Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 42

BUKU LACHIWIRI

Masalimo 42–72

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya ana a Kora.

42 Monga mbawala ipuma wefuwefu kufunafuna mitsinje yamadzi,
    kotero moyo wanga upuma wefuwefu kufunafuna Inu Mulungu.
Moyo wanga uli ndi ludzu lofuna Mulungu, lofuna Mulungu wamoyo.
    Kodi ndipite liti kukakumana ndi Mulungu?
Misozi yanga yakhala chakudya changa
    usana ndi usiku,
pamene anthu akunena kwa ine tsiku lonse kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”
Zinthu izi ndimazikumbukira
    pamene ndikukhuthula moyo wanga:
momwe ndinkapitira ndi gulu lalikulu,
    kutsogolera mayendedwe a ku Nyumba ya Mulungu
ndi mfuwu yachimwemwe ndi mayamiko
    pakati pa anthu a pa chikondwerero.

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni, iwe moyo wanga?
    Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Yembekezera Mulungu,
    pakuti ndidzamulambirabe,
Mpulumutsi wanga ndi     Mulungu wanga.

Moyo wanga uli ndi chisoni mʼkati mwanga
    kotero ndidzakumbukira Inu
kuchokera ku dziko la Yorodani,
    ku mitunda ya Herimoni kuchokera ku phiri la Mizara.
Madzi akuya akuyitana madzi akuya
    mu mkokomo wa mathithi anu;
mafunde anu onse obwera mwamphamvu
    andimiza.

Koma usana Yehova amalamulira chikondi chake,
    nthawi ya usiku nyimbo yake ili nane;
    pemphero kwa Mulungu wa moyo wanga.

Ine ndikuti kwa Mulungu Thanthwe langa,
    “Nʼchifukwa chiyani mwandiyiwala?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
    woponderezedwa ndi mdani?”
10 Mafupa anga ali ndi ululu wakufa nawo
    pamene adani anga akundinyoza,
tsiku lonse akunena kuti,
    “Mulungu wako ali kuti?”

11 Bwanji ukumva chisoni,
    iwe mtima wanga?
Chifukwa chiyani ukuvutika chonchi mʼkati mwanga?
    Khulupirira Mulungu, pakuti ndidzamutamandanso,
    Iye amene ali thandizo langa ndi Mulungu wanga.

Masalimo 43

43 Onetsani kusalakwa kwanga Inu Mulungu;
    ndipo mundinenere mlandu wanga kutsutsana ndi mtundu wosapembedza;
    mundilanditse mʼmanja mwa achinyengo ndi anthu oyipa.
Pajatu Inu Mulungu ndinu mphamvu zanga.
    Nʼchifukwa chiyani mwandikana ine?
Nʼchifukwa chiyani ndiyenera kuyenda ndikulira,
    woponderezedwa ndi mdani?
Tumizani kuwunika kwanu ndi choonadi chanu
    kuti zinditsogolere;
mulole kuti zindifikitse ku phiri lanu loyera,
    kumalo kumene inu mumakhala.
Ndipo ndidzapita ku guwa lansembe la Mulungu,
    kwa Mulungu, chimwemwe changa ndi chikondwerero changa.
Ndidzakutamandani ndi zeze,
    Inu Mulungu wanga.

Nʼchifukwa chiyani uli ndi chisoni iwe moyo wanga?
    Nʼchifukwa chiyani wakhumudwa iwe mʼkati mwanga?
Khulupirira Mulungu,
    pakuti ndidzamutamandabe Iye,
    Mpulumutsi wanga ndi Mulungu wanga.

Miyambo 11:3-13

Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera,
    koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.

Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu,
    koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo,
    koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo.

Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa,
    koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.

Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso.
    Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka.

Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto,
    koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa.

Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake,
    koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu.

10 Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera,
    ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.

11 Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima,
    koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa.

12 Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru,
    koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete.

13 Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi;
    koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.

Mateyu 9:27-34

Yesu Achiritsa Osaona ndi Osayankhula

27 Yesu atapitirira ulendo wake, amuna awiri osaona anamutsatira Iye, akufuwula kuti, “Tichitireni chifundo, Mwana wa Davide!”

28 Atalowa mʼnyumba, amuna awiri osaonawo anabwera kwa Iye ndipo anawafunsa kuti, “Kodi mukhulupirira kuti ndikhoza kukuchiritsani?”

Iwo anayankha kuti, “Inde Ambuye.”

29 Pomwepo anakhudza maso awo nati, “Zichitike kwa inu monga mwachikhulupiriro chanu.” 30 Ndipo anayamba kuona. Yesu anawachenjeza kwambiri nati, “Onani, wina aliyense asadziwe za zimenezi.” 31 Koma iwo anatuluka mʼnyumbamo nafalitsa za Iye mʼchigawo chonse.

32 Pamene iwo ankatuluka kunja, anthu anabwera kwa Iye ndi munthu wogwidwa ndi mzimu wosayankhula. 33 Ndipo atatulutsa mzimuwo, munthuyo anayankhula. Gulu la anthuwo linadabwa ndipo linati, “Zinthu zotere sizinaonekepo mu Israeli.”

34 Koma Afarisi anati, “Akutulutsa mizimu yoyipa ndi mphamvu ya mkulu wa ziwanda.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.