Print Page Options
Previous Prev Day Next DayNext

Revised Common Lectionary (Semicontinuous)

Daily Bible readings that follow the church liturgical year, with sequential stories told across multiple weeks.
Duration: 1245 days
Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)
Version
Masalimo 29

Salimo la Davide.

29 Perekani kwa Yehova, inu anthu amphamvu,
    perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.
Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake,
    pembedzani Yehova mwa kukongola kwa chiyero chake.

Liwu la Yehova lili pamwamba pa madzi;
    Mulungu waulemerero abangula,
    Yehova abangula pamwamba pa madzi amphamvu.
Liwu la Yehova ndi lamphamvu;
    liwu la Yehova ndi laulemerero.
Liwu la Yehova limathyola mikungudza;
    Yehova amathyolathyola mikungudza ya ku Lebanoni.
Iye amachititsa Lebanoni kulumphalumpha ngati mwana wangʼombe,
    Siriyoni ngati mwana wa njati:
Liwu la Yehova limakantha
    ngati kungʼanima kwa mphenzi.
Liwu la Yehova limagwedeza chipululu;
    Yehova amagwedeza chipululu cha Kadesi.
Liwu la Yehova limapindapinda mibawa
    ndi kuyeretsa nkhalango.
Ndipo mʼNyumba mwake onse amafuwula kuti, “Ulemerero!”

10 Yehova amakhala pamwamba pa madzi osefukira,
    Yehova ndiye mfumu kwamuyaya.
11 Yehova amapereka mphamvu kwa anthu ake;
    Yehova amadalitsa anthu ake ndi mtendere.

Eksodo 40:16-38

16 Mose anachita zonse monga Yehova anamulamulira.

17 Kotero anayimika chihema tsiku loyamba la mwezi woyamba mʼchaka chachiwiri. 18 Nthawi imene Mose anayimika chihema, anayika matsinde mʼmalo ake, kuyimitsa maferemu, kulowetsa mitanda ndi kuyika nsichi. 19 Kenaka anayika tenti pamwamba pa chihema ndipo anayika chophimba pa tenti monga momwe Yehova analamulira Mose.

20 Iye anatenga miyala ya umboni nayika mʼbokosi lija ndi kuyika chivundikiro pamwamba pake. 21 Kenaka analowetsa bokosilo mʼchihema ndipo anapachika katani ndi kubisa bokosi la umboni monga momwe Yehova analamulira iye.

22 Mose anayika tebulo mu tenti ya msonkhano kumpoto kwa chihema, kunja kwa katani, 23 ndipo anayikapo buledi pamaso pa Yehova, monga momwe Yehova analamulira Mose.

24 Iye anayikanso choyikapo nyale mu tenti ya msonkhano moyangʼanana ndi tebulo mbali yakummwera kwa chihema. 25 Ndipo anayikapo nyale zija pamaso pa Yehova, monga Yehova analamulira Mose.

26 Mose anayika guwa la golide mu tenti ya msonkhano patsogolo pa katani 27 ndipo anapserezapo lubani wonunkhira monga Yehova anamulamulira. 28 Kenaka anayika katani ya pa chipata cha chihema.

29 Iye anayika guwa lansembe yopsereza pafupi ndi chipata cha chihema, tenti ya msonkhano, ndipo anapereka nsembe yopsereza ndi nsembe ya ufa monga Yehova anamulamulira.

30 Iye anayika beseni pakati pa tenti ya msonkhano ndi guwa lansembe ndipo anathiramo madzi wosamba, 31 ndipo Mose, Aaroni ndi ana ake amasamba manja ndi mapazi awo. 32 Iwo amasamba nthawi zonse akamalowa mu tenti ya msonkhano kapena kuyandikira guwa lansembe monga Yehova analamulira Mose.

33 Kenaka Mose anamanga bwalo kuzungulira chihema ndi guwa lansembe ndipo anayika katani ya pa chipata cha bwalo. Kotero Mose anamaliza ntchito.

Ulemerero wa Yehova

34 Kenaka mtambo unaphimba tenti ya msonkhano, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho. 35 Mose sanathe kulowa mu tenti ya msonkhano chifukwa mtambo unali utakhazikika pa chihemacho, ndipo ulemerero wa Yehova unadzaza mʼchihemacho.

36 Pa maulendo awo onse, mtambo ukachoka pamwamba pa chihema, Aisraeli ankasamukanso pamene analipo. 37 Koma ngati mtambo sunachoke, iwo sankasamukanso mpaka tsiku limene udzachoke. 38 Kotero mtambo wa Yehova unkakhala pamwamba pa chihema usana, ndi mtambo wamoto umakhala usiku, pamaso pa nyumba yonse ya Israeli pa masiku onse aulendo wawo.

Machitidwe a Atumwi 16:35-40

35 Kutacha, woweruza milandu uja anatuma asilikali kwa woyangʼanira ndendeyo kukanena kuti, “Amasuleni anthu aja.” 36 Woyangʼanira ndendeyo anawuza Paulo kuti, “Woweruza milandu walamula kuti iwe ndi Sila mumasulidwe. Tsopano muzipita. Pitani mumtendere.”

37 Koma Paulo anati kwa asilikaliwo: “Iwo anatikwapula pa gulu la anthu asanatiweruze, ngakhale kuti ndife nzika za Chiroma natiponya mʼndende. Kodi tsopano akufuna kutitulutsa mwamseri? Ayi! Asiyeni abwere okha kuti adzatitulutse.”

38 Asilikali aja anakafotokozera woweruza milandu ndipo pamene anamva kuti Paulo ndi Sila anali nzika za Chiroma, anachita mantha. 39 Iye anabwera kudzawapepesa ndipo anawatulutsa mʼndende, nawapempha kuti achoke mu mzindawo. 40 Paulo ndi Sila atatuluka mʼndende, anapita ku nyumba ya Lidiya, kumene anakumana ndi abale nawalimbikitsa. Kenaka anachoka.

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero (CCL)

The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.