Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 60

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Mikitamu ya Davide yophunzitsira. Pamene anamenyana ndi Mesopotamiya ndi Aramu-Zoba, ndi pamene Yowabu anabwerera ndi kukantha Aedomu 12,000 mʼChigwa cha Mchere.

60 Inu Mulungu mwatikanatu ife, ndipo mwatiwonongera otiteteza.
    Inu mwatikwiyira, tsopano tibwezeretseni mwakale!
Inu mwagwedeza dziko ndipo mwalingʼamba,
    konzani mingʼalu yake pakuti ikugwedezeka kwambiri.
Inu mwaonetsa anthu anu nthawi za mavuto;
    inu mwatipatsa vinyo amene watichititsa kudzandira.

Koma kwa iwo amene amaopa Inu, Inu mwakweza mbendera
    kuti tisonkhanireko pothawa uta.

Tipulumutseni ndi kutithandiza ndi dzanja lanu lamanja,
    kuti iwo amene mumawakonda apulumutsidwe.
Mulungu wayankhula kuchokera ku malo ake opatulika:
    “Mwakupambana ndidzagawa Sekemu
    ndipo ndidzayeza malire a chigwa cha Sukoti.
Giliyadi ndi wanga, Manase ndi wanganso;
    Efereimu ndi chipewa changa chodzitetezera,
    Yuda ndi ndodo yanga yaufumu
Mowabu ndi mbale yanga yosambira,
    pa Edomu ndidzaponyapo nsapato yanga,
    pa Filisitiya ndidzafuwula mwakupambana.”

Adzandifikitse ndani ku mzinda wotetezedwa?
    Ndani adzanditsogolera ku Edomu?
10 Kodi si Inu Mulungu, Inu amene mwatikana ife
    ndipo simutuluka pamodzi ndi magulu athu ankhondo.
11 Tipatseni chithandizo kuti tilimbane ndi mdani wathu,
    pakuti thandizo lochokera kwa munthu ndi lopanda phindu.
12 Chifukwa cha Mulungu, ife tidzapeza chipambano
    ndipo tidzapondaponda adani athu.

Hoseya 14

Kulapa Kubweretsa Madalitso

14 Iwe Israeli bwerera kwa Yehova Mulungu wako.
    Machimo anu ndi amene akugwetsani!
Bweretsani zopempha zanu
    ndipo bwererani kwa Yehova.
Munene kwa Iye kuti,
    “Tikhululukireni machimo athu onse
ndi kutilandira mokoma mtima,
    kuti tithe kukuyamikani ndi mawu a pakamwa pathu.
Asiriya sangatipulumutse;
    ife sitidzakwera pa akavalo ankhondo,
sitidzanenanso kuti, ‘Milungu yathu’
    kwa zimene manja athu omwe anazipanga,
    pakuti ndinu amene mumachitira chifundo ana amasiye.”

Ine ndidzachiza kusakhulupirika kwawo
    ndipo ndidzawakonda mwaufulu
    pakuti ndaleka kuwakwiyira.
Ndidzakhala ngati mame kwa Israeli
    Ndipo iye adzachita maluwa ngati kakombo.
Adzazika mizu yake pansi
    ngati mkungudza wa ku Lebanoni;
    mphukira zake zidzakula.
Kukongola kwake kudzakhala ngati mtengo wa olivi,
    kununkhira kwake ngati mkungudza wa ku Lebanoni.
Anthu adzakhalanso mu mthunzi wake.
    Iye adzakula bwino ngati tirigu.
Adzachita maluwa ngati mphesa
    ndipo kutchuka kwake kudzakhala ngati vinyo wochokera ku Lebanoni.
Efereimu adzati, “Ndidzachita nawonso chiyani mafano?
    Ine ndidzamuyankha ndi kumusamalira.
Ine ndili ngati mtengo wa payini wobiriwira;
    zipatso zako zimachokera kwa Ine.”

Ndani ali ndi nzeru? Adzazindikire zinthu izi.
    Ndani amene amamvetsa zinthu? Adzamvetse izi.
Njira za Yehova ndi zolungama;
    anthu olungama amayenda mʼmenemo,
    koma anthu owukira amapunthwamo.

Luka 12:22-31

Musadere Nkhawa

22 Kenaka Yesu anati kwa ophunzira ake, “Choncho Ine ndikuwuzani kuti musadere nkhawa za moyo wanu, zimene mudzadya; kapena za thupi lanu, zimene mudzavala. 23 Moyo uposa chakudya, ndi thupi liposa chovala. 24 Taonani makwangwala: iwo safesa kapena kukolola, alibe nyumba zosungamo zinthu kapena nkhokwe; komabe, Mulungu amawadyetsa. Koposa kotani inu amene ndi ofunikira kuposa mbalame. 25 Ndi ndani wa inu akhoza kuwonjeza ora pa moyo wake chifukwa cha kudandaula? 26 Popeza simungathe kuchita kanthu kakangʼono aka, nʼchifukwa chiyani mumadandaula ndi zinazi?

27 “Taonani mmene maluwa amakulira. Iwo sagwira ntchito kapena kusoka zovala. Koma Ine ndikuwuzani kuti, ngakhale Solomoni muulemelero wake wonse sanavalepo ngati limodzi la awa. 28 Ngati umu ndi mmene Mulungu amavekera udzu wakuthengo, umene lero ulipo ndipo mawa uponyedwa pa moto, nanga Iye adzakuvekani inu motani. Haa! Inu achikhulupiriro chochepa! 29 Ndipo musayike mtima wanu pa zimene mudzadye kapena kumwa; musade nazo nkhawa. 30 Pakuti anthu akunja amathamanga kufunafuna zinthu zotere, ndipo Atate amadziwa kuti mumazifuna zimenezi. 31 Koma funafunani ufumu wake, ndipo mudzapatsidwa zonsezi.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.