Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Nyimbo. Salimo la ana a Kora.
48 Wamkulu ndi Yehova, ndi woyenera kwambiri matamando
mu mzinda wa Mulungu wathu, phiri lake loyera.
2 Lokongola mu utali mwake,
chimwemwe cha dziko lonse lapansi.
Malo aatali kwambiri a Zafoni ndiye Phiri la Ziyoni,
mzinda wa Mfumu yayikulu.
3 Mulungu ali mu malinga ake;
Iye wadzionetsa yekha kuti ndiye malinga akewo.
4 Pamene mafumu anasonkhana pamodzi,
pamene anayendera pamodzi kudzalimbana nafe,
5 iwo anaona mzindawo ndipo anadabwa kwambiri;
anathawa ndi mantha aakulu.
6 Pomwepo anagwidwa nako kunjenjemera,
ululu wonga wa mkazi woyembekezera pa nthawi yochira.
7 Inu munawawononga monga sitima zapamadzi za ku Tarisisi
zitawonongeka ndi mphepo ya kummawa.
8 Monga momwe tinamvera,
kotero ife tinaona
mu mzinda wa Yehova Wamphamvuzonse,
mu mzinda wa Mulungu wathu.
Mulungu adzawuteteza kwamuyaya.
9 Mʼkati mwa Nyumba yanu Mulungu,
ife timalingaliramo zachikondi chanu chosasinthika.
10 Monga dzina lanu, Inu Mulungu,
matamando anu amafika ku malekezero a dziko lapansi
dzanja lanu lamanja ladzaza ndi chilungamo.
11 Phiri la Ziyoni likukondwera,
midzi ya Yuda ndi yosangalala
chifukwa cha maweruzo anu.
12 Yendayendani mu Ziyoni, uzungulireni mzindawo,
werengani nsanja zake.
13 Yangʼanitsitsani bwino mipanda yake,
penyetsetsani malinga ake,
kuti mudzafotokoze za izo ku mʼbado wotsatira.
14 Pakuti Mulungu uyu ndi Mulungu wathu ku nthawi zosatha;
Iye adzakhala mtsogoleri wathu mpaka ku mapeto.
14 Yehova anayankhula nane kuti, 15 “Anthu okhala ku Yerusalemu akuwanena abale ako, anthu a ku ukapolo, onse a banja la Israeli, kuti, ‘Anthu onse amene anatengedwa ukapolo ali kutali ndi Yehova. Dziko lanu Yehova anatipatsa kuti likhale lathulathu.’ ”
Mulungu Alonjeza za Kubwerera kwa Israeli
16 “Nʼchifukwa chake nena kwa anzako a ku ukapolo kuti, ‘Ambuye Yehova akuti: Ine ndinawatumiza kutali pakati pa anthu a mitundu ina. Ndinawabalalitsa ku mayiko ambiri. Komabe ndakhala ndikuwasunga ku mayiko kumene anapitako!’
17 “Nʼchifukwa chake uwawuze zimene Ine Ambuye Yehova ndikunena kuti, Ndidzawasonkhanitsa kuchokera kwa anthu a mitundu inayo ndi kuwasonkhanitsira pamodzi kuchokera ku mayiko kumene ndinawabalalitsirako. Pambuyo pake ndidzawapatsa dziko la Israeli.
18 “Akadzalowa mʼdzikomo adzachotsa mafano awo onse oyipa ndi onyansa. 19 Ndidzawapatsa mtima watsopano ndipo ndidzayika mzimu watsopano mwa iwo. Ndidzachotsa mtima wowuma ngati mwala mwa iwo, ndipo ndidzawapatsa mtima wofewa ngati mnofu. 20 Motero adzatsata malamulo anga ndipo adzasunga mosamala malamulo anga. Adzakhala anthu anga, ndipo Ine ndidzakhala Mulungu wawo. 21 Koma kunena za amene akupembedza mafano oyipa ndi onyansa, ndidzawalanga chifukwa cha zimene achita. Ndikutero Ine Ambuye Yehova.”
22 Tsono akerubi aja anatambasula mapiko awo kuyamba kuwuluka, mikombero ili mʼmbali mwawo. Ulemerero wa Mulungu wa Israeli unali pamwamba pawo. 23 Ulemerero wa Yehova unakwera ndi kusiya mzindawo ndipo unakayima pa phiri cha kummawa kwake kwa mzindawo. 24 Pambuyo pake Mzimu wa Mulungu unandinyamula ndi kukandifikitsa. Zimenezi zinkachitika mʼmasomphenya monga mmene Mzimu wa Mulungu unkandionetsera.
Kenaka masomphenya amene ndinkawaonawo anayamba kuzimirira. 25 Ndipo ndinafotokozera akapolowo zonse zimene Yehova anandionetsa.
12 Mzimu amene tinalandira ife si wa dziko lapansi koma Mzimu wochokera kwa Mulungu wotipatsa ife mwaulere. 13 Izi ndi zimene timayankhula osati mʼmawu wophunzitsidwa ndi nzeru za munthu koma mʼmawu wophunzitsidwa ndi Mzimu, kufotokozera zoonadi zauzimu mʼmawu auzimu. 14 Munthu wopanda Mzimu savomereza zinthu zimene zichokera kwa Mzimu wa Mulungu, popeza ndi zopusa kwa iyeyo, ndipo sangazimvetsetse chifukwa zimazindikirika mwa Mzimu. 15 Munthu wauzimu amaweruza pa zinthu zonse, koma iye mwini saweruzidwa ndi munthu aliyense. 16 Pakuti
“Ndani anadziwa malingaliro a Ambuye,
kuti akhoza kumulangiza Iye.”
Koma tili nawo mtima wa Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.