Revised Common Lectionary (Semicontinuous)
Salimo la Davide.
27 Yehova ndiye kuwunika kwanga ndi chipulumutso changa;
ndidzaopa yani?
Yehova ndi linga la moyo wanga;
ndidzachita mantha ndi yani?
2 Pamene anthu oyipa abwera kudzalimbana nane
kudzadya mnofu wanga,
pamene adani anga ndi achiwembu andithira nkhondo,
iwo adzapunthwa ndi kugwa.
3 Ngakhale gulu lankhondo lindizinge,
mtima wanga sudzaopa.
Ngakhale nkhondo itayambika kulimbana nane,
ngakhale nthawi imeneyo, ine ndidzalimbika mtima.
4 Chinthu chimodzi chokha chimene ndipempha kwa Yehova,
ichi ndi chimene ndidzachifunafuna:
kuti ndikhale mʼNyumba ya Yehova
masiku onse a moyo wanga,
ndi kuyangʼana kukongola kwa Yehova,
ndi kumufunafuna Iye mʼNyumba yake.
5 Pakuti pa tsiku la msautso
Iye adzanditeteza mʼmalo ake okhalamo;
adzandibisa mʼkati mwa Nyumba yake
ndi kukhazika ine pamwamba pa thanthwe.
6 Kotero mutu wanga udzakwezedwa
kuposa adani anga amene andizungulira;
pa Nyumba yake ndidzapereka nsembe ndi mfuwu wachimwemwe;
ndidzayimba nyimbo kwa Yehova.
7 Imvani mawu anga pamene ndiyitana Inu Yehova
mundichitire chifundo ndipo mundiyankhe.
8 Mtima wanga ukuti kwa Inu, “Funafuna nkhope yake!”
Nkhope yanu Yehova ndidzayifunafuna.
9 Musandibisire nkhope yanu,
musamubweze mtumiki wanu mwamkwiyo;
mwakhala muli thandizo langa.
Musandikane kapena kunditaya,
Inu Mulungu Mpulumutsi wanga.
10 Ngakhale abambo ndi amayi anga anditaya
Yehova adzandisamala.
11 Phunzitseni njira yanu Inu Yehova,
munditsogolere mʼnjira yowongoka
chifukwa cha ondizunza.
12 Musandipereke ku zokhumba za adani anga,
pakuti mboni zambiri zauka kutsutsana nane
ndipo zikundiopseza.
13 Ine ndikutsimikiza mtima za zimenezi;
ndidzaona ubwino wa Yehova
mʼdziko la anthu amoyo.
14 Dikirani pa Yehova;
khalani anyonga ndipo limbani mtima
nimudikire Yehova.
17 Abramu atabwerera kuchokera kogonjetsa Kedorilaomere ndi mafumu amene anali nawo pa mgwirizano, mfumu ya ku Sodomu inabwera kudzakumana naye ku Chigwa cha Save (chimenechi ndicho Chigwa cha Mfumu).
18 Ndipo Melikizedeki mfumu ya ku Salemu anabweretsa buledi ndi vinyo. Iyeyu anali wansembe wa Mulungu Wammwambamwamba, 19 ndipo anadalitsa Abramu nati,
“Mulungu Wammwambamwamba,
wolenga kumwamba ndi dziko lapansi, akudalitse iwe Abramu.
20 Ndipo adalitsike Mulungu Wammwambamwamba
amene anapereka adani ako mʼdzanja lako.”
Ndipo Abramu anamupatsa iye chakhumi cha zonse anali nazo.
21 Mfumu ya Sodomu inati kwa Abramu, “Ine undipatse anthu okhawo, koma katundu akhale wako.”
22 Koma Abramu anawuza mfumu ya Sodomu kuti, “Ndakweza manja anga kwa Yehova, Mulungu Wammwambamwamba, Mlengi wakumwamba ndi dziko lapansi, kulumbira 23 kuti sindidzalandira kanthu kalikonse kako, ngakhale utakhala ulusi chabe kapena chingwe cha nsapato, kuopa kuti ungamanene kuti, ‘Ndamulemeretsa Abramu.’ 24 Sindidzalandira kanthu kalikonse kupatula zokhazo zimene anthu anga adya ndi gawo la katundu la anthu amene ndinapita nawo monga Aneri, Esikolo ndi Mamre. Iwowa atenge gawo lawo.”
17 Abale, nonsenu pamodzi mudzinditsanzira ine, ndipo monga inu muli ndi chitsanzo, phunzirani kwa amene akukhala moyo motsatira momwe timakhalira. 18 Pakuti monga ndakhala ndikukuwuzani kawirikawiri mʼmbuyomu, ndipo tsopano ndikunenanso ndi misozi kuti, anthu ambiri akukhala monga adani a mtanda wa Khristu. 19 Mapeto awo ndi chiwonongeko, mulungu wawo ndi mimba zawo, ndipo ulemerero wawo ndi manyazi awo. Mtima wawo uli pa zinthu za dziko lapansi. 20 Koma ife ndife nzika za kumwamba ndipo tikudikirira mwachidwi Mpulumutsi wochokera kumeneko, Ambuye Yesu Khristu.
The Word of God in Contemporary Chichewa Copyright © 2002, 2016 by Biblica, Inc.® Used by permission of Biblica, Inc.® All rights reserved worldwide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Mwini © 2002, 2016 ndi Biblica, Inc.® Kugwiritsa ntchito mwachilolezo. Umwini ndi otetezedwa pa dziko lonse.