Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe, potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Salimo la Asafu. Nyimbo.
75 Tikuthokoza Inu Mulungu,
tikuthokoza, pakuti dzina lanu lili pafupi nafe,
anthutu amafotokoza za ntchito zanu zodabwitsa.
2 Mumati, “Ine ndimayika nthawi yoyenera,
ndine amene ndimaweruza mwachilungamo.
3 Pamene dziko lapansi ndi anthu ake onse anjenjemera,
ndine amene ndimagwiriziza mizati yake molimba.
Sela
4 Kwa odzitama ndikuti, ‘Musadzitamenso,’
ndipo kwa oyipa, ‘Musatukulenso nyanga zanu.
5 Musatukule nyanga zanu motsutsana ndi kumwamba;
musayankhule ndi khosi losololoka.’ ”
6 Kugamula milandu sikuchokera kummawa kapena kumadzulo
kapena ku chipululu.
7 Koma ndi Mulungu amene amaweruza:
Iyeyo amatsitsa wina, nakwezanso wina.
8 Mʼdzanja la Yehova muli chikho
chodzaza ndi vinyo wochita thovu, wosakanizidwa ndi zokometsera;
Iye amamutsanulira pansi ndipo onse oyipa a dziko lapansi
amamwa ndi senga zake zonse.
9 Kunena za ine, ndidzalengeza izi kwamuyaya;
ndidzayimba matamando kwa Mulungu wa Yakobo.
10 Ndidzadula nyanga za onse oyipa
koma nyanga za olungama zidzakwezedwa.
4 Tsono Mesa, mfumu ya ku Mowabu ankaweta nkhosa, ndipo iye ankayenera kumapereka kwa mfumu ya ku Israeli chaka ndi chaka ana ankhosa onenepa okwanira 100,000 pamodzi ndi ubweya wankhosa 100,000 zazimuna. 5 Koma atamwalira Ahabu, mfumu ya ku Mowabu inawukira mfumu ya ku Israeli. 6 Choncho nthawi imeneyi mfumu Yoramu inatuluka mu Samariya ndi kukasonkhanitsa Aisraeli onse. 7 Yoramu anatumizanso uthenga uwu kwa Yehosafati mfumu ya ku Yuda: “Mfumu ya ku Mowabu yandiwukira. Kodi ungapite nane kukamenyana ndi Mowabu?”
Iye anayankha kuti, “Ine ndidzapita nawe. Iwe ndi ine ndife anthu amodzi, anthu anga ali ngati anthu ako, akavalo anga ali ngati akavalo ako.”
8 Yehosafati anafunsa kuti, “Kodi tidzera njira iti popita ku nkhondoko?”
Yoramu anayankha kuti, “Tidzera ku Chipululu cha Edomu.”
9 Choncho mfumu ya ku Israeli inanyamuka pamodzi ndi mfumu ya ku Yuda ndi ya ku Edomu. Ndipo atayenda mozungulira mʼchipululu kwa masiku asanu ndi awiri, asilikali analibe madzi woti amwe kapena kumwetsa nyama zawo zosenza katundu.
10 Mfumu inafuwula kuti, “Nʼchiyani chomwe chikutichitikira! Kodi Yehova wasonkhanitsa mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu?”
11 Koma mfumu Yehosafati inafunsa kuti, “Kodi kuno kulibe mneneri wa Yehova woti tingakafunse kwa Yehova kudzera mwa iyeyo?”
Mtsogoleri wa ankhondo wa mfumu ya ku Israeli anayankha kuti, “Alipo, Elisa mwana wa Safati. Iye anali mtumiki wa Eliya.”
12 Yehosafati anati, “Yehova amayankhula kudzera mwa iye.” Choncho mfumu ya ku Israeli pamodzi ndi Yehosafati ndiponso mfumu ya ku Edomu anapita kwa Elisa.
13 Elisa ananena kwa mfumu ya ku Israeli kuti, “Pali ubale wanji pakati pa inu ndi ine? Pitani kwa aneneri a abambo ndi amayi anu.”
Mfumu ya ku Israeli inayankha kuti, “Ayi, pakuti ndi Yehova amene anatisonkhanitsa ife mafumu atatu pamodzi kuti atipereke mʼmanja mwa Amowabu.”
14 Elisa anati, “Pali Yehova Wamphamvuzonse amene ndimamutumikira, pakanapanda kuti ndimamuchitira ulemu Yehosafati mfumu ya ku Yuda, sindikanakulabadirani kapena kukuyangʼanani nʼkomwe. 15 Koma tsopano ndiyitanireni munthu wodziwa kuyimba bwino zeze.”
Munthuyo akuyimba zeze, mphamvu ya Yehova inafika pa Elisa, 16 ndipo anati, “Yehova akuti, ‘Kumbani ngalande mʼchigwa chonse.’ 17 Pakuti Yehova akunena kuti, ‘Simudzaona mphepo kapena mvula, komabe chigwa ichi chopanda madzi chidzadzaza ndi madzi, ndipo inu mudzamwa pamodzi ndi ngʼombe zanu ndiponso nyama zanu zonse.’ 18 Izi ndi zosavuta pamaso pa Yehova. Ndipo adzaperekanso Amowabu mʼmanja mwanu. 19 Mudzagonjetsa mizinda yawo yonse yotetezedwa ndiponso mizinda yawo ikuluikulu. Mudzagwetsa mtengo wabwino uliwonse, mudzatseka akasupe onse amadzi, ndiponso mudzawononga minda yawo yonse yachonde poponyamo miyala.”
20 Mmawa mwake, nthawi yopereka nsembe ili pafupi, anangoona madzi akutuluka kuchokera ku Edomu, ndipo malo onse anadzaza ndi madzi.
6 Musalole wina akunamizeni ndi mawu opanda pake, pakuti chifukwa cha zinthu ngati izi mkwiyo wa Mulungu ukubwera pa amene samvera. 7 Nʼchifukwa chake musamayanjane nawo anthu otere.
8 Pajatu inu nthawi ina munali mdima, koma tsopano ndinu kuwunika mwa Ambuye. Mukhale ngati ana akuwunika 9 (pakuti pamene pali kuwunika pamapezekaponso zabwino zonse, chilungamo ndi choonadi). 10 Inu mufufuze chimene chimakondweretsa Ambuye. 11 Musayanjane nazo ntchito zosapindulitsa za mdima, koma mʼmalo mwake muzitsutse. 12 Pakuti ndi zochititsa manyazi ngakhale kutchula zomwe zimachitika mseri. 13 Koma kuwala kumawunikira zinthu, ndipo chilichonse chimaonekera poyera. Choncho chilichonse choonekera poyera chimasandukanso kuwala. 14 Nʼchifukwa chake Malemba akuti,
“Dzuka, wamtulo iwe,
uka kwa akufa,
ndipo Khristu adzakuwalira.”
15 Samalani makhalidwe anu, musakhale ngati opanda nzeru koma ngati anzeru. 16 Gwiritsani ntchito mpata uliwonse, chifukwa masiku ano ndi oyipa. 17 Choncho musakhale opusa, koma mudziwe zimene Ambuye akufuna kuti muchite. 18 Musaledzere ndi vinyo, chifukwa adzawononga moyo wanu. Mʼmalo mwake, mudzazidwe ndi Mzimu Woyera. 19 Muziyankhulana wina ndi mnzake mawu a Masalimo, nyimbo za Mulungu ndi nyimbo za uzimu. Muziyimbira Ambuye movomerezana ndi mitima yanu. 20 Muziyamika Mulungu Atate nthawi zonse chifukwa cha zonse, mʼdzina la Ambuye athu Yesu Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.