Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 5:1-7

Nyimbo ya Munda Wamphesa

Ndidzamuyimbira bwenzi langa
    nyimbo yokamba za munda wake wa mpesa:
Wokondedwa wanga anali ndi munda wamphesa
    pa phiri la nthaka yachonde.
Anatipula nachotsa miyala yonse
    ndipo anawokamo mipesa yabwino kwambiri.
Anamanga nsanja yolondera pakati pa mundawo
    ndipo anasemanso mopsinyira mphesa mʼmundamo.
Ndipo iye anayembekezera kuti mundawo udzabala mphesa zabwino,
    koma ayi, unabala mphesa zosadya.

“Tsopano, inu amene mumakhala mu Yerusalemu ndi inu anthu a ku Yuda,
    weruzani pakati pa ine ndi munda wanga wa mpesawu.
Kodi nʼchiyaninso china chimene ndikanachitira munda wanga wa mpesa
    kupambana chomwe ndawuchitira kale?
Pamene ndinkayembekezera kuti udzabala mphesa zabwino,
    bwanji unabala mphesa zosadya?
Tsopano ndikuwuzani
    chimene ndidzawuchitire munda wanga wa mpesa:
ndidzachotsa mpanda wake,
    ndipo mundawo udzawonongeka;
ndidzagwetsa khoma lake,
    ndipo nyama zidzapondapondamo.
Ndidzawusandutsa tsala,
    udzakhala wosatengulira ndi wosalimira
    ndipo mudzamera mkandankhuku ndi minga ina.
Ndidzalamula mitambo
    kuti isagwetse mvula pa mundapo.”

Munda wamphesa wa Yehova Wamphamvuzonse
    ndi Aisraeli,
ndipo anthu a ku Yuda ndiwo
    minda yake yomukondweretsa.
Ndipo Iye ankayembekezera chiweruzo cholungama, mʼmalo mwake anaona kuphana;
    mʼmalo mwa chilungamo Iye anamva kulira kwa anthu ozunzika.

Masalimo 80:1-2

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.

80 Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,
    Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;
Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani
    kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.
Utsani mphamvu yanu;
    bwerani ndi kutipulumutsa.

Masalimo 80:8-19

Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto;
    munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.
Munawulimira munda wamphesawo,
    ndipo unamera ndi kudzaza dziko.
10 Mapiri anaphimbidwa ndi mthunzi wake,
    mikungudza yamphamvu ndi nthambi zake.
11 Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja,
    mphukira zake mpaka ku mtsinje.

12 Chifukwa chiyani mwagwetsa makoma ake
    kuti onse amene akudutsa athyole mphesa zake?
13 Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga
    ndipo zirombo za mthengo zimawudya.
14 Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse!
    Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone!
Uyangʼanireni mpesa umenewu,
15     muzu umene dzanja lanu lamanja ladzala,
    mwana amene inu munamukuza nokha.

16 Mpesa wanu wadulidwa ndi kutenthedwa ndi moto;
    pakudzudzula kwanu anthu anu awonongeka.
17 Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,
    mwana wa munthu amene mwalera nokha.
18 Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;
    titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.

19 Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse
    nkhope yanu itiwalire
    kuti tipulumutsidwe.

Ahebri 11:29-12:2

29 Ndi chikhulupiriro Aisraeli anawoloka Nyanja Yofiira ngati pa mtunda powuma, koma Aigupto atayesa kutero anamizidwa.

30 Ndi chikhulupiriro mpanda wa Yeriko unagwa, Aisraeli atawuzungulira kasanu ndi kawiri.

31 Ndi chikhulupiriro Rahabe, mkazi wadama sanaphedwe pamodzi ndi osamvera aja chifukwa analandira bwino ozonda aja ku nyumba kwake.

