Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Miyambo 8:1-4

Nzeru Ikuyitana

Kodi nzeru sikuyitana?
    Kodi nzeru yomvetsa zinthu sinakweze mawu ake?
Nzeru imayima pa zitunda mʼmbali mwa njira,
    imayima pa mphambano ya misewu.
Imafuwula pafupi ndi zipata zolowera mu mzinda,
    pa makomo olowera imafuwula kuti,
Inu anthu, ndikuyitana inu;
    ndikuyitanatu anthu onse.

Miyambo 8:22-31

22 “Yehova anandilenga ine nzeru monga ntchito yake yoyamba.
    Mwa ntchito zake zakalekale yoyamba ndinali ine.
23 Ndinapangidwa kalekalelo,
    pachiyambi penipeni dziko lapansi lisanalengedwe.
24 Nyanja, akasupe odzaza ndi madzi,
    zonsezi kulibe pamene ine ndinkabadwa.
25 Mapiri asanakhazikitsidwe pa malo awo,
    mapiri angʼonoangʼono asanakhalepo, ine ndinali nditabadwa kale,
26 lisanalengedwe dziko lapansi ndi minda yake;
    lisanalengedwe dothi loyamba la dziko lapansi.
27 Ine ndinalipo pamene Yehova ankakhazikitsa mlengalenga,
    pamene ankalemba malire a nyanja yozama,
28 pamene anakhazikitsa mitambo ya mlengalenga
    ndi kukhazikitsa akasupe a madzi ozama,
29 pamene anayikira nyanja malire
    kuti madzi asadutse malirewo,
ndiponso pamene ankayika malire a dziko lapansi.
30     Tsono ine ndinali pambali pake ngati mmisiri;
ndikumukondweretsa tsiku ndi tsiku,
    kusangalala nthawi zonse pamaso pake.
31 Ndinkasangalala ndi dziko lake lonse
    ndiponso kumakondwera nawo anthu onse.”

Masalimo 8

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide.

Inu Yehova Ambuye athu,
    dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu
    mʼmayiko onse akumwamba.
Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,
    Inu mwakhazikitsa mphamvu
chifukwa cha adani anu,
    kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.

Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,
    ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi,
    zimene mwaziyika pa malo ake,
munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,
    ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba
    ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.

Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu;
    munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi
    ndi nyama zakuthengo,
mbalame zamlengalenga
    ndi nsomba zamʼnyanja
    zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.

Inu Yehova, Ambuye athu,
    dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!

Aroma 5:1-5

Mtendere ndi Chimwemwe

Tsopano popeza tayesedwa olungama mwa chikhulupiriro, tili ndi mtendere ndi Mulungu kudzera mwa Ambuye athu Yesu Khristu. Iyeyo ndiye amene anatsekulira njira mwachikhulupiriro yolowera mʼchisomo mʼmene takhazikikamo. Ndipo tikukondwerera chiyembekezo cha ulemerero wa Mulungu. Koma si pokhapo ayi, koma ife tikukondweranso mʼmasautso athu chifukwa tikudziwa kuti masautso amatiphunzitsa kupirira. Ndipo kupirira kumabweretsa makhalidwe, makhalidwe amabweretsa chiyembekezo. Ndipo chiyembekezo chimenechi sichitikhumudwitsa chifukwa Mulungu mwa Mzimu Woyera, amene Iye anatipatsa, wadzaza mʼmitima mwathu ndi chikondi chake.

Yohane 16:12-15

12 “Ine ndili ndi zambiri zoti ndiyankhule nanu, koma simungathe kuzilandira tsopano. 13 Koma pamene Iye, Mzimu wachoonadi, abwera, adzakutsogolerani mʼchoonadi chonse. Iye sadzayankhula mwa Iye yekha, adzayankhula zokhazo zimene wamva ndipo Iye adzakuwuzani zimene zikubwera. 14 Iye adzalemekeza Ine chifukwa adzatenga za Ine nadzakudziwitsani. 15 Zonse za Atate ndi zanga. Ichi nʼchifukwa chake Ine ndanena kuti Mzimu Woyera adzatenga kwa Ine zanga kuti muzidziwe.”

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.