Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 82

Salimo la Asafu.

82 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu;
    Iye akuweruza pakati pa “milungu.”

“Mudzateteza osalungama mpaka liti,
    ndi kukondera anthu oyipa?
Tetezani anthu ofowoka ndi amasiye;
    mukhazikitse ufulu wa anthu osauka ndi ozunzika.
Landitsani anthu ofowoka ndi osowa;
    apulumutseni mʼdzanja la anthu oyipa.

“Iwo sadziwa kanthu, sazindikira kalikonse.
    Amayendayenda mu mdima;
    maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.

“Ndinati, ‘Inu ndinu Mulungu,
    nonsenu ndinu ana a Wammwambamwamba.’
Koma mudzafa ngati anthu wamba;
    mudzagwa ngati wolamula wina aliyense.”

Dzukani Inu Mulungu, weruzani dziko lapansi,
    pakuti mayiko onse ndi cholowa chanu.

Amosi 2:4-11

Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Yuda akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Popeza iwo akana lamulo la Yehova
    ndipo sanasunge malangizo ake,
popeza asocheretsedwa ndi milungu yabodza,
    milungu imene makolo awo ankayitsatira,
Ine ndidzatumiza moto pa Yuda,
    umene udzanyeketsa nyumba zaufumu za ku Yerusalemu.”

Chilango cha Anthu a ku Israeli

Yehova akuti,

“Chifukwa anthu a ku Israeli akunka nachimwirachimwira,
    Ine sindileka kuwalanga.
Iwo amagulitsa anthu olungama ndi siliva,
    ndi osauka ndi nsapato.
Amapondereza anthu osauka
    ngati akuponda fumbi,
    ndipo sawaweruza mwachilungamo anthu oponderezedwa.
Abambo ndi mwana wawo amagonana ndi mtsikana mmodzi yemweyo,
    ndipo potero amanyozetsa dzina langa loyera.
Anthuwo amakagonana mʼmbali mwa guwa lililonse la nsembe
    pa zovala zimene anatenga ngati chikole.
Mʼnyumba ya mulungu wawo
    amamweramo vinyo amene analipiritsa anthu pa milandu.

“Ine ndinawononga Aamori pamaso pawo,
    ngakhale iwo anali anthu ataliatali ngati mikungudza
    ndiponso amphamvu ngati mitengo ya thundu.
Ndinawononga zipatso zawo
    ndiponso mizu yawo.

10 “Ine ndinakutulutsani ku Igupto,
    ndipo ndinakutsogolerani mʼchipululu kwa zaka makumi anayi,
    kudzakupatsani dziko la Aamori.
11 Ine ndinawutsanso ena mwa ana ako kuti akhale aneneri,
    ndi ena mwa anyamata ako kuti akhale anaziri.
Kodi si choncho, inu Aisraeli?”
            akutero Yehova.

Machitidwe a Atumwi 7:9-16

“Makolo athu anachita nsanje ndi Yosefe ndipo anamugulitsa kuti akakhale kapolo ku Igupto. Koma Mulungu anali naye 10 ndipo anamupulumutsa iye kumasautso ake onse. Mulungu anamupatsa Yosefe nzeru ndi chisomo pamaso pa Farao mfumu ya ku Igupto, kotero mfumuyo inamuyika iye kukhala nduna yayikulu ya dziko la Igupto ndiponso nyumba yake yonse yaufumu.

11 “Kenaka munalowa njala mʼdziko la Kanaani, kotero kuti anthu anavutika kwambiri, ndipo makolo athu sanathe kupeza chakudya. 12 Pamene Yakobo anamva kuti ku Igupto kunali tirigu, iye anatuma makolo athu ulendo woyamba. 13 Pa ulendo wawo wachiwiri, Yosefe anadziwulula kwa abale akewo ndipo Farao anadziwa za banja la Yosefe. 14 Izi zinachitika, Yosefe anayitanitsa abambo ake Yakobo ndi banja lonse, onse pamodzi analipo 75. 15 Motero Yakobo anapita ku Igupto, kumene iye ndiponso makolo athu anamwalira. 16 Mitembo yawo anayinyamula ndi kupita nayo ku Sekemu kumene inayikidwa mʼmanda amene Abrahamu anagula kochokera kwa ana a Hamori ku Sekemuko.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.