Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 81:1

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a gititi. Salimo la Asafu.

81 Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu;
    Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!

Masalimo 81:10-16

10 Ine ndine Yehova Mulungu wanu,
    amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.
    Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.

11 “Koma anthu anga sanandimvere;
    Israeli sanandigonjere.
12 Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo
    kuti atsate zimene ankafuna.

13 “Anthu anga akanangondimvera,
    Israeli akanatsatira njira zanga,
14 nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo
    ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!
15 Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake,
    ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.
16 Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri;
    ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.”

Yeremiya 11:1-17

Pangano Liphwanyidwa

11 Yehova anayankhula ndi Yeremiya kuti, “Imvani mawu a pangano ili, ndipo uwawuze anthu a ku Yuda ndi a ku Yerusalemu. Awuze kuti Yehova, Mulungu wa Israeli akuti ‘adzakhala wotembereredwa munthu amene samvera mawu a pangano ili. Awa anali mawu amene ndinalamulira makolo anu nditawatulutsa mu Igupto, kuchoka mʼngʼanjo yamoto.’ Ine ndinati, ‘Mverani Ine ndi kuchita chilichonse chimene ndakulamulirani. Mukatero mudzakhala anthu anga ndi Ine ndidzakhala Mulungu wanu. Tsono Ine ndidzakwaniritsa lumbiro lomwe ndinalumbira kwa makolo anu kuti ndidzawapatsa dziko loyenda mkaka ndi uchi,’ dziko lomwe inu lero mukukhalamo.”

Tsono Ine ndinayankha kuti, “Ameni, Yehova.”

Yehova anandiwuza kuti, “Lengeza mawu onsewa mʼmizinda yonse ya ku Yuda ndi mʼmisewu ya mu Yerusalemu: ‘Mverani mawu a pangano ili ndi kuzitsatira. Kuyambira nthawi imene ndinatulutsa makolo anu ku Igupto mpaka lero, ndakhala ndi kuwachenjeza kawirikawiri kuti, ‘Mverani Ine.’ Koma sanamvere kapena kulabadirako. Aliyense anawumirira kuchita zoyipa za mʼmitima yawo. Ngakhale ndinawalamulira kuti asunge pangano langa koma iwo sanasunge. Choncho ndinawalanga monga ndinaneneramo.’ ”

Kenaka Yehova anandiwuza kuti, “Anthu a ku Yuda ndi ku Yerusalemu andiwukira. 10 Abwereranso ku machimo a makolo awo, amene anakana kumvera mawu anga. Akutsata milungu ina ndi kumayitumikira. Aisraeli ndi Ayuda aphwanya pangano limene ndinachita ndi makolo awo. 11 Choncho Yehova akuti, ‘Ndidzawagwetsera mavuto amene sadzatha kuwalewa. Ngakhale adzandilirire, sindidzawamvera. 12 Anthu a mʼmizinda ya Yuda ndi anthu a ku Yerusalemu adzapita ndi kukalirira milungu imene ankayifukizira lubani, koma milunguyo sidzawathandiza ndi pangʼono pomwe mavuto akadzafika. 13 Iwe Yuda, uli ndi milungu yochuluka ngati chiwerengero cha mizinda yako; chiwerengero cha maguwa ansembe amene umafukizirapo lubani kwa Baala chili ngati misewu ya mu Yerusalemu.’

14 “Tsono iwe Yeremiya usawapempherere anthu amenewa ngakhale kuwadandaulira kapena kuwapepesera, chifukwa sindidzawamvera akadzandiyitana pa nthawi ya mavuto awo.

15 “Kodi anthu anga okondedwa akudzachita chiyani mʼNyumba yanga?
    Kodi suja iwowa amachita zoyipa zambiri?
    Kodi mungathe kupulumuka,
tsoka osakugwerani
    chifukwa cha nsembe zanuzo?”

16 Kale Yehova ankakutchani mtengo wa olivi wa masamba obiriwira,
    wokhala ndi zipatso zokongola.
Koma tsopano adzawutentha
    ndi mkuntho wamkokomo
    ndipo nthambi zake zidzapserera.

17 Yehova Wamphamvuzonse, amene anakudzalani, walamula kuti mavuto akugwereni. Inu a banja la Yuda ndi a banja la Israeli munachitira Yehova zoyipa ndi kumukwiyitsa pamene munkapereka nsembe zanu kwa Baala.

1 Petro 3:8-12

Kumva Zowawa Chifukwa cha Chilungamo

Potsiriza, nonse khalani a mtima umodzi, omverana chisoni. Kondanani monga abale, muchitirane chifundo ndi kudzichepetsa. Wina akakuchitirani choyipa musabwezere pochitanso choyipa, kapena kubwezera chipongwe akakuchitirani chipongwe, koma muwadalitse. Munayitanidwa kuti mulandire mdalitso. 10 Pakuti,

“Iye amene angakonde moyo
    ndi kuona masiku abwino,
aletse lilime lake kuyankhula zoyipa,
    ndiponso milomo yake kunena mabodza.
11 Apewe zoyipa, ndipo azichita zabwino.
    Afunefune mtendere ndi kuyesetsa kuwupeza.
12 Pakuti Ambuye amayangʼanira bwino anthu olungama
    ndipo amatchera khutu ku mapemphero awo.
Koma Ambuye sawayangʼana bwino amene amachita zoyipa.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.