Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
2 Nʼchifukwa chiyani anthu a mitundu ina akufuna kuchita chiwembu?
Akonzekeranji zopanda pake anthu?
2 Mafumu a dziko lapansi akugwirizana nazo;
ndipo olamulira asonkhana pamodzi
kulimbana ndi Ambuye
ndi wodzozedwa wakeyo.
3 Iwo akunena kuti, “Tiyeni timasule magoli awo
ndipo titaye zingwe zawo.”
4 Wokhala mmwamba akuseka;
Ambuye akuwanyoza iwowo.
5 Ndipo iye awadzudzula mu mkwiyo wake
ndi kuwaopseza mu ukali wake, kunena kuti,
6 “Ine ndakhazikitsa mfumu yanga
pa Ziyoni, phiri langa loyera.”
7 Ine ndidzalengeza zimene Yehova walamula:
Iye anati kwa Ine, “Iwe ndiwe mwana wanga;
lero Ine ndakhala Atate ako.
8 Tandipempha,
ndipo ndidzachititsa kuti mitundu ya anthu ikhale cholowa chako;
malekezero a dziko lapansi kuti akhale chuma chako.
9 Iweyo udzawalamulira ndi ndodo yaufumu yachitsulo;
udzawaphwanya zidutswazidutswa ngati zowumba zadothi.”
10 Kotero, inu mafumu, chenjerani;
chenjezedwani, inu olamulira a dziko lapansi.
11 Tumikirani Yehova mwa mantha
ndi kukondwerera ulamuliro wake monjenjemera.
12 Mpsopsoneni mwanayo kuti angakwiye;
kuti mungawonongedwe mʼnjira zanu,
pakuti ukali wake utha kuuka mʼkanthawi kochepa.
Odala ndi onse amene amathawira kwa Iye.
Yeremiya ndi Pasuri
20 Wansembe Pasuri mwana wa Imeri, woyangʼanira wamkulu wa Nyumba ya Yehova, anamva Yeremiya akulosera zinthu zimenezi. 2 Tsono iye analamula kuti mneneri Yeremiyayo amenyedwe ndi kuyikidwa mʼndende pa Chipata chakumtunda kwa Benjamini ku Nyumba ya Yehova. 3 Mmawa mwake, Pasuri anatulutsa Yeremiya mʼndende, ndipo Yeremiyayo anamuwuza kuti, “Pasuri, Yehova sadzakutchulanso dzina lako kuti Pasuri koma Zoopsa pa Mbali Zonse. 4 Pakuti Yehova akuti, ‘Ndidzakusandutsa choopsa kwa mwiniwakewe ndi kwa abwenzi ako onse; iweyo ukuona. Anthu a ku Yuda ndidzawapereka onse mʼmanja mwa mfumu ya ku Babuloni. Ena adzatengedwa ukapolo ku Babuloni ndipo ena adzaphedwa pa nkhondo. 5 Ndidzapereka kwa adani awo chuma chonse cha mu mzinda uno, phindu lonse la ntchito yake, zinthu zake zonse za mtengowapatali ndiponso katundu yense wa mafumu a ku Yuda. Iwo adzazitenga monga zinthu zolanda ku nkhondo ndi kupita nazo ku Babuloni. 6 Ndipo iwe, Pasuri, pamodzi ndi onse a pa banja pako mudzapita ku ukapolo ku Babuloni. Mudzafera kumeneko ndi kuyikidwa mʼmanda, iweyo pamodzi ndi abwenzi ako amene unawalosera zabodza.’ ”
Madandawulo a Yeremiya
7 Inu Yehova, mwandinamiza, ndipo ndinapusadi;
Inu ndi wamphamvu kuposa ine ndipo munandipambana.
Anthu akundinyoza tsiku lonse.
Aliyense akundiseka kosalekeza.
8 Nthawi iliyonse ndikamayankhula,
ndimafuwula kunena kuti, ziwawa kuno! Tikuwonongeka!
Mawu anu Yehova andisandutsa chinthu chonyozeka
ndipo ndimachitidwa chipongwe tsiku lonse.
