Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Yesaya 1:1

Masomphenya wonena za Yuda ndi Yerusalemu, amene Yesaya mwana wa Amozi, anaona pa nthawi ya ulamuliro wa Uziya, Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a Yuda.

Yesaya 1:10-20

10 Imvani mawu a Yehova,
    inu olamulira Sodomu;
mverani lamulo la Mulungu wathu,
    inu anthu a ku Gomora!
11 Yehova akuti, “Kodi ndili nazo chiyani
    nsembe zanu zochuluka?”
“Zandikola nsembe zanu zopsereza
    za nkhosa zazimuna ndiponso mafuta a nyama zonenepa;
sindikusangalatsidwanso
    ndi magazi angʼombe zamphongo ndi a ana ankhosa ndi ambuzi zazimuna.
12 Ndani anakulamulirani kuti
    mubwere nazo pamaso panga?
    Ndani anakuwuzani kuti muzipondaponda mʼmabwalo a nyumba yanga?
13 Siyani kubweretsa nsembe zachabechabezo!
    Nsembe zanu zofukiza zimandinyansa Ine.
Sindingapirire misonkhano yanu yoyipa,
    kapenanso zikondwerero za Mwezi Watsopano ndi Masabata.
14 Zikondwerero zanu za Mwezi Watsopano ndi masiku anu opatulika
    ndimadana nazo.
Zasanduka katundu wondilemera;
    ndatopa kuzinyamula.
15 Mukamatambasula manja anu popemphera,
    Ine sindidzakuyangʼanani;
ngakhale muchulukitse mapemphero anu,
    sindidzakumverani.
Manja anu ndi odzaza ndi magazi;
16     sambani, dziyeretseni.
Chotsani pamaso panu
    ntchito zanu zoyipa!
Lekani kuchita zoyipa,
17     phunzirani kuchita zabwino!
Funafunani chilungamo,
    thandizani oponderezedwa.
Tetezani ana amasiye,
    muwayimirire akazi amasiye pa milandu yawo.”

18 Yehova akuti,
    “Tiyeni tsono tikambe mlandu wanu.
Ngakhale machimo anu ali ofiira,
    adzayera ngati thonje.
Ngakhale ali ofiira ngati kapezi,
    adzayera ngati ubweya wankhosa.
19 Ngati muli okonzeka kundimvera
    mudzadya zinthu zabwino za mʼdziko;
20 koma mukakana ndi kuwukira
    mudzaphedwa ndi lupanga.”
            Pakuti Yehova wayankhula.

Masalimo 50:1-8

Salimo la Asafu.

50 Wamphamvuyo, Yehova Mulungu,
    akuyankhula ndi kuyitanitsa dziko lapansi
    kuyambira kotulukira dzuwa mpaka kumene limalowera.
Kuchokera ku Ziyoni, mokongola kwambiri
    Mulungu akuwala.
Mulungu wathu akubwera ndipo sadzakhala chete;
    moto ukunyeketsa patsogolo pake,
    ndipo pomuzungulira pali mphepo yamkuntho
Iye akuyitanitsa zamumlengalenga
    ndi za pa dziko lapansi kuti aweruze anthu ake.
Mundisonkhanitsire okhulupirika anga,
    amene anachita pangano ndi ine pochita nsembe.
Ndipo mayiko akumwamba akulengeza chilungamo chake,
    pakuti Mulungu mwini ndi woweruza.

Imvani inu anthu anga, ndipo Ine ndidzayankhula,
    iwe Israeli, ndipo Ine ndidzayankhula mokutsutsa;
    ndine Mulungu, Mulungu wako.
Sindikudzudzula chifukwa cha nsembe zako,
    kapena nsembe zako zopsereza zimene zili pamaso panga nthawi zonse.

Masalimo 50:22-23

22 “Ganizira izi, iwe amene umayiwala Mulungu
    kuti ndingakukadzule popanda wokupulumutsa:
23 Iye amene amapereka nsembe yamayamiko amandilemekeza,
    ndipo amakonza njira zake kuti ndimuonetse
    chipulumutso cha Mulungu.”