32 Kodi ndinenenso chiyani? Nthawi yandichepera yoti ndinene za Gideoni, Baraki, Samsoni, Yefita, Davide, Samueli ndi aneneri, 33 amene ndi chikhulupiriro anagonjetsa mafumu, anakhazikitsa chilungamo ndi kulandira zimene zinalonjezedwa. Anatseka pakamwa pa mikango, 34 anazimitsa moto waukali, ndipo anapulumuka osaphedwa ndi lupanga. Anali ofowoka koma analandira mphamvu; anasanduka amphamvu pa nkhondo, nathamangitsa magulu a ankhondo a adani awo. 35 Amayi ena analandira anthu awo amene anafa, ataukitsidwanso. Enanso anazunzidwa ndipo anakana kumasulidwa, kuti adzaukenso ndi moyo wabwino. 36 Ena anawaseka ndi kuwakwapula, pamenenso ena anamangidwa ndi kupita ku ndende. 37 Anagendedwa miyala; anachekedwa pakati; ena anaphedwa ndi lupanga. Iwo anayendayenda atavala zikopa zankhosa ndi zikopa zambuzi, umphawi okhaokha, ozunzidwa ndi kuvutitsidwa. 38 Dziko lapansi silinawayenere. Anayendayenda mʼzipululu ndi mapiri, ndiponso mʼmapanga ndi mʼmaenje.

39 Onsewa anayamikidwa chifukwa cha chikhulupiriro chawo, komabe palibe wa iwo amene analandira zimene analonjezedwa. 40 Mulungu anatikonzera ife kanthu koposa, kuti iwo asayesedwe angwiro popanda ife.

Yesu Chitsanzo Chathu

12 Tsono popeza ifenso tazunguliridwa ndi gulu lalikulu la mboni, tiyeni titaye chilichonse chimene chimatitchinga, makamaka tchimo limene limatikola mosavuta, ndipo tithamange ndi khama mpikisano umene tayambawu. Tiyeni tiyangʼanitsitse Yesu, amene ndi woyamba ndi wotsiriza wa chikhulupiriro chathu. Chifukwa cha chimwemwe chimene chimamudikira anapirira zowawa zapamtanda. Iye ananyoza manyazi a imfa yotere ndipo tsopano akukhala ku dzanja lamanja la mpando waufumu wa Mulungu.

Luka 12:49-56

Za Kugawikana

49 “Ine ndabwera kudzayatsa moto pa dziko lapansi, ndipo ndikanakonda ukanayaka kale. 50 Koma Ine ndiyenera kubatizidwa, ndipo ndikusautsika mu mtima mpaka utachitika! 51 Kodi mukuganiza kuti Ine ndinabwera kudzabweretsa mtendere pa dziko lapansi? Ayi, Ine ndikukuwuzani kuti, ndinabweretsa kugawikana. 52 Kuyambira tsopano mpaka mʼtsogolo mʼbanja limodzi mudzakhala anthu asanu ndipo adzawukirana wina ndi mnzake, atatu kuwukira awiri, ndipo awiri kuwukira atatu. 53 Anthu adzawukirana. Abambo kudzawukira mwana wawo wamwamuna, mwana wawoyo adzawukira abambo ake. Amayi adzawukira mwana wawo wamkazi, mwana wawoyo adzawukira amayi ake. Amayi adzawukira mpongozi wawo wamkazi, mpongoziyo adzawukira amayiwo.”

Kumasulira Nthawi

54 Iye anati kwa gulu la anthu, “Pamene mukuona mtambo ukukwera kummawa, nthawi yomweyo inu mumati, ‘kugwa mvula,’ ndipo imagwadi. 55 Ndipo pamene mphepo yakummwera ikuwomba, inu mumati ‘kutentha’ ndipo kumaterodi. 56 Achiphamaso inu! Inu mumadziwa kutanthauzira maonekedwe a dziko lapansi ndi thambo. Zikutheka bwanji kuti simukudziwa kumasulira kwa nthawi ino?

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.