9 Koma ndikanena kuti, “Sindidzalalikiranso za Iye
kapena kuyankhulanso mʼdzina lake,”
mawu anu amayaka ngati moto mu mtima mwanga,
amakhaladi ngati moto wotsekeredwa mʼmafupa anga.
Ndapirira kusunga mawu anu mu mtima mwanga osawatulutsa,
koma sindingathe kupirirabe.
10 Ndimamva anthu ambiri akunongʼona kuti,
“Zoopsa ku mbali zonse!
Kamunenezeni! Tiyeni tikamuneneze!”
Onse amene anali abwenzi anga
akuyembekezera kuti ndigwa pansi, akumanena kuti,
“Mwina mwake adzanyengedwa;
tidzamugwira
ndi kulipsira pa iye.”
11 Koma Yehova ali nane, ndiye wankhondo wamphamvu.
Nʼchifukwa chake ondizunza adzalephera ndipo sadzandipambana.
Adzachita manyazi kwambiri chifukwa sadzapambana.
Manyazi awo sadzayiwalika konse.
12 Inu Yehova Wamphamvuzonse, Inu amene mumayesa anthu molungama
ndipo mupenya za mu mtima mwa munthu.
Ndiloleni kuti ndione kuti mwalipsira adani anga
popeza ndapereka mlandu wanga kwa Inu.
13 Imbirani Yehova!
Mutamandeni Yehova!
Iye amapulumutsa wosauka
mʼmanja mwa anthu oyipa.
14 Litembereredwe tsiku limene ndinabadwa!
Tsiku limene amayi anga anandibereka lisatamandidwe!
15 Wotembereredwa munthu amene anapita kukasangalatsa abambo anga
ndi uthenga woti:
“Kwabadwa mwana wamwamuna!”
16 Munthu ameneyo akhale ngati mizinda imene
Yehova anayiwononga mopanda chisoni.
Amve mfuwu mmawa,
phokoso la nkhondo masana.
17 Chifukwa sanandiphere mʼmimba,
kuti amayi anga asanduke manda anga,
mimba yawo ikhale yayikulu mpaka kalekale.
18 Kodi ndinabadwira mavuto ndi chisoni
kuti moyo wanga
ukhale wamanyazi wokhawokha?
Munthu Wachuma ndi Ufumu wa Mulungu
18 Oweruza wina wake anamufunsa Iye kuti, “Aphunzitsi abwino, ndichite chiyani kuti ndilandire moyo wosatha?”
19 Yesu anamuyankha kuti, “Chifukwa chiyani ukunditcha wabwino, palibe wabwino kupatula Mulungu yekha. 20 Iwe umadziwa malamulo: ‘Usachite chigololo, usaphe, usabe, usapereke umboni wonama, lemekeza abambo ndi amayi ako.’ ”
21 Iye anati, “Zonsezi ndinasunga kuyambira ndili mnyamata.”
22 Yesu atamva izi, anati kwa iye, “Ukusowabe chinthu chimodzi: Gulitsa zonse zimene uli nazo ndipo uzipereke kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Kenaka ubwere, nunditsate ine.”
23 Atamva zimenezi, anakhumudwa kwambiri chifukwa anali munthu wachuma chambiri. 24 Yesu anamuyangʼana nati, “Nʼkwapatali kwambiri kuti anthu achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu! 25 Ndithudi, nʼkwapafupi kuti ngamira idutse pa kabowo ka zingano kusiyana ndi munthu wachuma kulowa mu ufumu wa Mulungu.”
26 Amene anamva izi anafunsa kuti, “Nanga ndani amene angapulumuke?”
27 Yesu anayankha kuti, “Zinthu zosatheka ndi anthu zimatheka ndi Mulungu.”
28 Petro anati kwa Iye, “Ife tinasiya zonse tinali nazo kutsatira Inu!”
29 Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, Ine ndikukuwuzani kuti palibe amene anasiya nyumba kapena mkazi kapena abale kapena makolo kapena ana chifukwa cha ufumu wa Mulungu 30 adzalephera kulandira mowirikiza mʼmoyo uno, ndi mʼmoyo ukubwerawo, moyo wosatha.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.