Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 30

Salimo la Davide. Nyimbo yoyimba popereka Nyumba ya Mulungu.

30 Ndidzakukwezani Yehova,
    chifukwa mwanditulutsa kwakuya,
    ndipo simunalole kuti adani anga akondwere pa ine.
Inu Yehova Mulungu wanga ndinapempha kwa Inu thandizo
    ndipo Inu munandichiritsa.
Inu Yehova, munanditulutsa ku manda,
    munandisunga kuti ndisatsalire mʼdzenje.

Imbirani Yehova inu anthu ake okhulupirika;
    tamandani dzina lake loyera.
Pakuti mkwiyo wake umakhala kwa kanthawi
    koma kukoma mtima kwake ndi kwa moyo wonse;
utha kuchezera kulira usiku wonse,
    koma chimwemwe chimabwera mmawa.

Pamene ndinaona kuti ndili otetezedwa ndinati,
    “Sindidzagwedezekanso.”
Inu Yehova, pamene munandikomera mtima,
    munachititsa phiri langa kuyima chilili;
koma pamene munabisa nkhope yanu,
    ndinataya mtima.

Kwa Inu Yehova ndinayitana;
    kwa Ambuye ndinapempha chifundo;
“Kodi pali phindu lanji powonongeka kwanga
    ngati nditsikira ku dzenje?
Kodi fumbi lidzakutamandani Inu?
    Kodi lidzalengeza za kukhulupirika kwanu?
10 Imvani Yehova ndipo mundichitire chifundo;
    Yehova mukhale thandizo langa.”

11 Inu munasandutsa kulira kwanga kukhala kuvina;
    munachotsa chiguduli changa ndi kundiveka ndi chimwemwe,
12 kuti mtima wanga uthe kuyimbira Inu usakhale chete.
    Yehova Mulungu wanga, ndidzapereka kwa Inu mayamiko kwamuyaya.

2 Mafumu 4:18-31

18 Mwana uja anakula, ndipo tsiku lina anapita kwa abambo ake amene anali ndi anthu odula tirigu. 19 Mwanayo anafuwula kwa abambo ake kuti, “Mayo! Mutu wanga ine! Mayo! Mutu wanga ine!”

Abambo akewo anawuza wantchito wake kuti, “Munyamule ndi kukamupereka kwa amayi ake.” 20 Wantchito uja atamunyamula ndi kumupereka kwa amayi ake. Mwanayo anakhala pa miyendo ya amayi akeyo mpaka masana, ndipo pambuyo pake anamwalira. 21 Mayiyo ananyamula mwanayo nakamugoneka pa bedi la munthu wa Mulungu uja. Kenaka anatseka chitseko iye nʼkuchokapo.

22 Iye anayitanitsa mwamuna wake namuwuza kuti, “Tumizireni wantchito mmodzi ndi bulu mmodzi kuti ndipite mofulumira kwa munthu wa Mulungu nʼkubwererako.”

23 Mwamuna wakeyo anafunsa kuti, “Chifukwa chiyani ukupita kwa iyeyo lero? Lero si tsiku la Chikondwerero cha Mwezi Watsopano kapena tsiku la Sabata.”

Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”

24 Mayiyo anamangirira chishalo pa bulu ndipo anawuza wantchito wake kuti, “Yendetsa bulu mofulumira. Usachepetse liwiro pokhapokha nditakuwuza.” 25 Choncho ananyamuka nakafika kwa munthu wa Mulungu uja ku Phiri la Karimeli.

Munthu wa Mulungu ataona mayiyo patali, anawuza mtumiki wake Gehazi kuti, “Taona! Msunemu uyo! 26 Thamanga msanga ukakumane naye ndipo ukamufunse kuti, ‘Kodi muli bwino? Kodi mwamuna wanu ali bwino? Kodi mwana wanu ali bwino?’ ”

Mayiyo anayankha kuti, “Zonse zili bwino.”

27 Atafika kwa munthu wa Mulunguyo pa phiripo, mayiyo anagwira mapazi a Elisa. Gehazi anabwera kuti amukankhe, koma munthu wa Mulungu anati, “Musiye! Iyeyu ali pa mavuto aakulu, koma Yehova wandibisira zimenezi ndipo sanandiwuze chifukwa chake.”

28 Tsono mayiyo anati, “Mbuye wanga, kodi ine ndinakupemphani mwana? Kodi sindinakuwuzeni kuti musandinamize?”

29 Elisa anawuza Gehazi kuti, “Manga lamba mʼchiwuno mwako, tenga ndodo yanga mʼdzanja lako ndipo thamanga. Ngati ukumana ndi munthu wina aliyense, usamupatse moni, ndipo ngati wina akupatsa moni, usayankhe. Ukagoneke ndodo yanga pa nkhope ya mwanayo.”

30 Koma mayi wake wa mwana uja anati, “Pali Yehova wamoyo ndiponso pali inu nomwe, ineyo sindidzakusiyani.” Choncho Elisa ananyamuka natsatira mayiyo.

31 Gehazi anatsogola nakagoneka ndodoyo pa nkhope ya mwanayo, koma sipanamveke mawu kapena kugwedezeka kuonetsa kuti ali moyo. Choncho Gehazi anabwerera kukakumana ndi Elisa ndipo anamuwuza kuti, “Mwanayo sanatsitsimuke.”

2 Akorinto 8:1-7

Kulimbikitsa Zopereka

Ndipo tsopano, abale, tikufuna kuti mudziwe za chisomo chimene Mulungu wapereka ku mipingo ya ku Makedoniya. Pakati pa mayesero owawitsa, chimwemwe chawo chosefukira ndi umphawi wawo otheratu, anapereka mowolowamanja kwambiri. Motero ndikuchitira umboni kuti anapereka mmene akanathera, ndipo mwinanso kuposera mmene akathera kupereka. Anapereka mosakakamizidwa, ndipo anatipempha motiwumiriza kuti tiwapatse mwayi woti nawonso athandize anthu oyera mtima a ku Yudeya. Iwo anachita moposera mmene ife timayembekezera. Choyamba anadzipereka kwa Ambuye ndipo kenaka kwa ife monga mwa chifuniro cha Mulungu. Choncho tinamupempha Tito kuti atsirize poti nʼkuti atayamba kale ntchito yachisomoyi pakati panu. Popeza pa zinthu zonse munachita bwino, monga pachikhulupiriro, poyankhula, pachidziwitso, pakhama lambiri ndi pachikondi chanu pa ife, onetsetsani kuti muchitenso bwino pachisomo ichi chopereka.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.