Ahebri 11:1-3

Za Chikhulupiriro cha anthu Akale

11 Tsopano chikhulupiriro ndi kusakayika konse pa zinthu zimene tikuziyembekeza, ndi kutsimikiza kuti zinthu zimene sitiziona zilipo ndithu. Ndi chikhulupiriro chimenechi makolo athu akale anayamikidwa.

Ndi chikhulupiriro timazindikira kuti dziko lapansi ndi la mmwamba zinapangidwa ndi Mawu a Mulungu, ndikuti zinthu zoonekazi zinachokera ku zinthu zosaoneka.

Ahebri 11:8-16

Ndi chikhulupiriro Abrahamu atayitanidwa kuti apite ku dziko limene anamulonjeza kuti lidzakhala lake, anamvera ndi kupita, ngakhale sanadziwe kumene ankapita. Ndi chikhulupiriro chomwecho anakhala ngati mlendo mʼdziko lija limene Mulungu anamulonjeza. Anakhala mʼmatenti monganso anachitira Isake ndi Yakobo, amene nawonso analonjezedwanso. 10 Pakuti amadikira mudzi wokhala ndi maziko, umene mmisiri ndi womanga wake ndi Mulungu.

11 Ndi chikhulupiriro Sara analandira mphamvu zokhala ndi pakati ngakhale kuti zaka zake zobala mwana zinali zitapita kale, popeza anamutenga amene analonjeza kukhala wokhulupirika. 12 Nʼchifukwa chake mwa munthu mmodzi, amene anali ngati wakufa, munatuluka mibado yochuluka ngati nyenyezi ndi yosawerengeka ngati mchenga wa mʼmbali mwa nyanja.

13 Onsewa anakhalabe mwachikhulupiriro mpaka anafa. Iwo sanalandire zimene Mulungu anawalonjeza; iwo anangozionera chapatali ndi kuzilandira. Ndipo iwo anavomereza kuti analidi alendo ndi osakhazikika pa dziko lapansi. 14 Anthu amene amanena zinthu zotere amaonekeratu kuti akufuna dziko lawo lenileni. 15 Akanakhala kuti akuganizira za dziko limene analisiya akanapeza mpata obwerera kwawo. 16 Mʼmalo mwake, iwo amafunitsitsa dziko labwino, ndilo lakumwamba. Nʼchifukwa chake Mulungu sachita manyazi kutchedwa Mulungu wawo, pakuti Iye anawalonjeza mudzi.

Luka 12:32-40

Chuma cha Kumwamba

32 “Musachite mantha, inu kagulu kankhosa, pakuti zinakondweretsa Atate anu kuti akupatseni ufumu. 33 Gulitsani zonse zimene muli nazo, ndipo ndalama zake mupereke kwa osauka. Dzipezereni zikwama zandalama zimene sizidzatha, ndi kudzikundikira chuma chomwe sichidzatha kumwamba, kumene mbala sizingafikeko, ndipo dzimbiri silingawononge. 34 Popeza kumene kuli chuma chanu, mtima wanunso udzakhala komweko.”

Kukhala a Atcheru

35 “Khalani okonzekeratu ndipo nyale zanu ziziyaka, 36 ngati anthu oyembekezera kubwera kwa mbuye wawo kuchokera kuphwando la ukwati, kuti pamene afika ndi kugogoda akhoza nthawi yomweyo kumutsekulira chitseko. 37 Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo pobwera adzawapeze akudikira. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti adzakonzekera kuwatumikira, adzakhala nawo pa tebulo ndipo adzabwera ndi kuwatumikira. 38 Zidzakhala bwino kwa antchitowo amene mbuye wawo adzawapeze ali okonzeka, ngakhale iye atabwera pa ora lachiwiri kapena lachitatu usiku. 39 Koma zindikirani izi: Ngati mwini nyumba akanadziwa ora limene mbala ibwera, sakanalola kuti nyumba yake ithyoledwe. 40 Inunso muyenera kukhala okonzeka, chifukwa Mwana wa Munthu adzabwera pa ora limene simukumuyembekezera Iye.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.