Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Asafu.
82 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;
Iye akuweruza pakati pa “milungu.”
2 “Mudzateteza osalungama mpaka liti,
ndi kukondera anthu oyipa?
3 Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;
mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.
4 Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;
apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.
5 “Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.
Amayendayenda mu mdima;
maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.
6 “Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu,
nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’
7 Koma mudzafa ngati anthu wamba;
mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”
8 Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,
pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.
12 “Koma inu munawamwetsa vinyo anaziri aja,
ndipo munalamula aneneri kuti asanenere.
13 “Tsono Ine ndidzakupsinjani
monga imapsinjikira ngolo imene yadzaza ndi tirigu.
14 Munthu waliwiro sadzatha kuthawa,
munthu wamphamvu sadzakhalanso ndi nyonga,
wankhondo sadzapulumutsa moyo wake.
15 Munthu wa uta sadzalimbika,
msilikali wothamanga kwambiri sadzapulumuka,
ndipo wokwera pa akavalo sadzapulumutsa moyo wake.
16 Ngakhale asilikali olimba mtima kwambiri
adzathawa ali maliseche pa tsikulo,”
akutero Yehova.
Mboni Zotsutsa Israeli
3 Inu Aisraeli, imvani mawu awa amene Yehova wayankhula kutsutsana nanu, kutsutsana ndi banja lonse limene analitulutsa mu Igupto:
2 “Inu nokha ndi amene ndinakusankhani
pakati pa mabanja onse a dziko lapansi;
nʼchifukwa chake ndidzakulangani
chifukwa cha machimo anu onse.”
3 Kodi anthu awiri nʼkuyendera limodzi
asanapangane?
4 Kodi mkango umabangula mʼnkhalango
usanagwire nyama?
Kodi msona wamkango umalira mʼphanga mwake
pamene sunagwire kanthu?
5 Kodi mbalame nʼkutera pa msampha
pamene palibe nyambo yake?
Kodi msampha umafwamphuka
usanakole kanthu?
6 Kodi pamene lipenga la nkhondo lalira mu mzinda,
anthu sanjenjemera?
Pamene tsoka lafika mu mzinda,
kodi si Yehova amene wachititsa zimenezo?
7 Zoonadi Ambuye Yehova sachita kanthu
asanawulule zimene akufuna kuchita
kwa atumiki ake, aneneri.
8 Mkango wabangula,
ndani amene sachita mantha?
Ambuye Yehova wayankhula,
ndani amene sanganenere?
16 “Pakuti Mulungu anakonda dziko lapansi, kotero anapereka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense wokhulupirira Iye asatayike koma akhale ndi moyo wosatha. 17 Pakuti Mulungu sanatume Mwana wake ku dziko lapansi, kuti akaweruze, koma kuti akapulumutse dziko lapansi. 18 Aliyense wokhulupirira Iye saweruzidwa, koma aliyense wosakhulupirira waweruzidwa kale chifukwa sanakhulupirire dzina la Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. 19 Ndipo chiweruzo ndi ichi: kuwunika kunabwera mʼdziko lapansi, koma anthu anakonda mdima mʼmalo mwa kuwunikako, chifukwa ntchito zawo zinali zoyipa. 20 Aliyense wochita zoyipa amadana ndi kuwunika, ndipo sabwera poyera chifukwa cha mantha kuti ntchito zake zingaonekere. 21 Koma aliyense wokhala mu choonadi amabwera ku kuwunika, kuti zionekere poyera zimene iye wachita zachitika kudzera mwa Mulungu.”
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.