.
18 Ndikapita kuthengo,
ndikuona amene aphedwa ndi lupanga;
ndikapita mu mzinda,
ndikuona amene asakazidwa ndi njala.
Ngakhale aneneri pamodzi
ndi ansembe onse atengedwa.’ ”
19 Kodi anthu a ku Yuda mwawakana kwathunthu?
Kodi mtima wanu wanyansidwa nawo anthu a ku Ziyoni?
Chifukwa chiyani mwatikantha chotere
kuti sitingathenso kuchira?
Ife tinayembekezera mtendere
koma palibe chabwino chomwe chabwera,
tinayembekezera kuchira
koma panali kuopsezedwa kokhakokha.
20 Inu Yehova, ife tikuvomereza kuyipa kwathu
ndiponso kulakwa kwa makolo athu;
ndithu ife tinakuchimwiranidi.
21 Musatikane kuopa kuti dzina lanu linganyozedwe;
musanyoze mpando wanu waufumu waulemerero.
Kumbukirani pangano lanu ndi ife
ndipo musachiphwanye.
22 Mwa milungu yachabechabe ya anthu a mitundu ina,
kodi pali mulungu amene angagwetse mvula?
Ife chikhulupiriro chathu chili pa Inu,
popeza Inu nokha ndinu Yehova Mulungu wathu
amene mukhoza kuchita zimenezi.
Yesu Aneneratu kuti Petro Adzamukana
31 “Simoni, Simoni, Satana wapempha kuti akupete ngati tirigu. 32 Koma Ine ndakupempherera Simoni, kuti chikhulupiriro chako chisafowoke ndipo pamene udzabwerera kwa Ine, udzalimbikitse abale ako.”
33 Koma iye anayankha kuti, “Ambuye, ndine wokonzeka kupita nanu ku ndende ndi kufa komwe.”
Petro Akana Yesu
54 Pamenepo anamugwira Iye, napita naye ndipo anamutengera ku nyumba ya mkulu wa ansembe. Petro anamutsatira patali. 55 Koma pamene anasonkha moto pakati pa bwalo la milandu, anakhala onse pansi ndipo Petro anakhalanso pansi. 56 Mtsikana wantchito anamuona atakhala nawo pafupi ndi moto. Iye anamuyangʼanitsitsa ndipo anati, “Munthu uyu anali ndi Yesu.”
57 Koma Petro anakana nati, “Mtsikana, ine sindimudziwa ameneyu.”
58 Patatha kanthawi pangʼono, wina wake anamuona ndipo anati, “Iwenso ndiwe mmodzi mwa iwo.”
Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, ayi sindine.”
59 Patatha pafupifupi ora limodzi, munthu winanso anati, “Zoonadi, munthu uyu anali ndi Iye, pakuti ndi mu Galileya.”
60 Petro anayankha kuti, “Munthu iwe, sindikudziwa zimene ukunena apa.” Pamene iye ankayankhula, tambala analira. 61 Ambuye anachewuka namuyangʼanitsitsa Petro. Pamenepo Petro anakumbukira mawu amene Ambuye anayankhula kwa iye kuti, “Asanalire tambala lero lino, udzandikana Ine katatu.” 62 Ndipo iye anapita panja nakalira kwambiri.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.